Fanizo la wofesa
1 Ndipo anayambanso kuphunzitsa pambali pa nyanja. Ndipo anasonkhana kwa Iye khamu lalikulukulu, kotero kuti analowa Iye mungalawa, nakhala m’nyanja; ndipo khamu lonse linakhala pamtunda m’mbali mwa nyanja.
2 Ndipo anawaphunzitsa zinthu zambiri m’mafanizo, nanena nao m’chiphunzitso chake,
3 Mverani: taonani, wofesa anatuluka kukafesa;
4 ndipo kunali, m’kufesa kwake, zina zinagwa m’mbali mwa njira, ndi mbalame zinadza ndi kuzitha kudya.
5 Ndipo zina zinagwa pa nthaka yathanthwe, pamene panalibe nthaka yambiri; ndipo pomwepo zinamera, chifukwa zinalibe nthaka yakuya;
6 ndipo litakwera dzuwa zinapserera; ndipo popeza zinalibe mizu zinakhwinyata.
7 Ndipo zina zinagwa paminga, ndipo minga inakula, nkuzitsamwitsa, ndipo sizinabale zipatso.
8 Ndipo zina zinagwa m’nthaka yabwino, ndipo zinapatsa zipatso, ndi kukula ndi kuchuluka; ndipo zinabala kupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
9 Ndipo ananena, Amene ali nao makutu akumva amve.
10 Ndipo pamene anakhala pa yekha, iwo amene anali pafupi ndi Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo anamfunsa za mafanizo.
11 Ndipo Iye ananena nao, Kwa inu kwapatsidwa chinsinsi cha Ufumu wa Mulungu; koma kwa iwo ali kunja zonse zichitidwa m’mafanizo;
12 kuti kupenya apenye, koma asazindikire; ndipo kumva amve, koma asadziwitse; kuti pena angatembenuke, ndi kukhululukidwa.
13 Ndipo ananena nao, Simudziwa kodi fanizo ili? Mukazindikira bwanji mafanizo onse?
Kumasulira kwa fanizo la wofesa
14 Wofesa afesa mau.
15 Ndipo iwo ndiwo a m’mbali mwa njira mofesedwamo mau; ndipo pamene anamva, pomwepo akudzaSatananachotsa mau ofesedwa mwa iwo.
16 Ndipo momwemonso iwo ndiwo amene afesedwa pathanthwe, atamva mau, awalandira pomwepo ndi kusekera;
17 ndipo alibe mizu mwa iwo okha, koma akhala kanthawi; pamenepo pakudza masautso kapena mazunzo chifukwa cha mau, pomwepo akhumudwa.
18 Ndipo ena ndiwo akufesedwa kuminga; iwo ndiwo amene adamva mau,
19 ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.
20 Ndipo iwo ofesedwa pa nthaka yabwino ndiwo oterewa akumva mau, nawalandira, nabala zipatso zakupindula makumi atatu, ndi makumi asanu ndi limodzi, ndi makumi khumi.
Fanizo la nyali
21 Ndipo ananena ndi iwo, Kodi atenga nyali kuti akaivundikire mbiya, kapena akaiike pansi pa kama, osati kuti akaiike pa choikapo chake?
22 Pakuti kulibe kanthu kobisika, koma kuti kaonetsedwe; kapena kulibe kanthu kanakhala kam’tseri, koma kuti kakaululidwe.
23 Ngati munthu ali nao makutu akumva, amve.
24 Ndipo ananena nao, Yang’anirani chimene mukumva; ndi muyeso umene muyesera nao udzayesedwa kwa inu; ndipo kudzaonjezedwa kwa inu.
25 Pakuti kwa iye amene ali nako kanthu, kadzapatsidwa; ndipo kwa iye amene alibe kanthu, kadzachotsedwa ngakhale kanthu kalikonse ali nako.
Fanizo la mbeu
26 Ndipo ananena, Ufumu wa Mulungu uli wotero, monga ngati munthu akataya mbeu panthaka;
27 nakagona ndi kuuka, usiku ndi usana, ndipo mbeu zikamera, ndi kukula, iye sadziwa umo zichitira.
28 Nthaka ibala zipatso zake yokha; uyamba mmera, zitsata ngala, pamenepo maso okhwima m’ngalamo.
29 Pakucha zipatso, pamenepo atenga chisenga, pakuti nthawi yakumweta yafika.
Fanizo la mbeu yampiru
30 Ndipo ananena, Tidzafaniziranji Ufumu wa Mulungu? Kapena tidzaulinganiza ndi fanizo lotani?
31 Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko,
32 koma pamene ifesedwa, imera nkukula koposa zitsamba zonse, nkukhala ndi nthambi zazikulu; kotero kuti mbalame za m’mlengalenga zikhoza kubindikira mumthunzi mwake.
33 Ndipo ndi mafanizo otere ambiri analankhula nao mau, monga anakhoza kumva;
34 ndipo sanalankhule nao wopanda fanizo: koma m’tseri anatanthauzira zonse kwaophunziraake.
Yesu aletsa namondwe
35 Ndipo dzuwa lomwelo, pofika madzulo, ananena kwa iwo, Tiolokere tsidya lina.
36 Ndipo posiya khamulo anamtenga apite nao, monga momwe anali, mungalawa. Ndipo panali ngalawa zina pamodzi ndi Iye.
37 Ndipo panauka namondwe wamkulu wa mphepo, ndi mafunde anagavira mungalawa, motero kuti ngalawa inayamba kudzala.
38 Ndipo Iye mwini anali kutsigiro, nagona tulo pamtsamiro; ndipo anamuutsa Iye nanena kwa Iye, Mphunzitsi, kodi simusamala kuti titayika ife?
39 Ndipo anauka, nadzudzula mphepo, nati kwa nyanja, kuti, Tonthola, khala bata. Ndipo mphepo inaleka, ndipo kunagwa bata lalikulu.
40 Ndipo ananena nao, Muchitiranji mantha? Kufikira tsopano mulibe chikhulupiriro kodi?
41 Ndipo iwo anachita mantha aakulu, nanenana wina ndi mnzake, Uyu ndani nanga, kuti ingakhale mphepo ndi nyanja zimvera Iye?
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/4-3e8b40ea9cc6590ef53e50c37c8f2678.mp3?version_id=1068—