Apempha Mulungu amlanditse pa omnamiza
Nyimbo yokwerera.
1 Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga,
ndipo anandivomereza.
2 Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza,
ndi kulilime lonyenga.
3 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji,
lilime lonyenga iwe?
4 Mivi yakuthwa ya chiphona,
ndi makala tsanya.
5 Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki,
kuti ndigonera m’mahema a Kedara!
6 Moyo wanga unakhalitsa nthawi
pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere.
7 Ine ndikuti, Mtendere;
koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/120-9446c9b8452065a4e6d585a5fdd35301.mp3?version_id=1068—