Categories
MASALIMO

MASALIMO 119

Chilamulo cha Mulungu ndi chokometsetsa. Adalitsidwa akuchisunga

1 Odala angwiro m’mayendedwe ao,

akuyenda m’chilamulo cha Yehova.

2 Odala iwo akusunga mboni zake,

akumfuna ndi mtima wonse;

3 inde, sachita chosalungama;

ayenda m’njira zake.

4 Inu munatilamulira,

tisamalire malangizo anu ndi changu.

5 Ha? Mwenzi zitakhazikika njira zanga

kuti ndisamalire malemba anu.

6 Pamenepo sindidzachita manyazi,

pakupenyerera malamulo anu onse.

7 Ndidzakuyamikani ndi mtima woongoka,

pakuphunzira maweruzo anu olungama.

8 Ndidzasamalira malemba anu:

Musandisiye ndithu.

9 Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?

Akawasamalira monga mwa mau anu.

10 Ndinakufunani ndi mtima wanga wonse;

ndisasokere kusiyana nao malamulo anu.

11 Ndinawabisa mau anu mumtima mwanga,

kuti ndisalakwire Inu.

12 Inu ndinu wodala Yehova;

ndiphunzitseni malemba anu.

13 Ndinafotokozera ndi milomo yanga

maweruzo onse a pakamwa panu.

14 Ndinakondwera m’njira ya mboni zanu,

koposa ndi chuma chonse.

15 Ndidzalingirira pa malangizo anu,

ndi kupenyerera mayendedwe anu.

16 Ndidzadzikondweretsa nao malemba anu;

sindidzaiwala mau anu.

17 Muchitire chokoma mtumiki wanu kuti ndikhale ndi moyo;

ndipo ndidzasamalira mau anu.

18 Munditsegulire maso, kuti ndipenye

zodabwitsa za m’chilamulo chanu.

19 Ine ndine mlendo padziko lapansi;

musandibisire malamulo anu.

20 Mtima wanga wasweka ndi kukhumba

maweruzo anu nyengo zonse.

21 Munadzudzula odzikuza otembereredwa,

iwo akusokera kusiyana nao malamulo anu.

22 Mundichotsere chotonza, ndi chimpepulo;

pakuti ndinasunga mboni zanu.

23 Nduna zomwe zinakhala zondineneza;

koma mtumiki wanu analingirira malemba anu.

24 Mboni zanu zomwe ndizo zondikondweretsa,

ndizo zondipangira nzeru.

25 Moyo wanga umamatika ndi fumbi;

mundipatse moyo monga mwa mau anu.

26 Ndinafotokozera njira zanga, ndipo munandiyankha:

Mundiphunzitse malemba anu.

27 Mundizindikiritse njira ya malangizo anu;

kuti ndilingalire zodabwitsa zanu.

28 Moyo wanga wasungunuka ndi chisoni:

Mundilimbitse monga mwa mau anu.

29 Mundichotsere njira ya chinyengo;

nimundipatse mwachifundo chilamulo chanu.

30 Ndinasankha njira yokhulupirika;

ndinaika maweruzo anu pamaso panga.

31 Ndimamatika nazo mboni zanu;

musandichititse manyazi, Yehova.

32 Ndidzathamangira njira ya malamulo anu,

mutakulitsa mtima wanga.

33 Mundiphunzitse, Yehova, njira ya malemba anu;

ndidzaisunga kufikira kutha kwake.

34 Mundizindikiritse, ndipo ndidzasunga malamulo anu;

ndidzawasamalira ndi mtima wanga wonse.

35 Mundiyendetse mopita malamulo anu;

pakuti ndikondwera m’menemo.

36 Lingitsani mtima wanga kumboni zanu,

si ku chisiriro ai.

37 Muchititse mlubza maso anga ndisapenye zachabe,

mundipatse moyo mu njira yanu.

38 Limbitsirani mtumiki wanu mau anu,

ndiye wodzipereka kukuopani.

39 Mundipatutsire chotonza changa ndichiopacho;

popeza maweruzo anu ndi okoma.

40 Taonani, ndinalira malangizo anu;

mundipatse moyo mwa chilungamo chanu.

41 Ndipo chifundo chanu chindidzere, Yehova,

ndi chipulumutso chanu, monga mwa mau anu.

42 Kuti ndikhale nao mau akuyankha wonditonza;

popeza ndikhulupirira mau anu.

43 Ndipo musandichotsere ndithu mau a choonadi pakamwa panga;

pakuti ndinayembekeza maweruzo anu.

44 Potero ndidzasamalira malamulo anu chisamalire

kunthawi za nthawi.

45 Ndipo ndidzayenda mwaufulu;

popeza ndinafuna malangizo anu.

46 Ndidzalankhulanso za umboni wanu pamaso pa mafumu,

osachitapo manyazi.

47 Ndipo ndidzadzikondweretsa nao malamulo anu,

amene ndiwakonda.

48 Ndidzakwezanso manja anga ku malamulo anu, amene ndiwakonda;

ndipo ndidzalingalira pa malemba anu.

49 Kumbukirani mau a kwa mtumiki wanu,

amene munandiyembekezetsa nao.

50 Chitonthozo changa m’kuzunzika kwanga ndi ichi;

pakuti mau anu anandipatsa moyo.

51 Odzikuza anandinyoza kwambiri:

koma sindinapatukanso nacho chilamulo chanu.

52 Ndinakumbukira maweruzo anu kuyambira kale, Yehova,

ndipo ndinadzitonthoza.

53 Ndinasumwa kwakukulu,

chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.

54 Malemba anu anakhala nyimbo zanga

m’nyumba ya ulendo wanga.

55 Usiku ndinakumbukira dzina lanu, Yehova,

ndipo ndinasamalira chilamulo chanu.

56 Ichi ndinali nacho,

popeza ndinasunga malangizo anu.

57 Yehova ndiye gawo langa:

Ndinati ndidzasunga mau anu.

58 Ndinapemba pankhope panu ndi mtima wanga wonse:

Mundichitire chifundo monga mwa mau anu.

59 Ndinaganizira njira zanga,

ndipo ndinabweza mapazi anga atsate mboni zanu.

60 Ndinafulumira, osachedwa,

kusamalira malamulo anu.

61 Anandikulunga nazo zingwe za oipa;

koma sindinaiwale chilamulo chanu.

62 Pakati pa usiku ndidzauka kukuyamikani

chifukwa cha maweruzo anu olungama.

63 Ine ndine wakuyanjana nao onse akukuopani,

ndi iwo akusamalira malangizo anu.

64 Dziko lapansi lidzala nacho chifundo chanu, Yehova;

mundiphunzitse malemba anu.

65 Munachitira mtumiki wanu chokoma, Yehova,

monga mwa mau anu.

66 Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru;

pakuti ndinakhulupirira malamulo anu.

67 Ndisanazunzidwe ndinasokera;

koma tsopano ndisamalira mau anu.

68 Inu ndinu wabwino, ndi wakuchita zabwino;

mundiphunzitse malemba anu.

69 Odzikuza anandipangira bodza:

Ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.

70 Mtima wao unona ngati mafuta;

koma ine ndikondwera nacho chilamulo chanu.

71 Kundikomera kuti ndinazunzidwa;

kuti ndiphunzire malemba anu.

72 Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera

koposa golide ndisilivazikwizikwi.

73 Manja anu anandilenga nandiumba;

mundizindikiritse, kuti ndiphunzire malemba anu.

74 Iwo amene akuopani adzandiona ine nadzakondwera;

popeza ndayembekezera mau anu.

75 Ndidziwa kuti maweruzo anu ndiwo olungama, Yehova,

ndi kuti munandizunza ine mokhulupirika.

76 Chifundo chanu chikhaletu chakunditonthoza, ndikupemphani,

monga mwa mau anu kwa mtumiki wanu.

77 Nsoni zokoma zanu zindidzere, kuti ndikhale ndi moyo;

popeza chilamulo chanu chindikondweretsa.

78 Odzikuza achite manyazi, popeza anandichitira monyenga ndi bodza:

Koma ine ndidzalingalira malangizo anu.

79 Iwo akuopa Inu abwere kwa ine,

ndipo adzadziwa mboni zanu.

80 Mtima wanga ukhale wangwiro m’malemba anu;

kuti ndisachite manyazi.

81 Moyo wanga unakomoka ndi kukhumba chipulumutso chanu:

Ndinayembekezera mau anu.

82 Maso anga anatha mphamvu ndi kukhumba mau anu,

ndikuti, Mudzanditonthoza liti?

83 Popeza ndakhala ngati thumba lofukirira;

koma sindiiwala malemba anu.

84 Masiku a mtumiki wanu ndiwo angati?

Mudzaweruza liti iwo akundilondola koipa?

85 Odzikuza anandikumbira mbuna,

ndiwo osasamalira chilamulo chanu.

86 Malamulo anu onse ngokhulupirika;

andilondola nalo bodza; ndithandizeni.

87 Akadandithera padziko lapansi;

koma ine sindinasiye malangizo anu.

88 Mundipatse moyo monga mwa chifundo chanu;

ndipo ndidzasamalira mboni ya pakamwa panu.

89 Mau anu aikika kumwamba,

kosatha, Yehova.

