Yesu achiritsa wogwidwa ndi mzimu wonyansa ku Gerasa
1 Ndipo anafika tsidya lina la nyanja, kudziko la Agerasa.
2 Ndipo pamene adatuluka mungalawa, pomwepo anakomana naye munthu wotuluka kumanda wa mzimu wonyansa,
3 amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;
4 pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya.
5 Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m’manda ndi m’mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala.
6 Ndipo pakuona Yesu kutali, anathamanga, namgwadira Iye;
7 ndipo anafuula ndi mau olimba, nanena, Ndili ndi chiyani ine ndi Inu, Yesu Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, msandizunze.
8 Pakuti ananena kwa iye, Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu.
9 Ndipo anamfunsa, Dzina lako ndani? Ndipo ananena kwa Iye, Dzina langa ndine Legio; chifukwa tili ambiri.
10 Ndipo anampempha Iye kwambiri kuti asaitulutsire kunja kwake kwa dziko.
11 Ndipo panali pamenepo gulu lalikulu la nkhumba zilinkudya kuphiri.
12 Ndipo inampempha Iye, kuti, Titumizeni ife mu nkhumbazo, kuti tilowe mu izo.
13 Ndipo anailola. Ndipo mizimu yonyansa inatuluka, nilowa mu nkhumba; ndipo gulu linatsika liwiro potsetsereka ndi kulowa m’nyanja, ndizo ngati zikwi ziwiri; ndipo zinatsamwa m’nyanja.
14 Ndipo akuziweta anathawa, nauza m’mzinda, ndi kuminda. Ndipo anadza kudzaona chochitikacho.
15 Ndipo anadza kwa Yesu, napenya wogwidwa ziwandayo alikukhala pansi, wovala ndi wa nzeru zake zabwino, ndiye amene anali ndi legio; ndipo anaopa iwo.
16 Ndipo adapenyawo adawafotokozera umo anachitira ndi wogwidwa ziwandayo, ndi za nkhumbazo.
17 Ndipo anayamba kumpempha Iye kuti achoke m’malire ao.
18 Ndipo m’mene Iye analikulowa mungalawa, anampempha waziwanda uja kuti akhale ndi Iye.
19 Ndipo sanamlole, koma ananena naye, Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.
20 Ndipo anamuka nayamba kulalikira ku Dekapoli zinthu zazikulu Yesu adamchitira iye; ndipo anthu onse anazizwa.
Mwana wa Yairo. Mkazi wokhudza chofunda cha Yesu
21 Ndipo pamene Yesu anaolokanso mungalawa tsidya lina, khamu lalikulu linasonkhana kwa Iye; ndipo Iye anali pambali pa nyanja.
22 Ndipo anadzako mmodzi wa akulu asunagoge, dzina lake Yairo; ndipo pakuona Iye, anagwada pa mapazi ake, nampempha kwambiri,
23 nanena, kuti, Kamwana kanga kabuthu kalinkutsirizika; ndikupemphani Inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti kapulumuke, ndi kukhala ndi moyo.
24 Ndipo ananka naye pamodzi; ndipo khamu lalikulu linamtsata Iye, ndi kumkanikiza Iye.
25 Ndipo munthu wamkazi amene anali ndi nthenda yachidwalire zaka khumi ndi ziwiri,
26 ndipo anamva zowawa zambiri ndi asing’anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang’ono ponse, koma makamaka nthenda yake idakula,
27 m’mene iye anamva mbiri yake ya Yesu, anadza m’khamu kumbuyo kwake, nakhudza chovala chake.
28 Pakuti ananena iye, Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.
29 Ndipo pomwepo kasupe wa nthenda yake adaphwa; ndipo anazindikira m’thupi kuti anachiritsidwa chivutiko chake.
30 Ndipo pomwepo Yesu, pamene anazindikira mwa Iye yekha kuti mphamvu idatuluka mwa Iye, anapotoloka m’khamu, nanena, Ndani anakhudza zovala zanga?
31 Ndipoophunziraake ananena kwa Iye, Muona kuti khamu lilikukanikiza Inu, ndipo munena kodi, Wandikhudza ndani?
32 Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi.
33 Koma mkaziyo anachita mantha, ndi kunthunthumira, podziwa chimene anamchitira iye, nadza, namgwadira, namuuza choona chonse.
34 Ndipo anati kwa iye, Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.
35 M’mene iye ali chilankhulire, anafika a kunyumba ya mkulu wa sunagoge, nanena, kuti, Mwana wako wafa; uvutiranjinso Mphunzitsi?
36 Koma Yesu wosasamala mau olankhulidwawo, ananena kwa mkulu wa sunagoge, Usaope, khulupirira kokha.
37 Ndipo sanalole munthu yense kutsagana naye, koma Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane mbale wake wa Yakobo.
38 Ndipo anafika kunyumba kwake kwa mkulu wa sunagoge; ndipo anaona chipiringu, ndi ochita maliro, ndi akukuwa ambiri.
39 Ndipo m’mene atalowa, ananena nao, Mubuma ndi kulira bwanji? Mwana sanafe, koma ali m’tulo.
40 Ndipo anamseka Iye pwepwete. Koma Iye anawatulutsa onse, natenga atate wa mwana, ndi amake, ndi ajawo anali naye, nalowa m’mene munali mwanayo.
41 Ndipo anagwira dzanja lake la mwana, nanena kwa iye,Talita koumi, ndiko kunena posandulika, Buthu, ndinena ndi iwe, Uka.
42 Ndipo pomwepo buthulo linauka, niliyenda; pakuti linali la zaka khumi ndi ziwiri. Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.
43 Ndipo anawalamulira kwambiri kuti asadziwe ichi munthu mmodzi, nawauza kuti ampatse iye kudya.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/5-b1dbb167811aa64b74cb4b84357b645d.mp3?version_id=1068—