Categories
MASALIMO

MASALIMO 118

Wa Salimo alemekeza Mulungu womlanditsa m’manja mwa adani

1 Yamikani Yehova; pakuti Iye ndiye wabwino;

pakuti chifundo chake nchosatha.

2 Anene tsono Israele,

kuti chifundo chake nchosatha.

3 Anene tsono nyumba ya Aroni,

kuti chifundo chake nchosatha.

4 Anene tsono iwo akuopa Yehova,

kuti chifundo chake nchosatha.

5 M’mene ndinasautsika ndinaitanira pa Yehova;

anandiyankha nandiika motakasuka Yehova.

6 Yehova ndi wanga; sindidzaopa;

adzandichitanji munthu?

7 Yehova ndi wanga, mwa iwo akundithandiza;

m’mwemo ndidzaona chofuna ine pa iwo akundida.

8 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

koposa kukhulupirira munthu.

9 Kuthawira kwa Yehova nkokoma

koposa kukhulupirira akulu.

10 Amitunduonse adandizinga,

zedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

11 Adandizinga, inde, adandizinga:

Indedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

12 Adandizinga ngati njuchi;

anazima ngati moto waminga;

indedi, m’dzina la Yehova ndidzawaduladula.

13 Kundikankha anandikankha ndikadagwa;

koma Yehova anandithandiza.

14 Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;

ndipo anakhala chipulumutso changa.

15 M’mahema a olungama muli liu lakufuula mokondwera

Dzanja lamanja la Yehova ndi la chipulumutso:

16 Dzanja lamanja la Yehova likwezeka,

Dzanja lamanja la Yehova lichita mwamphamvu.

17 Sindidzafa koma ndidzakhala ndi moyo,

ndipo ndidzafotokozera ntchito za Yehova.

18 Kulanga anandilangadi Yehova:

koma sanandipereke kuimfa ai.

19 Nditsegulireni zipata za chilungamo;

ndidzalowamo, ndidzayamika Yehova.

20 Chipata cha Yehova ndi ichi;

olungama adzalowamo.

21 Ndidzakuyamikani, popeza munandiyankha,

ndipo munakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene omangawo anaukana

wakhala mutu wa pangodya.

23 Ichi chidzera kwa Yehova;

nchodabwitsa ichi pamaso pathu.

24 Tsiku ili ndilo adaliika Yehova;

tidzasekera ndi kukondwera m’mwemo.

25 Tikupemphani, Yehova, tipulumutseni tsopano;

tikupemphani, Yehova, tipindulitseni tsopano.

26 Wodala wakudzayo m’dzina la Yehova;

takudalitsani kochokera m’nyumba ya Yehova.

27 Yehova ndiye Mulungu, amene anatiunikira;

mangani nsembe ndi zingwe, kunyanga za guwa la nsembe.

28 Inu ndinu Mulungu wanga, ndipo ndidzakuyamikani;

ndinu Mulungu wanga, ndidzakukwezani.

29 Yamikani Yehova, pakuti Iye ndiye wabwino,

pakuti chifundo chake nchosatha.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/118-ea1f8e4aa14fcd99c2b772e2e0d4c19c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *