Categories
MASALIMO

MASALIMO 19

Davide alemekeza zolengedwa ndi Mulungu, ndi malamulo ao omwe

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide.

1 Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu;

ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.

2 Usana ndi usana uchulukitsa mau,

ndipo usiku ndi usiku uonetsa nzeru.

3 Palibe chilankhulidwe, palibe mau;

liu lao silimveka.

4 Muyeso wao wapitirira padziko lonse lapansi,

ndipo mau ao ku malekezero a m’dziko muli anthu.

Iye anaika hema la dzuwa m’menemo,

5 ndipo lili ngati mkwati wakutuluka m’chipinda mwake,

likondwera ngati chiphona kuthamanga m’njira.

6 Kutuluka kwake lituluka kolekezera thambo,

ndipo kuzungulira kwake lifikira ku malekezero ake;

ndipo kulibe kanthu kobisalira kutentha kwake.

7 Malamulo a Yehova ali angwiro, akubwezera moyo;

mboni za Yehova zili zokhazikika, zakuwapatsa opusa nzeru.

8 Malangizo a Yehova ali olungama, akukondweretsa mtima;

malamulo a Yehova ali oyera, akupenyetsa maso.

9 Kuopa Yehova kuli mbee, kwakukhalabe nthawi zonse;

maweruzo a Yehova ali oona, alungama konsekonse.

10 Ndizo zifunika koposa golide,

inde, golide wambiri woyengetsa;

zizuna koposa uchi ndi zakukha za zisa zake.

11 Ndiponso kapolo wanu achenjezedwa nazo,

m’kuzisunga izo muli mphotho yaikulu.

12 Adziwitsa zolowereza zake ndani?

Mundimasule kwa zolakwa zobisika.

13 Ndiponso muletse kapolo wanu pa zodzitama;

zisachite ufumu pa ine.

Pamenepo ndidzakhala wangwiro,

ndi wosachimwa cholakwa chachikulu.

14 Mau a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga

avomerezeke pamaso panu,

Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/19-dbb1b75cff85c5c4a164cc3805ea20cf.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *