Davide ayamika Mulungu pa kugonjetsa adani
Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.
1 Yehova, adzasekera mfumu mu mphamvu yanu;
adzakondwera kwakukulu m’chipulumutso chanu!
2 Mwampatsa iye chikhumbo cha mtima wake,
ndipo simunakane pempho la milomo yake.
3 Pakuti mufika kwa iye ndi madalitso okoma;
muika korona wa golide woyengetsa pamutu pake.
4 Anakupemphani moyo, mwampatsa iye;
mwamtalikitsira masiku kunthawi za nthawi.
5 Ulemerero wake ngwaukulu mwa chipulumutso chanu;
mumchitira iye ulemu ndi ukulu.
6 Pakuti mumuikira madalitso kunthawi zonse;
mumkondweretsa ndi chimwemwe pankhope panu.
7 Pakuti mfumu akhulupirira Yehova,
ndipo mwa chifundo cha Wam’mwambamwamba sadzagwedezeka iye.
8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse,
dzanja lanu lamanja lidzapeza iwo akuda Inu.
9 Mudzawaika ngati ng’anjo yamoto pa nyengo ya mkwiyo wanu.
Yehova adzawatha m’kukwiya kwake,
ndipo moto udzawanyeketsa.
10 Mudzaziononga zobala zao kuzichotsa padziko lapansi,
ndi mbeu zao mwa ana a anthu.
11 Pakuti anakupangirani choipa,
anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.
12 Pakuti mudzawabweza m’mbuyo,
popiringidza m’nsinga zanu pankhope pao.
13 Kwezekani, Yehova, mu mphamvu yanu;
potero tidzaimba ndi kulemekeza chilimbiko chanu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/21-3b1823598324ec263045853364f077b7.mp3?version_id=1068—