Categories
MASALIMO

MASALIMO 10

Athamangira Mulungu pothawa adani omtsata

1 Muimiranji patali, Yehova?

Mubisaliranji m’nyengo za nsautso?

2 Podzikuza woipa apsereza waumphawi;

agwe m’chiwembu anapanganacho.

3 Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake,

adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

4 Woipa, monga mwa kudzikuza kwa nkhope yake, akuti, Sadzafunsira.

Malingaliro ake onse akuti, Palibe Mulungu.

5 Mayendedwe ake alimbika nthawi zonse;

maweruzo anu ali pamwamba posaona iye;

adani ake onse awanyodola.

6 Ati mumtima mwake, Sindidzagwedezeka ine;

ku mibadwomibadwo osagwa m’tsoka ine.

7 M’kamwa mwake mwadzala kutemberera

ndi manyengo ndi kuchenjerera;

pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.

8 Akhala m’molalira midzi;

mobisalamo akupha munthu wosachimwa.

Ambisira waumphawi nkhope yake.

9 Alalira monga mkango m’ngaka mwake;

alalira kugwira wozunzika,

agwira wozunzika, pakumkola mu ukonde mwake.

10 Aunthama, nawerama,

ndipo aumphawi agwa m’zala zake.

11 Anena m’mtima mwake, Mulungu waiwala;

wabisa nkhope yake; sapenya nthawi zonse.

12 Ukani, Yehova; samulani dzanja lanu, Mulungu;

musaiwale ozunzika.

13 Woipa anyozeranji Mulungu,

anena m’mtima mwake, Simudzafunsira?

14 Mwapenya; pakuti mumayang’anira chivutitso

ndi chisoni kuti achipereke m’manja mwanu;

waumphawi adzipereka kwa Inu;

wamasiye mumakhala mthandizi wake.

15 Thyolani mkono wa woipa;

ndipo wochimwa, mutsate choipa chake

kufikira simuchipezanso china.

16 Yehova ndiye Mfumu kunthawi yamuyaya;

aonongekaamitundum’dziko lake.

17 Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika,

mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;

18 kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi,

kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/PSA/10-4363149da873ad6239f11877cd226247.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *