Categories
MARKO

MARKO 15

Yesu aweruzidwa ndi Pilato

1 Ndipo pomwepo mamawa anakhala upo ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, ndi alembi, ndi akulu a milandu onse, namanga Yesu, namtenga, nampereka kwa Pilato.

2 Ndipo Pilato anamfunsa Iye, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo anayankha, nanena naye, Mwatero.

3 Ndipo ansembe aakulu anamnenera Iye zinthu zambiri.

4 Ndipo Pilato anamfunsanso, nanena, Suyankha kanthu kodi? Taona, akunenera Iwe zinthu zambiri zotere.

5 Koma Yesu sanayankhenso kanthu; kotero kuti Pilato anazizwa.

6 Ndipo ankawamasulira pachikondwerero wandende mmodzi, amene iwo anampempha.

7 Ndipo analipo wina dzina lake Barabasi, womangidwa pamodzi ndi opanduka, amene anapha munthu mumpanduko.

8 Ndipo khamu la anthu anabwera nayamba kupempha kuti achite monga anali kuwachitira nthawi zonse.

9 Ndipo Pilato anawayankha, nanena nao, Kodi mufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?

10 Pakuti anazindikira kuti ansembe aakulu anampereka Iye mwanjiru.

11 Koma ansembe aakulu anasonkhezera khamulo, kuti makamaka awamasulire Barabasi.

12 Ndipo Pilato anawayankhanso, nati kwa iwo, Pamenepo ndidzachita chiyani ndi Iye amene mumtchula mfumu ya Ayuda?

13 Ndipo anafuulanso, Mpachikeni pamtanda.

14 Ndipo Pilato ananena nao, Pakuti Iye anachita choipa chotani? Koma iwo anafuulitsatu, Mpachikeni Iye.

15 Ndipo Pilato pofuna kuwakhazika mtima anthuwo, anawamasulira Barabasi, napereka Yesu, atamkwapula, akampachike pamtanda.

16 Ndipo asilikali anachoka naye nalowa m’bwalo, ndilo Pretorio; nasonkhanitsa gulu lao lonse.

17 Ndipo anamveka Iye chibakuwa, naluka korona waminga, namveka pa Iye;

18 Ndipo anayamba kumlankhula Iye, kuti, Tikuoneni, mfumu ya Ayuda!

19 Ndipo anampanda Iye pamutu pake ndi bango, namthira malovu, nampindira maondo, namlambira.

20 Ndipo atatha kumnyoza anamvula chibakuwacho namveka Iye zovala zake. Ndipo anatuluka naye kuti akampachike Iye pamtanda.

Ampachika Yesu pamtanda

21 Ndipo anakakamiza wina wopitirirapo, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, atate wao wa Aleksandro ndi Rufu, kuti anyamule mtanda wake.

22 Ndipo anamtenga kunka naye kumalo Gologota, ndiwo, osandulika, Malo a Bade.

23 Ndipo anampatsa vinyo wosakaniza ndimure; koma Iye sanamlandire.

24 Ndipo anampachika Iye, nagawana zovala zake mwa iwo okha, ndi kuchita maere pa izo, kuti adziwe yense adzatenga chiyani.

25 Ndipo panali ora lachitatu, ndipo anampachika Iye.

26 Ndipo lembo la mlandu wake linalembedwa pamwamba, MFUMU YA AYUDA.

27 Ndipo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri; mmodzi kudzanja lake lamanja ndi wina kulamanzere.

29 Ndipo iwo akupitirirapo anamchitira mwano, napukusa mitu yao, nanena, Ha! Iwe wakupasula Kachisi, ndi kummanga masiku atatu,

30 udzipulumutse mwini, nutsike pamtanda.

31 Moteronso ansembe aakulu anamtonza mwa iwo okha pamodzi ndi alembi, nanena, Anapulumutsa ena; sangathe kudzipulumutsa yekha.

32 Atsike tsopano pamtanda,Khristumfumu ya Israele, kuti tione, ndi kukhulupirira. Ndipo iwo akupachikidwa naye anamlalatira.

Yesu afa pamtanda

33 Ndipo pofika ora lachisanu ndi chimodzi, panali mdima padziko lonse, kufikira ora lachisanu ndi chinai.

34 Ndipo pa ora lachisanu ndi chinai Yesu anafuula ndi mau okweza,Eloi, Eloi, lama sabakitani?ndiko kusandulika,

Mulungu wanga, Mulungu wanga mwandisiyiranji Ine?

35 Ndipo ena akuimirirapo, pakumva, ananena, Taonani, aitana Eliya.

36 Ndipo anathamanga wina, nadzaza chinkhupule ndi vinyo wosasa, nachiika pabango, namwetsa Iye, nanena, Lekani; tione ngati Eliya adza kudzamtsitsa.

37 Ndipo Yesu anatulutsa mau okweza, napereka mzimu wake.

38 Ndipo chinsalu chotchinga cha mu Kachisi chinang’ambika pakati, kuyambira kumwamba kufikira pansi.

39 Ndipo pamenekenturiyo, woimirirapo popenyana ndi Iye, anaona kuti anapereka mzimu kotero, anati, Zoonadi, munthu uyu anali Mwana wa Mulungu.

40 Ndipo analinso kumeneko akazi akuyang’anira kutali; mwa iwo anali Maria wa Magadala, ndi Maria amake wa Yakobo wamng’ono ndi wa Yosefe, ndi Salome;

41 amene anamtsata Iye, pamene anali mu Galileya, namtumikira; ndi akazi ena ambiri, amene anakwera kudza ndi Iye kuYerusalemu.

Yesu aikidwa m’manda

42 Ndipo atafika tsono madzulo, popeza mpa tsiku lokonzekera, ndilo la pambuyo paSabata,

43 anadzapo Yosefe wa ku Arimatea, mkulu wa milandu womveka, amene yekha analikuyembekezera Ufumu wa Mulungu; nalimba mtima nalowa kwa Pilato, napempha mtembo wake wa Yesu.

44 Ndipo Pilato anazizwa ngati adamwaliradi; naitana kenturiyo, namfunsa ngati adamwalira kale.

45 Ndipo pamene anachidziwa ndi kenturiyo, anamninkha Yosefe mtembowo.

46 Ndipo anagula bafuta, namtsitsa Iye, namkulunga m’bafutamo, namuika m’manda osemedwa m’thanthwe; nakunkhunizira mwala pakhomo la manda.

47 Ndipo Maria wa Magadala ndi Maria amake wa Yosefe anapenya pomwe anaikidwapo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/15-7d67cb9447ef586d9640862f5b6a4c78.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *