Categories
MARKO

MARKO 6

Apeputsa Yesu ku Nazarete

1 Ndipo Iye anatuluka kumeneko; nafika kudziko la kwao; ndipoophunziraake anamtsata.

2 Ndipo pofika tsiku laSabata, anayamba kuphunzitsa m’sunagoge; ndipo ambiri anamva Iye, nazizwa, nanena, Uyu adazitenga kuti izi? Nzeru yopatsidwa kwa munthuyu njotani, ndi zamphamvu zotere zochitidwa ndi manja ake?

3 Si mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Maria, mbale wao wa Yakobo, ndi Yose, ndi Yudasi, ndi Simoni? Ndipo alongo ake sali nafe pano kodi? Ndipo anakhumudwa ndi Iye.

4 Ndipo Yesu ananena kwa iwo,Mnenerisakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwao ndimo, ndi pakati pa abale ake, ndi m’nyumba yake.

5 Ndipo kumeneko sanakhoze Iye kuchita zamphamvu konse, koma kuti anaika manja ake pa anthu odwala owerengeka, nawachiritsa.

6 Ndipo anazizwa chifukwa cha kusakhulupirira kwao. Ndipo anayendayenda m’midzi yozungulirapo, naphunzitsa.

Yesu atuma khumi ndi awiriwo

7 Ndipo anadziitanira khumi ndi awiriwo, nayamba kuwatumiza iwo awiriawiri; nawapatsa mphamvu pa mizimu yonyansa;

8 ndipo anawauza kuti asatenge kanthu ka paulendo, koma ndodo yokha; asatenge mkate, kapena thumba, kapena ndalama m’lamba lao;

9 koma avale nsapato; ndipo anati, Musavale malaya awiri.

10 Ndipo ananena nao, Kumene kulikonse mukalowa m’nyumba, khalani komweko kufikira mukachokako.

11 Ndipo pamalo ponse sakulandirani, kapena kumvera inu, pakuchoka kumeneko, sansani fumbi lili kumapazi anu, likhale mboni ya kwa iwo.

12 Ndipo anatuluka nalalikira kuti anthu atembenuke mitima.

13 Ndipo anatulutsa ziwanda zambiri, nadzoza mafuta anthu ambiri akudwala, nawachiritsa.

Kuphedwa kwa Yohane Mbatizi

14 Ndipo mfumuHerodeanamva izi; pakuti dzina lake lidamveka; ndipo ananena, kuti, Yohane Mbatizi wauka kwa akufa, ndipo chifukwa chake mphamvu izi zichitachita mwa Iye.

15 Koma ena ananena, kuti, Ndiye Eliya. Anati enanso, Ndiye mneneri, monga ngati mmodzi wa aneneriwo.

16 Koma Herode pamene anamva, ananena, Yohane amene ndamdula mutu, wauka iyeyo.

17 Pakuti Herode, mwini yekha, adatuma anthu namgwira Yohane, nammanga m’nyumba yandende, chifukwa cha Herodiasi, mkazi wa Filipo mbale wake; chifukwa adamkwatira iye.

18 Pakuti Yohane adanena kwa Herode, Si kuloledwa kwa inu kukhala naye mkazi wa mbale wanu.

19 Ndipo Herodiasi anamuda, nafuna kumupha; koma sanakhoze;

20 pakuti Herode anaopa Yohane, podziwa kuti ali munthu wolungama ndi woyera mtima, ndipo anamsunga iye. Ndipo pamene anamva iye anathedwa nzeru, nakondwa kumva iye.

21 Ndipo pamene panafika tsiku loyenera, tsiku la kubadwa kwake kwa Herode, iye anawakonzera phwando akulu ake ndi akazembe ake ndi anthu omveka a ku Galileya;

22 ndipo pamene mwana wamkazi wa Herodiasi analowa yekha navina, anakondwetsa Herode ndi iwo akukhala naye pachakudya; ndipo mfumuyo inati kwa buthulo, Tapempha kwa ine chilichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe.

23 Ndipo anamlumbirira iye, kuti, Chilichonse ukandipempha ndidzakupatsa, kungakhale kukugawira ufumu wanga.

24 Ndipo anatuluka, nati kwa amake, Ndidzapempha chiyani? Ndipo iye anati, Mutu wake wa Yohane Mbatizi.

25 Ndipo pomwepo analowa m’mangum’mangu kwa mfumu, napempha kuti, Ndifuna kuti mundipatse tsopano apa, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbale.

26 Ndipo mfumu inamva chisoni chachikulu; koma chifukwa cha malumbiro ake, ndi cha iwo akukhala pachakudya, sanafune kumkaniza.

