Categories
MASALIMO

MASALIMO 140

Davide apempha Mulungu amlanditse kwa mdani woipa wamphamvu

Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la Davide.

1 Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa;

ndisungeni kwa munthu wachiwawa;

2 amene adzipanga zoipa mumtima mwao;

masiku onse amemeza nkhondo.

3 Anola lilime lao ngati njoka;

pansi pa milomo yao pali ululu wa mphiri.

4 Ndilindireni Yehova, ndisalowe m’manja mwa woipa;

ndisungeni kwa munthu wachiwawa;

kwa iwo akuti akankhe mapazi anga.

5 Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe;

anatcha ukonde m’mphepete mwa njira;

ananditchera makwekwe.

6 Ndinati kwa Yehova, Inu ndinu Mulungu wanga;

munditcherere khutu mau a kupemba kwanga, Yehova.

7 Yehova Ambuye, ndinu mphamvu ya chipulumutso changa,

munandiphimba mutu wanga tsiku lakulimbana nkhondo.

8 Yehova, musampatse woipa zokhumba iye;

musamthandize zodzipanga zake; angadzikuze.

9 Kunena za mutu wao wa iwo akundizinga,

choipa cha milomo yao chiwaphimbe.

10 Makala amoto awagwere;

aponyedwe kumoto;

m’maenje ozama, kuti asaukenso.

11 Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi;

choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse.

12 Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu,

ndi kuweruzira aumphawi.

13 Indedi, olungama adzayamika dzina lanu;

oongoka mtima adzakhala pamaso panu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/140-f00ee044309bcb1491e964d9efe48d2e.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *