Categories
MASALIMO

MASALIMO 145

Ukulu ndi ukoma wa Mulungu

Salimo lolemekeza; la Davide.

1 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu;

ndipo ndidzalemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

2 Masiku onse ndidzakuyamikani;

ndi kulemekeza dzina lanu kunthawi za nthawi.

3 Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu;

ndi ukulu wake ngwosasanthulika.

4 Mbadwo wina udzalemekezera ntchito zanu mbadwo unzake,

ndipo udzalalikira zamphamvu zanu.

5 Ndidzalingalira ulemerero waukulu wa ulemu wanu,

ndi ntchito zanu zodabwitsa.

6 Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa;

ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.

7 Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu,

nadzaimbira chilungamo chanu.

8 Yehova ndiye wachisomo, ndi wachifundo;

osakwiya msanga, ndi wa chifundo chachikulu.

9 Yehova achitira chokoma onse;

ndi nsoni zokoma zake zigwera ntchito zake zonse.

10 Ntchito zanu zonse zidzakuyamikani, Yehova;

ndi okondedwa anu adzakulemekezani.

11 Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu,

adzalankhulira mphamvu yanu.

12 Kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake,

ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.

13 Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya,

ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.

14 Yehova agwiriziza onse akugwa,

naongoletsa onse owerama.

15 Maso a onse ayembekeza Inu;

ndipo muwapatsa chakudya chao m’nyengo zao.

16 Muolowetsa dzanja lanu,

nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.

17 Yehova ali wolungama m’njira zake zonse,

ndi wachifundo m’ntchito zake zonse.

18 Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye,

onse akuitanira kwa Iye m’choonadi.

19 Adzachita chokhumba iwo akumuopa;

nadzamva kufuula kwao, nadzawapulumutsa.

20 Yehova asunga onse akukondana naye;

koma oipa onse adzawaononga.

21 Pakamwa panga padzanena chilemekezo cha Yehova;

ndi zinthu zonse zilemekeze dzina lake loyera

kunthawi za nthawi.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/145-1717429a59961e0a42ee09b207785c43.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *