Mawalitsidwe a Yesu paphiri
1 Ndipo ananena nao, Ndithu ndinena ndi inu kuti, Alipo ena akuimirira pano, amene sadzalawa imfa konse, kufikira akaona Ufumu wa Mulungu utadza ndi mphamvu.
2 Ndipo atapita masiku asanu ndi limodzi, Yesu anatenga Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nakwera nao paphiri lalitali padera pa okha; ndipo anasandulika pamaso pao:
3 ndipo zovala zake zinakhala zonyezimira, zoyera mbuu; monga ngati muomba wotsuka nsalu padziko lapansi sangathe kuziyeretsai.
4 Ndipo anaonekera kwa iwo Eliya ndi Mose, alikulankhulana ndi Yesu.
5 Ndipo Petro anayankha, nanena ndi Yesu,Rabi, kutikomera ife kukhala pano; ndipo timange misasa itatu; umodzi wa inu, ndi wina wa Mose, ndi wina wa Eliya.
6 Pakuti sanadziwe chimene adzayankha; chifukwa anachita mantha ndithu.
7 Ndipo panadza mtambo wakuwaphimba iwo; ndipo mau munatuluka m’mtambomo, kuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa; mverani Iye.
8 Ndipo dzidzidzi pounguzaunguza, sanapenye munthu wina yense, koma Yesu yekha, ndi iwo eni.
9 Ndipo pakutsika iwo paphiri, Iye anawalamula kuti asauze munthu zinthu zimene adaziona, koma pameneMwana wa Munthuakadzauka kwa akufa.
10 Ndipo anasunga mauwo, nafunsana mwa iwo okha, kuti, Kuuka kwa akufa nchiyani?
11 Ndipo anamfunsa Iye, nanena, Nanga alembi anena kuti adzayamba kufika Eliya?
12 Ndipo Iye ananena nao, Eliya ayamba kudza ndithu, nadzakonza zinthu zonse; ndipo kwalembedwa bwanji za Mwana wa Munthu, kuti ayenera kumva zowawa zambiri ndi kuyesedwa chabe?
13 Koma ndinena ndi inu kuti anafikadi Eliya, ndipo anamchitiranso zilizonse iwo anazifuna, monga kwalembedwa za iye.
Achiritsidwa mwana wogwidwa ndi mzimu wosalankhula
14 Ndipo pamene anadza kwaophunzira, anaona khamu lalikulu la anthu ozungulira iwo, ndi alembi alikufunsana nao.
15 Ndipo pomwepo anthu onse a khamulo, pakumuona Iye, anazizwa kwambiri, namthamangira Iye, namlonjera.
16 Ndipo anawafunsa iwo, Mufunsana nao chiyani?
17 Ndipo wina wa m’khamulo anamyankha Iye, kuti, Mphunzitsi, ndadza naye kwa Inu mwana wanga, ali nao mzimu wosalankhula;
18 ndipo ponse pamene umgwira, umgwetsa; ndipo achita thovu, nakukuta mano, nanyololoka; ndipo ndinalankhula nao ophunzira anu kuti autulutse; koma sanakhoze.
19 Ndipo Iye anawayankha nanena, Mbadwo wosakhulupirira inu, ndidzakhala ndi inu kufikira liti? Ndidzakulekererani nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine.
20 Ndipo anadza naye kwa Iye; ndipo pakumuona, pomwepo mzimuwo unamng’amba koopsa; ndipo anagwa pansi navimvinika ndi kuchita thovu.
21 Ndipo Iye anafunsa atate wake, kuti, Chimenechi chinayamba kumgwira liti? Ndipo anati, Chidamyamba akali mwana.
22 Ndipo kawirikawiri ukamtaya kumoto ndi kumadzi, kumuononga; koma ngati mukhoza kuchita kanthu mtithandize, ndi kutichitira chifundo.
23 Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.
24 Pomwepo atate wa mwana anafuula, nanena, Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga.
25 Ndipo pamene Yesu anaona kuti khamu la anthu lilikuthamangira pamodzi, anadzudzula mzimu woipawo, nanena ndi uwo, Mzimu wosalankhula ndi wogontha iwe, Ine ndikulamula iwe, tuluka mwa iye, ndipo usalowenso mwa iye.
