Categories
MASALIMO

MASALIMO 143

Davide apempha Mulungu amlanditse msanga kwa adani ake

Salimo la Davide.

1 Imvani pemphero langa, Yehova; nditcherere khutu kupemba kwanga;

ndiyankheni mwa chikhulupiriko chanu, mwa chilungamo chanu.

2 Ndipo musaitane mlandu wa mtumiki wanu;

pakuti pamaso panu sipadzakhala wolungama wamoyo mmodzi yense.

3 Pakuti mdani alondola moyo wanga;

apondereza pansi moyo wanga;

andikhalitsa mumdima monga iwo adafa kale lomwe.

4 Potero mzimu wanga wakomoka mwa ine;

mtima wanga utenga nkhawa m’kati mwanga.

5 Ndikumbukira masiku a kale lomwe;

zija mudazichita ndilingirirapo;

ndikamba pandekha za ntchito ya manja anu.

6 Nditambalitsira manja anga kwa Inu:

Moyo wanga ulira Inu monga dziko lolira mvula.

7 Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha.

Musandibisire nkhope yanu;

ndingafanane nao akutsikira kudzenje.

8 Mundimvetse chifundo chanu mamawa;

popeza ndikhulupirira Inu:

Mundidziwitse njira ndiyendemo;

popeza ndikweza moyo wanga kwa Inu.

9 Mundilanditse kwa adani anga, Yehova;

ndibisala mwa Inu.

10 Mundiphunzitse chokonda Inu; popeza Inu ndinu Mulungu wanga;

Mzimu wanu ndi wokoma; munditsogolere kuchidikha.

11 Mundipatse moyo, Yehova, chifukwa cha dzina lanu;

mwa chilungamo chanu mutulutse moyo wanga m’sautso.

12 Ndipo mwa chifundo chanu mundidulire adani anga,

ndipo muononge onse akusautsa moyo wanga;

pakuti ine ndine mtumiki wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/143-c4534d5452662442eac4ab35bfdad210.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *