Categories
MASALIMO

MASALIMO 18

Nyimbo yoyamikira Yehova ya Davide

Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova, amene ananena kwa Yehova mau a nyimbo iyi m’mene Yehova anamlanditsa m’dzanja la adani ake onse, ndi m’dzanja la Saulo: ndipo anati,

1 Ndikukondani, Yehova, mphamvu yanga.

2 Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa,

ndi Mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye;

chikopa changa, nyanga ya chipulumutso changa, msanje wanga.

3 Ndidzaitanira Yehova, woyenera kutamandika,

ndipo adzandipulumutsa ine kwa adani anga.

4 Zingwe za imfa zinandizinga,

ndipo mitsinje ya zopanda pake inandiopsa.

5 Zingwe za manda zindizinga,

misampha ya imfa inandifikira ine.

6 M’kusauka kwanga ndinaitana Yehova,

ndipo ndinakuwira Mulungu wanga;

mau anga anawamva mu Kachisi mwake,

ndipo mkuwo wanga wa pankhope pake unalowa m’makutu mwake.

7 Pamenepo linagwedezeka, ndi kutenthemera dziko lapansi,

ndi maziko a mapiri ananjenjemera

nagwedezeka, pakuti anakwiya Iyeyo.

8 Unakwera utsi wotuluka m’mphuno mwake,

ndi moto wa m’kamwa mwake unanyeka

nuyakitsa makala.

9 Ndipo Iye anaweramitsa thambo, natsika;

ndipo pansi pa mapazi ake panali mdima bii.

10 Ndipo anaberekeka pakerubi, nauluka;

nauluka msanga pa mapiko a mphepo.

11 Anaika mdima pobisala pake, hema wake womzinga;

mdima wa madzi, makongwa a kuthambo.

12 Mwa kuchezemira kunali pamaso pake makongwa anakanganuka,

matalala ndi makala amoto.

13 Ndipo anagunda m’mwamba Yehova,

ndipo Wam’mwambamwamba anamvetsa liu lake;

matalala ndi makala amoto.

14 Ndipo anatuma mivi yake nawabalalitsa;

inde mphezi zaunyinji, nawamwaza.

15 Ndipo zidaoneka zoyendamo madzi,

nafukuka maziko a dziko lapansi,

mwa kudzudzula kwanu, Yehova,

mwa mpumo wa mpweya wa m’mphuno mwanu.

16 Anatuma kuchokera m’mwamba, ananditenga;

anandivuula m’madzi ambiri.

17 Anandipulumutsa ine kwa mdani wanga wamphamvu,

ndi kwa iwo ondida ine, pakuti anandiposa mphamvu.

18 Anandipeza ine tsiku la tsoka langa;

koma Yehova anali mchirikizo wanga.

19 Ananditulutsanso andifikitse motakasuka;

anandilanditsa, pakuti anakondwera ndi ine.

20 Yehova anandibwezera monga mwa chilungamo changa;

anandisudzula monga mwa kusisira kwa manja anga.

21 Pakuti ndasunga njira za Yehova,

ndipo sindinachitire choipa kusiyana ndi Mulungu wanga.

22 Pakuti maweruzo ake onse anali pamaso panga,

ndipo malemba ake sindinawachotse kwa ine.

23 Ndipo ndinakhala wangwiro ndi Iye,

ndipo ndinadzisunga wosachita choipa changa.

24 Ndimo anandisudzulira Yehova monga mwa chilungamo changa,

monga mwa kusisira kwa manja anga pamaso pake.

25 Pa wachifundo mukhala wachifundo;

pa munthu wangwiro mukhala wangwiro.

26 Pa woyera mtima mukhala woyera mtima;

pa wotsutsatsutsa mukhala wotsutsana naye.

27 Pakuti Inu muwapulumutsa anthu aumphawi;

koma maso okweza muwatsitsa.

28 Pakuti Inu muyatsa nyali yanga;

Yehova, Mulungu wanga, aunikira mdima wanga.

29 Pakuti mwa Inu ndipyola khamu la anthu;

ndipo mwa Mulungu wanga ndilumphira linga.

30 Mulungu ndiye wangwiro m’njira zake;

mau a Yehova ngoyengeka;

ndiye chikopa cha onse okhulupirira Iye.

31 Pakuti Mulungu ndani wosati Yehova?

Ndipo thanthwe ndani wosati Mulungu wathu?

32 Mulungu ndiye wondizingiza mphamvu m’chuuno,

nakonza njira yanga ikhale yangwiro.

33 Alinganiza mapazi anga ngati a mbawala,

nandiimitsa pamsanje panga.

34 Aphunzitsa manja anga agwire nkhondo;

kuti walifuka uta wamkuwa ndi manja anga.

35 Ndipo mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu;

ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza,

ndipo chifatso chanu chandikuza ine.

36 Mwandipondetsa patalipatali,

sanaterereke mapazi anga.

37 Ndidzalondola adani anga, ndi kuwapeza,

ndipo sindidzabwerera asanathe psiti.

38 Ndidzawapyoza kuti sangakhoze kuuka,

adzagwa pansi pa mapazi anga.

39 Pakuti mwandizingiza mphamvu m’chuuno ku nkhondoyo;

mwandigonjetsera amene andiukira.

40 Ndipo adani anga mwawalozetsa m’mbuyo kwa ine,

kuti ndipasule ondidawo.

41 Anafuula, koma panalibe wopulumutsa;

ngakhale kwa Yehova, koma sanawavomereze.

42 Pamenepo ndinawapera ngati fumbi la kumphepo;

ndinawakhuthula ngati matope a pabwalo.

43 Mwandipulumutsa pa zolimbana nane za anthu;

mwandiika mutu waamitundu;

mtundu wa anthu sindinaudziwe udzanditumikira.

44 Pakumva m’khutu za ine adzandimvera,

alendo adzandigonjera monyenga.

45 Alendo adzafota,

nadzatuluka monjenjemera m’ngaka mwao.

46 Yehova ngwa moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;

nakwezeke Mulungu wa chipulumutso changa.

47 Ndiye Mulungu amene andibwezerera chilango,

nandigonjetsera mitundu ya anthu.

48 Andipulumutsa kwa adani anga.

Inde mundikweza pa iwo akundiukira ine,

mundikwatula kwa munthu wachiwawa.

49 Chifukwa chake Yehova ndidzakuyamikani mwa amitundu,

ndipo dzina lanu ndidzaliimbira.

50 Alanditsa mfumu yake ndi chipulumutso chachikulu;

nachitira chifundo wodzozedwa wake,

Davide, ndi mbumba yake, kunthawi zonse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/18-941b51d1b23796a989b54e0b72f4dd8b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *