Wopsinjika apempha Mulungu achitire anthu ake chifundo, amitundu nammverenso
Pemphero la Wozunzika, m’mene anakomoka natsanulira cholingalira chake pamaso pa Yehova.
1 Yehova, imvani pemphero langa,
ndipo mfuu wanga ufikire Inu.
2 Musandibisire nkhope yanu tsiku la nsautso yanga;
munditchereze khutu lanu;
tsiku limene ndiitana ine mundiyankhe msanga.
3 Popeza masiku anga akanganuka ngati utsi,
ndi mafupa anga anyeka ngati nkhuni.
4 Mtima wanga ukunga udzu womweta, nufota;
popeza ndiiwala kudya mkate wanga.
5 Chifukwa cha liu la kubuula kwanga
mnofu wanga umamatika kumafupa anga.
6 Ndikunga vuwo m’chipululu;
ndikhala ngati kadzidzi wa kumabwinja.
7 Ndidikira, ndikhala ngati mbalame
ili yokha pamwamba pa tsindwi.
8 Adani anga anditonza tsiku lonse;
akundiyalukirawo alumbirira ine.
9 Pakuti ndadya mapulusa ngati mkate,
ndi kusakaniza chomwera changa ndi misozi,
10 chifukwa cha ukali wanu ndi kuzaza kwanu;
popeza munandinyamula ndipo munandigwetsa.
11 Masiku anga akunga mthunzi womka m’tali;
ndipo ine ndauma ngati udzu.
12 Koma Inu, Yehova, mukhalabe kunthawi yonse;
ndi chikumbukiro chanu ku mibadwomibadwo.
13 Inu mudzauka, ndi kuchitira nsoniZiyoni;
popeza yafika nyengo yakumchitira chifundo, nyengo yoikika.
14 Pakuti atumiki anu akondwera nayo miyala yake,
nachitira chifundo fumbi lake.
15 Pamenepoamitunduadzaopa dzina la Yehova,
ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova anamanga Ziyoni,
anaoneka mu ulemerero wake;
17 anasamalira pemphero la iwo akusowa konse,
osapepula pemphero lao.
18 Ichi adzachilembera mbadwo ukudza;
ndi mtundu wa anthu umene udalengedwa udzamlemekeza Yehova.
19 Pakuti anapenya pansi ali kumwamba kuli malo ake opatulika;
Yehova pokhala kumwamba anapenya dziko lapansi;
20 kuti amve kubuula kwa wandende;
namasule ana a imfa.
21 Kuti anthu alalikire dzina la Yehova mu Ziyoni,
ndi chilemekezo chake muYerusalemu;
22 Posonkhana pamodzi mitundu ya anthu,
ndi maufumu kuti atumikire Yehova.
23 Iye analanda mphamvu yanga panjira;
anachepsa masiku anga.
24 Ndinati, Mulungu wanga, musandichotse pakati pa masiku anga:
Zaka zanu zikhalira m’mibadwomibadwo.
25 Munakhazika dziko lapansi kalelo;
ndipo zakumwamba ndizo ntchito ya manja anu.
26 Zidzatha izi, koma Inu mukhala:
Inde, zidzatha zonse ngati chovala;
mudzazisintha ngati malaya, ndipo zidzasinthika:
27 Koma Inu ndinu yemweyo,
ndi zaka zanu sizifikira kutha.
28 Ana a atumiki anu adzakhalitsa,
ndi mbeu zao zidzakhazikika pamaso panu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/102-49465b440a1a1f3bc67c9b0b36b64c7c.mp3?version_id=1068—