Yesu achulukitsa mikate kachiwiri
1 Masiku ajawo pakukhalanso khamu lalikulu la anthu, ndipo analibe kanthu kakudya, Iye anadziitaniraophunziraake, nanena nao,
2 Ndimva nalo chifundo khamulo, chifukwa ali ndi Ine chikhalire masiku atatu, ndipo alibe kanthu kakudya:
3 ndipo ngati ndiwauza iwo amuke kwao osadya kanthu, adzakomoka panjira; ndipo ena a iwo achokera kutali.
4 Ndipo ophunzira ake anamyankha Iye, kuti, Munthu adzatha kutenga kuti mikate yakukhutitsa anthu awa m’chipululu muno?
5 Ndipo anawafunsa, Muli nayo mikate ingati? Ndipo anati, Isanu ndi iwiri.
6 Ndipo analamulira anthu a khamulo akhale pansi; natenga mikate isanu ndi iwiriyo, nayamika, nanyema, napatsa ophunzira ake, kuti apereke kwa iwo; ndipo anapereka kwa khamulo.
7 Ndipo anali nato tinsomba towerengeka; ndipo Iye anatidalitsa, nati atipereke itonso.
8 Ndipo anadya nakhuta; ndipo anatola makombo madengu asanu ndi awiri.
9 Ndipo iwo anali ngati zikwi zinai; ndipo Iye analawirana nao.
10 Ndipo pomwepo analowa m’ngalawa ndi ophunzira ake, nafika ku mbali ya ku Dalamanuta.
Afarisi afuna chizindikiro
11 NdipoAfarisianatuluka, nayamba kufunsana naye, ndi kufuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba, namuyesa Iye.
12 Ndipo anausitsa moyo m’mzimu wake, nanena, Anthu a mbadwo uno afunafuna chizindikiro bwanji? Indetu ndinena kwa inu, ngati chizindikiro chidzapatsidwa kwa mbadwo uno!
13 Ndipo anawasiya iwo, nalowanso m’ngalawa, nachoka kunka ku tsidya lija.
Chotupitsa mkate cha Afarisi
14 Ndipo ophunzira adaiwala kutenga mikate, ndipo analibe mkate m’ngalawa koma umodzi wokha.
15 Ndipo Iye anawalamula, nanena, Yang’anirani, penyani kuti mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi, ndi chotupitsa mkate chaHerode.
16 Ndipo anatsutsana wina ndi mnzake, nanena kuti, Tilibe mikate.
17 Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma?
18 Pokhala nao maso simupenya kodi? Ndi pokhala nao makutu simukumva kodi? Ndipo simukumbukira kodi?
19 Pamene ndinawagawira anthu zikwi zisanu mikate isanu ija, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ananena naye, Khumi ndi iwiri.
20 Ndipo mikate isanu ndi iwiri kwa anthu zikwi zinai, munatola madengu angati odzala ndi makombo? Ndipo ananena naye, Asanu ndi awiri.
21 Ndipo Iye ananena nao, Simudziwitsa ngakhale tsopano kodi?
Yesu achiritsa munthu wakhungu ku Betsaida
22 Ndipo anadza ku Betsaida. Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wakhungu, nampempha Iye kuti amkhudze.
23 Ndipo anamgwira dzanja munthu wakhunguyo, natulukira naye kunja kwa mudzi; ndipo atamthira malovu m’maso mwake, naika manja pa iye, anamfunsa, Uona kanthu kodi?
24 Ndipo anakweza maso, nanena, Ndiona anthu; pakuti ndiwapenya ayendayenda ngati mitengo.
25 Pamenepo anaikanso manja m’maso mwake; ndipo anapenyetsa, nachiritsidwa, naona zonse mbee.
26 Ndipo anamtumiza amuke kwao, nanena, Usalowe konse m’mudzi.
Petro avomereza Khristu
27 Ndipo anatuluka Yesu, ndi ophunzira ake, nalowa kumidzi ya ku Kesareya-Filipi; ndipo panjira anafunsa ophunzira ake, nanena nao, Kodi anthu ananena kuti Ine ndine yani?
28 Ndipo ananena, nati, Yohane Mbatizi; ndi ena, Eliya; koma ena, Mmodzi wa aneneri.
29 Ndipo Iye anawafunsa, Koma inu munena kuti ndine yani? Petro anayankha nanena naye, NdinuKhristu.
30 Ndipo anawauzitsa iwo kuti asanene kwa munthu mmodzi za Iye.
Yesu aneneratu za mazunzo ndi imfa yake
31 Ndipo anayamba kuwaphunzitsa, kuti kuyenera kutiMwana wa Munthuakamve zowawa zambiri, nakakanidwe ndi akulu ndi ansembe aakulu, ndi alembi, nakaphedwe, ndipo mkucha wake akauke.
32 Ndipo mauwo ananena poyera. Ndipo Petro anamtenga Iye, nayamba kumdzudzula.
33 Koma Iye anapotoloka, napenya ophunzira ake, namdzudzula Petro, nanena, Choka, pita kumbuyo kwanga,Satanaiwe; popeza susamalira zinthu za Mulungu, koma za anthu.
Kunyamula mtanda
34 Ndipo anadziitanira khamulo la anthu pamodzi ndi ophunzira ake, nati kwa iwo, Ngati munthu afuna kudza pambuyo panga, adzikanize yekha, nanyamule mtanda wake, nanditsate Ine.
35 Pakuti yense wakufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya; ndipo yense wakutaya moyo wake chifukwa cha Ine, ndi chifukwa cha Uthenga Wabwino, adzaupulumutsa.
36 Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?
37 Pakuti munthu akapereka chiyani chosintha nacho moyo wake?
38 Pakuti yense wakuchita manyazi chifukwa cha Ine, ndi cha mau anga mu mbadwo uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachitanso manyazi chifukwa cha iyeyu, pamene Iye adzafika naoangeloake oyera, mu ulemerero wa Atate wake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/8-e87776aaabbc902cb1ecd2ba35a96ccc.mp3?version_id=1068—