Olanditsidwa, alendo, omangidwa, odwala, amalinyero ndi ena onse alemekeze Yehova
1 Yamikani Yehova pakuti Iye ndiye wabwino;
pakuti chifundo chake nchosatha.
2 Atere oomboledwa a Yehova,
amene anawaombola m’dzanja la wosautsa;
3 nawasokolotsa kumaiko,
kuchokera kum’mawa ndi kumadzulo,
kumpoto ndi kunyanja.
4 Anasokera m’chipululu, m’njira yopanda anthu;
osapeza mzinda wokhalamo.
5 Anamva njala ndi ludzu,
moyo wao unakomoka m’kati mwao.
6 Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao,
ndipo anawalanditsa m’kupsinjika kwao.
7 Ndipo anawatsogolera panjira yolunjika,
kuti amuke kumzinda wokhalamo.
8 Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,
ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!
9 Pakuti akhutitsa mtima wolakalaka,
nadzaza mtima wanjala ndi zabwino.
10 Iwo akukhala mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,
omangika ndi kuzunzika ndi chitsulo;
11 popeza anapikisana nao mau a Mulungu,
napeputsa uphungu wa Wam’mwambamwamba;
12 kotero kuti anagonjetsa mtima wao ndi chovuta;
iwowa anakhumudwa koma panalibe mthandizi.
13 Pamenepo anafuulira kwa Yehova mumsauko mwao,
ndipo anawapulumutsa m’kupsinjika kwao.
14 Anawatulutsa mumdima ndi mu mthunzi wa imfa,
nadula zomangira zao.
15 Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,
ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!
16 Popeza adaswa zitseko zamkuwa,
nathyola mipiringidzo yachitsulo.
17 Anthu opusa azunzika chifukwa cha zolakwa zao,
ndi chifukwa cha mphulupulu zao.
18 Mtima wao unyansidwa nacho chakudya chilichonse;
ndipo ayandikira zipata za imfa.
19 Pamenepo afuulira kwa Yehova m’kusauka kwao,
ndipo awapulumutsa m’kupsinjika kwao.
20 Atumiza mau ake nawachiritsa,
nawapulumutsa ku chionongeko chao.
21 Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,
ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!
22 Ndipo apereke nsembe zachiyamiko,
nafotokozere ntchito zake ndi kufuula mokondwera.
23 Iwo akutsikira kunyanja nalowa m’zombo,
akuchita ntchito zao pamadzi aakulu.
24 Iwowa apenya ntchito za Yehova,
ndi zodabwitsa zake m’madzi ozama.
25 Popeza anena, nautsa namondwe,
amene autsa mafunde ake.
26 Akwera kuthambo, atsikira kozama;
mtima wao usungunuka nacho choipacho.
27 Adzandira napambanitsa miyendo ngati munthu woledzera,
nathedwa nzeru konse.
28 Pamenepo afuulira kwa Yehova m’kusauka kwao,
ndipo awatulutsa m’kupsinjika kwao.
29 Asanduliza namondwe akhale bata,
kotero kuti mafunde ake atonthole.
30 Pamenepo akondwera, popeza pagwa bata;
ndipo Iye awatsogolera kudooko afunako.
31 Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake,
ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!
32 Amkwezenso mu msonkhano wa anthu,
namlemekeze pokhala akulu.
33 Asanduliza mitsinje ikhale chipululu,
ndi akasupe a madzi akhale nthaka youma.
34 Dziko la zipatso, likhale lakhulo,
chifukwa cha choipa cha iwo okhalamo.
35 Asanduliza chipululu chikhale thawale,
ndi dziko louma likhale akasupe a madzi.
36 Ndi apo akhalitsa anjala,
kuti amangeko mzinda wokhalamo anthu;
37 nafese m’minda, naoke mipesa,
ndiyo yakubala zipatso zambiri.
38 Ndipo awadalitsa, kotero kuti achuluka kwambiri;
osachepsanso zoweta zao.
39 Koma achepanso, nawerama,
chifukwa cha chisautso, choipa ndi chisoni.
40 Atsanulira chimpepulo pa akulu,
nawasokeretsa m’chipululu mopanda njira.
41 Koma aika waumphawi pamsanje posazunzika,
nampatsa mabanja ngati gulu la nkhosa.
42 Oongoka mtima adzachiona nadzasekera;
koma chosalungama chonse chitseka pakamwa pake.
43 Wokhala nazo nzeru asamalire izi,
ndipo azindikire zachifundo za Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/107-c55deac6f7b308043773ea8648e7aa75.mp3?version_id=1068—