27 Ndipo pomwepo mfumu inatuma mnyamata, namlamulira akatenge mutu wake; ndipo iye anamuka namdula mutu m’nyumba yandende;

28 natengera mutu wake mumbale, naupereka kwa buthulo; ndipo buthu linaupereka kwa amake.

29 Ndipo m’mene ophunzira ake anamva, anadza nanyamula mtembo wake nauika m’manda.

Yesu achulukitsa mikate

30 Ndipoatumwianasonkhana kwa Yesu; namuuza zilizonse adazichita, ndi zonse adaziphunzitsa.

31 Ndipo Iye ananena nao, idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi. Pakuti akudza ndi akuchoka anali piringupiringu, ndipo analibe nthawi yokwanira kudya.

32 Ndipo anachokera m’ngalawa kunka kumalo achipululu padera.

33 Ndipo anthu anawaona alikumuka, ndipo ambiri anawazindikira, nathamangira limodzi kumeneko pamtunda, ochokera m’midzi monse, nawapitirira.

34 Ndipo anatuluka Iye, naona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.

35 Ndipo pamene dzuwa lidapendeka ndithu, anadza kwa Iye ophunzira ake, nanena, Malo ano nga chipululu, ndi dzuwa lapendeka ndithu;

36 muwauze kuti amuke, alowe kuminda ndi kumidzi yozungulira, akadzigulire okha kanthu kakudya.

37 Koma Iye anayankha nati kwa iwo, Apatseni kudya ndinu. Ndipo iwo ananena naye, Kodi tikapita ife ndi kugula mikate ya pa marupiya atheka mazana awiri, ndi kuwapatsa kudya?

38 Ndipo Iye ananena nao, kuti, Muli nayo mikate ingati? Pitani, mukaone. Ndipo m’mene anadziwa ananena, Isanu, ndi nsomba ziwiri.

39 Ndipo anawalamulira kuti akhalitse pansi onse magulumagulu pamsipu.

40 Ndipo anakhala pansi mabungwemabungwe a makumi khumi, ndi a makumi asanu.

41 Ndipo Iye anatenga mikate isanuyo ndi nsomba ziwirizo nayang’ana kumwamba, nadalitsa, nagawa mikate; napatsa kwa ophunzira kuti apereke kwa iwo; ndi nsomba ziwiri anagawira onsewo.

42 Ndipo anadya iwo onse, nakhuta.

43 Ndipo anatola makombo, madengu khumi ndi iwiri, ndiponso za nsomba.

44 Ndipo amene anadya mikate iyo anali amuna zikwi zisanu.

Yesu ayenda pa nyanja

45 Ndipo pomwepo Iye anakakamiza ophunzira ake alowe m’ngalawa, ndi kumtsogolera kutsidya lija ku Betsaida, m’mene Iye yekha alimkuuza khamulo kuti amuke.

46 Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m’phiri kukapemphera.

47 Ndipo pofika madzulo ngalawa inali pakati pa nyanja, ndi Iye yekha pamtunda.

48 Ndipo pakuwaona ali kuvutidwa ndi kupalasa, pakuti mphepo inadza nikomana nao, pa ulonda wachinai wa usiku Iye anadza kwa iwo, alikuyenda pamwamba pa nyanja; nati awapitirire;

49 koma iwo, pamene anamuona alikuyenda panyanja, anayesa kuti ndi mzukwa, nafuula:

50 pakuti iwo onse anamuona Iye, nanthunthumira. Koma pomwepo anawalankhula nanena nao, Limbani mtima; ndinetu, musaope.

51 Ndipo Iye anakwera, nalowa kwa iwo m’ngalawa, ndipo mphepo inaleka; ndipo anadabwa kwakukulu mwa iwo okha;

52 pakuti sanazindikire za mikateyo, koma mitima yao inauma.

53 Ndipo ataoloka iwo, anafika pamtunda ku Genesarete, nakocheza padooko.

54 Ndipo pamene anatuluka m’ngalawa anamzindikira pomwepo,

55 nathamangira dziko lonselo nayamba kunyamula anthu odwala pa mphasa zao, kufika nao kumene anamva kuti analiko Iye.

56 Ndipo kumene konse adalowa Iye m’midzi, kapena m’mizinda, kapena kumadera, anthu anagoneka odwala pamisika, nampempha Iye kuti akakhudze ngakhale mphonje yokha ya chovala chake; ndipo onse amene anamkhudza anachiritsidwa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/6-44e056abd7acf338f477d9993ae47538.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *