Zolengedwa zonse zilemekeze Mulungu
1 Aleluya.
Lemekezani Yehova kochokera kumwamba;
mlemekezeni m’misanje.
2 Mlemekezeni,angeloake onse;
mlemekezeni, makamu ake onse.
3 Mlemekezeni, dzuwa ndi mwezi;
mlemekezeni, nyenyezi zonse zounikira.
4 Mlemekezeni, m’mwambamwamba,
ndi madzi inu, a pamwamba pa thambo.
5 Alemekeze dzina la Yehova;
popeza analamulira, ndipo zinalengedwa.
6 Anazikhazikanso kunthawi za nthawi;
anazipatsa chilamulo chosatumphika.
7 Lemekezani Yehova kochokera ku dziko lapansi,
zinsomba inu, ndi malo ozama onse;
8 moto ndi matalala, chipale chofewa ndi nkhungu;
mphepo ya namondwe, yakuchita mau ake;
9 mapiri ndi zitunda zonse;
mitengo yazipatso ndi yamikungudza yonse:
10 Nyama zakuthengo ndi zoweta zonse;
zokwawa, ndi mbalame zakuuluka.
11 Mafumu a padziko ndi mitundu yonse ya anthu;
zinduna ndi oweruza onse a padziko.
12 Anyamata ndiponso anamwali;
okalamba pamodzi ndi ana.
13 Alemekeze dzina la Yehova;
pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka;
ulemerero wake uli pamwamba padziko lapansi ndi thambo.
14 Ndipo anakweza nyanga ya anthu ake,
chilemekezo cha okondedwa ake onse;
ndiwo ana a Israele, anthu a pafupi pa Iye.
Aleluya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/148-c66f417a2811e794129a4da622dd16f6.mp3?version_id=1068—