Categories
MASALIMO

MASALIMO 104

Ulemerero wa Mulungu m’zolengedwa ndi m’kuzisunga komwe

1 Lemekeza Yehova, moyo wanga;

Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu;

2 muvala ulemu ndi chifumu.

Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala;

ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.

3 Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m’madzi;

naika makongwa akhale agaleta ake;

nayenda pa mapiko a mphepo.

4 Amene ayesa mphepo amithenga ake;

lawi la moto atumiki ake;

5 anakhazika dziko lapansi pa maziko ake,

silidzagwedezeka kunthawi yonse.

6 Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi chovala;

madzi anafikira pamwamba pa mapiri.

7 Pa kudzudzula kwanu anathawa;

anathawa msanga liu la bingu lanu;

8 anakwera m’mapiri, anatsikira m’zigwa,

kufikira malo mudawakonzeratu.

9 Munaika malire kuti asapitirireko;

kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

10 Atumiza akasupe alowe m’makwawa;

ayenda pakati pa mapiri:

11 Zimamwamo nyama zonse zakuthengo;

mbidzi zipherako ludzu lao.

12 Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo,

zimaimba pakati pa mitawi.

13 Iye amwetsa mapiri mochokera m’zipinda zake:

Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu.

14 Ameretsa msipu ziudye ng’ombe,

ndi zitsamba achite nazo munthu;

natulutse chakudya chochokera m’nthaka;

15 ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,

ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake,

ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

16 Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi;

mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka;

17 m’mwemo mbalame zimanga zisa zao;

pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza.

18 Mapiri aatali ndiwo ayenera zinkhoma;

pamatanthwe mpothawirapo mbira.

19 Anaika mwezi nyengo zake;

dzuwa lidziwa polowera pake.

20 Muika mdima ndipo pali usiku;

pamenepo zituluka zilombo zonse za m’thengo.

21 Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao,

nifuna chakudya chao kwa Mulungu.

22 Potuluka dzuwa, zithawa,

zigona pansi m’ngaka mwao.

23 Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake,

nagwiritsa kufikira madzulo.

24 Ntchito zanu zichulukadi, Yehova!

Munazichita zonse mwanzeru;

dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.

25 Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando,

m’mwemo muli zokwawa zosawerengeka;

zamoyo zazing’ono ndi zazikulu.

26 M’mwemo muyenda zombo;

ndiLeviyataniamene munamlenga aseweremo.

27 Izi zonse zikulindirirani,

muzipatse chakudya chao pa nyengo yake.

28 Chimene muzipatsa zigwira;

mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.

29 Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa;

mukalanda mpweya wao, zikufa,

ndipo zibwerera kufumbi kwao.

30 Potumizira mzimu wanu, zilengedwa;

ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.

31 Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha;

Yehova akondwere mu ntchito zake;

32 amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera;

akhudza mapiri, ndipo afuka.

33 Ndidzaimbira Yehova m’moyo mwanga:

ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.

34 Pomlingirira Iye pandikonde;

ndidzakondwera mwa Yehova.

35 Ochimwa athedwe kudziko lapansi,

ndi oipa asakhalenso.

Yamika Yehova, moyo wanga.

Aleluya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/104-90ec120186134980a5e19a6a2f99ffb8.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *