Davide apempha Mulungu amsunge pa ofuna kumuononga
Pemphero la Davide.
1 Yehova, imvani chilungamo, mverani mfuu wanga;
tcherani khutu ku pemphero langa
losatuluka m’milomo ya chinyengo.
2 Pankhope panu patuluke chiweruzo changa;
maso anu apenyerere zolunjika.
3 Mwayesera mtima wanga; mwandizonda usiku;
mwandisuntha, simupeza kanthu;
mwatsimikiza mtima kuti m’kamwa mwanga simudzalakwa.
4 Za machitidwe a anthu, ndachenjera ndi mau a milomo yanu
ndingalowe njira za woononga.
5 M’mayendedwe anga ndasunga mabande anu,
mapazi anga sanaterereke.
6 Ine ndinakuitanani, pakuti mudzandiyankha, Mulungu;
tcherani khutu lanu kwa ine, imvani mau anga.
7 Onetsani chifundo chanu chodabwitsa,
Inu wakupulumutsa okhulupirira Inu
kwa iwo akuwaukira ndi dzanja lanu lamanja.
8 Ndisungeni monga kamwana ka m’diso,
ndifungatireni mu mthunzi wa mapiko anu,
9 kundilanditsa kwa oipa amene andipasula,
adani a pa moyo wanga amene andizinga.
10 Mafuta ao awatsekereza;
m’kamwa mwao alankhula modzikuza.
11 Tsopano anatizinga m’mayendedwe athu,
apenyetsetsa m’maso kuti atigwetse pansi.
12 Afanana ndi mkango wofuna kumwetula,
ndi msona wa mkango wakukhala mobisalamo.
13 Ukani Yehova, Mumtsekereze, mumgwetse,
landitsani moyo wanga kwa woipa ndi lupanga lanu;
14 kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova,
kwa anthu a dziko lapansi pano
amene cholowa chao chili m’moyo uno,
ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika;
akhuta mtima ndi ana,
nasiyira ana amakanda zochuluka zao.
15 Koma ine ndidzapenyerera nkhope yanu m’chilungamo,
ndidzakhuta mtima ndi maonekedwe anu, pamene ndidzauka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/17-9d8ddf7ef741f74133cbdf9abe033de3.mp3?version_id=1068—