26 Ndipo pamene unafuula, numng’ambitsa, unatuluka; ndipo mwana anakhala ngati wakufa; kotero kuti ambiri ananena, Wamwalira.
27 Koma Yesu anamgwira dzanja lake, namnyamutsa; ndipo anaimirira.
28 Ndipo pamene Iye adalowa m’nyumba, ophunzira ake anamfunsa m’tseri, kuti, Nanga bwanji sitinathe ife kuutulutsa?
29 Ndipo Iye anati kwa iwo, Mtundu uwu sungathe kutuluka ndi kanthu kena konse, koma ndi kupemphera.
Yesu anena kachiwiri za imfa yake
30 Ndipo anachoka iwo kumeneko, napyola pakati pa Galileya; ndipo Iye sanafune kuti munthu adziwe.
31 Pakuti anaphunzitsa ophunzira ake, nanena nao, kuti, Mwana wa Munthu aperekedwa m’manja anthu, ndipo adzamupha Iye; ndipo ataphedwa, adzauka pofika masiku atatu.
32 Koma iwo sanazindikire mauwo, naopa kumfunsa.
Wamkulu ndani mu Ufumu wa Mulungu?
33 Ndipo iwo anadza ku Kapernao; ndipo pamene anakhala m’nyumba, Iye anawafunsa, Munalikutsutsana ninji panjira?
34 Koma iwo anakhala chete; pakuti anatsutsana wina ndi mnzake panjira, kuti, wamkulu ndani?
35 Ndipo m’mene anakhala pansi anaitana khumi ndi awiriwo; nanena nao, Ngati munthu afuna kukhala woyamba, akhale wakuthungo wa onse, ndi mtumiki wa onse.
36 Ndipo anatenga kamwana, nakaika pakati pao, nakayangata, nanena nao,
37 Munthu aliyense adzalandira kamodzi ka tiana totere chifukwa cha dzina langa, alandira Ine; ndipo yense amene akalandira Ine, salandira Ine, koma Iye amene anandituma Ine.
Osatsutsana nafe athandizana nafe
38 Yohane anati kwa Iye, Mphunzitsi, tinaona munthu alikutulutsa ziwanda m’dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa sanalikutsata ife.
39 Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m’dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.
40 Pakuti iye wosatsutsana ndi ife athandizana nafe.
41 Pakuti munthu aliyense adzakumwetsani inu chikho cha madzi m’dzina langa chifukwa muli ake aKhristu, indetu ndinena ndi inu, kuti iye sadzataya konse mphotho yake.
Malakwitso
42 Ndipo yense amene adzalakwitsa kamodzi ka tiana timeneto takukhulupirira Ine, kuli kwabwino kwa iye makamaka kuti mwala waukulu wamphero ukolowekedwe m’khosi mwake, naponyedwe iye m’nyanja.
43 Ndipo ngati dzanja lako likulakwitsa iwe, ulidule: nkwabwino kwa iwe kulowa m’moyo wopunduka dzanja, koposa kukhala ndi manja ako awiri ndi kulowa muGehena, m’moto wosazima.
45 Ndipo ngati phazi lako likulakwitsa, ulidule; kulowa iwe m’moyo wopunduka mwendo, kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi mapazi ako awiri ndi kuponyedwa mu Gehena.
47 Ndipo ngati diso lako likulakwitsa ulikolowole; kulowa iwe mu Ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi kuli kwabwino koposa ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu Gehena;
48 kumeneko mphutsi yao siikufa, ndi moto suzimidwa.
49 Pakuti onse adzathiridwa mchere wamoto.
50 Mchere uli wabwino; koma ngati mchere unasukuluka, mudzaukoleretsa ndi chiyani? Khalani nao mchere mwa inu nokha, ndipo khalani ndi mtendere wina ndi mnzake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/9-14eae60b02e6bfe589c82130bbb6d20a.mp3?version_id=1068—