Davide akuti adzasamala okhulupirika nadzachotsa oipa
Salimo la Davide.
1 Ndidzaimba zachifundo ndi chiweruzo;
ndidzaimba zakukulemekezani Inu, Yehova.
2 Ndidzachita mwanzeru m’njira yangwiro;
mudzandidzera liti?
Ndidzayenda m’nyumba mwanu ndi mtima wangwiro.
3 Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga;
chochita iwo akupatuka padera chindiipira;
sichidzandimamatira.
4 Mtima wopulukira udzandichokera;
sindidzadziwana naye woipa.
5 Wakuneneza mnzake m’tseri ndidzamdula;
wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
6 Maso anga ayang’ana okhulupirika m’dziko, kuti akhale ndi Ine;
iye amene ayenda m’njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.
7 Wakuchita chinyengo sadzakhala m’kati mwa nyumba yanga;
wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.
8 Mamawa onse ndidzadula oipa onse a m’dziko;
kuduliratu onse akuchita zopanda pake kumzinda wa Yehova.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/101-c79d9d75fa245d4b3f9ed3cd86427ff4.mp3?version_id=1068—