90 Chikhulupiriko chanu chifikira mibadwomibadwo;

munakhazikitsa dziko lapansi, ndipo likhalitsa.

91 Kunena za maweruzo anu alimbikira kufikira lero;

pakuti onsewa ndiwo atumiki anu.

92 Chilamulo chanu chikadapanda kukhala chikondweretso changa,

ndikadatayika m’kuzunzika kwanga.

93 Sindidzaiwala malangizo anu nthawi zonse;

popeza munandipatsa nao moyo.

94 Ine ndine wanu, ndipulumutseni

pakuti ndinafuna malangizo anu.

95 Oipa anandilalira kundiononga;

koma ndizindikira mboni zanu.

96 Ndinapenya malekezero ake a ungwiro wonse;

koma lamulo lanu ndi lotakasuka ndithu.

97 Ha! Ndikondadi chilamulo chanu;

ndilingiriramo ine tsiku lonse.

98 Malamulo anu andipatsa nzeru yakuposa adani anga;

pakuti akhala nane chikhalire.

99 Ndili nayo nzeru yakuposa aphunzitsi anga onse;

pakuti ndilingalira mboni zanu.

100 Ndizindikira koposa okalamba

popeza ndinasunga malangizo anu.

101 Ndinaletsa mapazi anga njira iliyonse yaoipa,

kuti ndisamalire mau anu.

102 Sindinapatukane nao maweruzo anu;

pakuti Inu munandiphunzitsa.

103 Mau anu azunadi powalawa ine!

Koposa uchi m’kamwa mwanga.

104 Malangizo anu andizindikiritsa;

chifukwa chake ndidana nao mayendedwe onse achinyengo.

105 Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga,

ndi kuunika kwa panjira panga.

106 Ndinalumbira, ndipo ndinatsimikiza mtima,

kuti ndidzasamalira maweruzo anu olungama.

107 Ndazunzika kwambiri:

Ndipatseni moyo, Yehova, monga mwa mau anu.

108 Landirani, Yehova, zopereka zaufulu za pakamwa panga,

ndipo ndiphunzitseni maweruzo anu.

109 Moyo wanga ukhala m’dzanja langa chikhalire;

koma sindiiwala chilamulo chanu.

110 Oipa ananditchera msampha;

koma sindinasokere m’malangizo anu.

111 Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha;

pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.

112 Ndinalingitsa mtima wanga uchite malemba anu,

kosatha, kufikira chimaliziro.

113 Ndidana nao a mitima iwiri;

koma ndikonda chilamulo chanu.

114 Inu ndinu pobisalapo panga, ndi chikopa changa;

ndiyembekezera mau anu.

115 Mundichokere ochita zoipa inu;

kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.

116 Mundichirikize monga mwa mau anu, kuti ndikhale ndi moyo;

ndipo ndisachite manyazi pa chiyembekezo changa.

117 Mundigwirizize ndipo ndidzapulumutsidwa,

ndipo ndidzasamalira malemba anu chisamalire.

118 Mupepula onse akusokera m’malemba anu;

popeza chinyengo chao ndi bodza.

119 Muchotsa oipa onse a padziko lapansi ngati mphala:

Chifukwa chake ndikonda mboni zanu.

120 Thupi langa linjenjemera ndi kuopa Inu;

ndipo ndichita mantha nao maweruzo anu.

121 Ndinachita chiweruzo ndi chilungamo;

musandisiyira akundisautsa.

122 Mumkhalire chikole mtumiki wanu chimkomere;

odzikuza asandisautse.

123 Maso anga anatha mphamvu pofuna chipulumutso chanu,

ndi mau a chilungamo chanu.

124 Muchitire mtumiki wanu monga mwa chifundo chanu,

ndipo ndiphunzitseni malemba anu.

125 Ine ndine mtumiki wanu, ndizindikiritseni;

kuti ndidziwe mboni zanu.

126 Yafika nyengo yakuti Yehova achite kanthu;

pakuti anaswa chilamulo chanu.

127 Chifukwa chake ndikonda malamulo anu

koposa golide, inde golide woyengeka.

128 Chifukwa chake ndiyesa ngolunjika

malangizo anu onse akunena zonse;

koma ndidana nazo njira zonse zonyenga.

129 Mboni zanu nzodabwitsa;

chifukwa chake moyo wanga uzisunga.

130 Potsegulira mau anu paunikira;

kuzindikiritsa opusa.

131 Ndinatsegula pakamwa panga, ndi kupuma wefuwefu;

popeza ndinakhumba malamulo anu.

132 Munditembenukire, ndi kundichitira chifundo,

monga mumatero nao akukonda dzina lanu.

133 Khazikitsani mapazi anga m’mau anu;

ndipo zisandigonjetse zopanda pake zilizonse.

134 Mundiombole kunsautso ya munthu:

Ndipo ndidzasamalira malangizo anu.

135 Muwalitse nkhope yanu pa mtumiki wanu;

ndipo mundiphunzitse malemba anu.

136 Maso anga atsitsa mitsinje ya madzi,

popeza sasamalira chilamulo chanu.

137 Inu ndinu wolungama, Yehova,

ndipo maweruzo anu ndiwo olunjika.

138 Mboni zanuzo mudazilamulira

zili zolungama ndi zokhulupirika ndithu.

139 Changu changa chinandithera,

popeza akundisautsa anaiwala mau anu.

140 Mau anu ngoyera ndithu;

ndi mtumiki wanu awakonda.

141 Wamng’ono ine, ndi wopepulidwa;

koma sindiiwala malemba anu.

142 Chilungamo chanu ndicho chilungamo chosatha;

ndi chilamulo chanu ndicho choonadi.

143 Kusautsika ndi kupsinjika kwandigwera;

koma malamulo anu ndiwo ondikondweretsa ine.

144 Mboni zanu ndizo zolungama kosatha;

mundizindikiritse izi, ndipo ndidzakhala ndi moyo.

145 Ndinaitana ndi mtima wanga wonse; mundiyankhe, Yehova;

ndidzasunga malemba anu.

146 Ndinaitanira Inu; ndipulumutseni,

ndipo ndidzasamalira mboni zanu.

147 Ndinafuula kusanake:

ndinayembekezera mau anu.

148 Maso anga anakumana ndi maulonda a usiku,

kuti ndilingirire mau anu.

149 Imvani liu langa monga mwa chifundo chanu;

mundipatse moyo monga mwa kuweruza kwanu, Yehova.

150 Otsata zachiwembu andiyandikira;

akhala kutali ndi chilamulo chanu.

151 Inu muli pafupi, Yehova;

ndipo malamulo anu onse ndiwo choonadi.

152 Kuyambira kale ndinadziwa mu mboni zanu,

kuti munazikhazika kosatha.

153 Penyani kuzunzika kwanga, nimundilanditse;

pakuti sindiiwala chilamulo chanu.

154 Mundinenere mlandu wanga, nimundiombole;

mundipatse moyo monga mwa mau anu.

155 Chipulumutso chitalikira oipa;

popeza safuna malemba anu.

156 Zachifundo zanu ndi zazikulu, Yehova;

mundipatse moyo monga mwa maweruzo anu.

157 Ondilondola ndi ondisautsa ndiwo ambiri;

koma sindinapatukane nazo mboni zanu.

158 Ndinapenya ochita monyenga, ndipo ndinanyansidwa nao;

popeza sasamalira mau anu.

159 Penyani kuti ndikonda malangizo anu;

mundipatse moyo, Yehova, monga mwa chifundo chanu.

160 Chiwerengero cha mau anu ndicho choonadi;

ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.

161 Nduna zinandilondola kopanda chifukwa;

koma mtima wanga uchita nao mantha mau anu.

162 Ndikondwera nao mau anu,

ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.

163 Ndidana nalo bodza ndi kunyansidwa nalo;

koma ndikonda chilamulo chanu.

164 Ndikulemekezani kasanu ndi kawiri, tsiku limodzi,

chifukwa cha maweruzo anu olungama.

165 Akukonda chilamulo chanu ali nao mtendere wambiri;

ndipo alibe chokhumudwitsa.

166 Ndinayembekeza chipulumutso chanu, Yehova,

ndipo ndinachita malamulo anu.

167 Moyo wanga unasamalira mboni zanu;

ndipo ndizikonda kwambiri.

168 Ndinasamalira malangizo anu ndi mboni zanu;

popeza njira zanga zonse zili pamaso panu.

169 Kufuula kwanga kuyandikire pamaso panu, Yehova;

mundizindikiritse monga mwa mau anu.

170 Kupemba kwanga kudze pamaso panu;

mundilanditse monga mwa mau anu.

171 Milomo yanga itulutse chilemekezo;

popeza mundiphunzitsa malemba anu.

172 Lilime langa liimbire mau anu;

pakuti malamulo anu onse ndiwo olungama.

173 Dzanja lanu likhale lakundithandiza;

popeza ndinasankha malangizo anu.

174 Ndinakhumba chipulumutso chanu, Yehova;

ndipo chilamulo chanu ndicho chondikondweretsa.

175 Mzimu wanga ukhale ndi moyo, ndipo udzakulemekezani;

ndipo maweruzo anu andithandize.

176 Ndinasochera ngati nkhosa yotayika; funani mtumiki wanu;

pakuti sindiiwala malamulo anu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/119-58c604d3573d228e8e4d87bb21504897.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *