Ansembe aakulu achita chiwembu pa Yesu
1 Ndipo popita masiku awiri kuli phwando laPaskandi Mkate wopanda chotupitsa; ndipo ansembe aakulu ndi alembi anafunafuna momchitira chiwembu, ndi kumupha:
2 pakuti anati, Pachikondwerero ai, kuti pangakhale phokoso la anthu.
Phwando la ku Betaniya
3 Ndipo pakukhala Iye ku Betaniya m’nyumba ya Simoni wakhate, m’mene anaseama kudya, anadzapo mkazi ali nayo nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino anaridoweniweni a mtengo wapatali; naswa nsupayo, nawatsanulira pamutu pake.
4 Koma anakhalako ena anavutika mtima mwa iwo okha, ndi kuti, Mafutawo atayidwa chifukwa ninji?
5 Pakuti mafuta amene akadagula marupiya atheka mazana atatu ndi mphamvu zake, ndi kupatsa aumphawi. Ndipo anadandaulira mkaziyo.
6 Koma Yesu anati, Mlekeni, mumvutiranji? Wandichitira Ine ntchito yabwino.
7 Pakuti muli nao aumphawi pamodzi ndi inu masiku onse, ndipo paliponse pamene mukafuna mukhoza kuwachitira zabwino; koma Ine simuli nane masiku onse.
8 Iye wachita chimene wakhoza; anandidzozeratu thupi langa ku kuikidwa m’manda.
9 Ndipo ndithu ndinena ndi inu, Ponse pamene padzalalikidwa Uthenga Wabwino kudziko lonse lapansi, ichinso chimene anachita mkazi uyu chidzanenedwa, chikhale chomkumbukira nacho.
Yudasi apangana ndi ansembe aakulu
10 Ndipo Yudasi Iskariote, ndiye mmodzi wa khumi ndi awiriwo, anachoka napita kwa ansembe aakulu, kuti akampereke Iye kwa iwo.
11 Ndipo pamene iwo anamva, anasekera, nalonjezana naye kuti adzampatsa ndalama. Ndipo iye anafunafuna pompereka Iye bwino.
Paska wotsiriza
12 Ndipo tsiku loyamba la mikate yopanda chotupitsa, pamene amapha Paska,ophunziraananena naye, Mufuna tinke kuti, tikakonze mkadyereko Paska?
13 Ndipo anatuma awiri a ophunzira ake, nanena nao, Lowani m’mzinda, ndipo adzakomana nanu munthu wakusenza mtsuko wa madzi; mumtsate iye;
14 ndipo kumene akalowako iye, munene naye mwini nyumba, Mphunzitsi anena, Chilikuti chipinda cha alendo changa, m’menemo ndikadye Paska ndi ophunzira anga?
15 Ndipo iye yekha adzakusonyezani chipinda chapamwamba chachikulu choyalamo ndi chokonzedwa; ndipo m’menemo mutikonzere.
16 Ndipo ophunzira anatuluka, nafika m’mzinda, napeza monga anati kwa iwo; ndipo anakonza Paska.
17 Ndipo pofika madzulo anadza Iye pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
18 Ndipo pamene anaseama iwo kudya, Yesu anati, Ndithu ndinena ndi inu, Mmodzi wa inu adzandipereka Ine, ndiye wakudya ndi Ine pamodzi.
19 Anayamba iwo kukhala ndi chisoni, ndi kunena naye mmodzimmodzi, kuti, Ndine kodi?
20 Ndipo anati kwa iwo, Mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndiye wakusunsa pamodzi ndi Ine m’mbale.
21 Pakuti Mwana wa Munthu amukadi, monga kwalembedwa za Iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.
Mgonero wa Ambuye
22 Ndipo pamene iwo analikudya, Iye anatenga mkate, ndipo pamene anadalitsa, ananyema, napereka kwa iwo, kuti, Tengani; thupi langa ndi ili.
23 Ndipo anatenga chikho, ndipo pamene adayamika, anapereka kwa iwo; ndipo iwo onse anamweramo.
24 Ndipo Iye anati kwa iwo, Ichi ndi mwazi wanga wachipangano, wothiridwa chifukwa cha anthu ambiri.
25 Ndithu ndinena nanu, Sindidzamwanso chipatso cha mpesa, kufikira tsiku lijalo, limene ndidzamwa icho chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.
26 Ndipo ataimba nyimbo, anatuluka, namuka kuphiri la Azitona.
Yesu achenjeza Petro
27 Ndipo Yesu ananena nao, Mudzakhumudwa nonsenu; pakuti kwalembedwa,
Ndidzakantha mbusa, ndi nkhosa zidzamwazika.
28 Komatu nditadzauka ndidzatsogolera inu ku Galileya.
29 Koma Petro ananena naye, Angakhale adzakhumudwa onse, komatu ine iai.
30 Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.
31 Koma iye analimbitsa mau chilimbitsire, kuti, Ngakhale ndidzafa nanu, sindidzakana Inu. Ndipo onsewo anatero.
Getsemani
32 Ndipo iwo anadza kumalo dzina lake Getsemani; ndipo ananena kwa ophunzira ake, Bakhalani pano, kufikira ndikapemphera.
33 Ndipo anatenga pamodzi ndi Iye Petro, ndi Yakobo, ndi Yohane, nayamba kudabwa kwambiri, ndi kusauka mtima ndithu.
34 Ndipo ananena nao, Moyo wanga uli wa chisoni chambiri, kufikira imfa. Bakhalani pano, nimundikire.
35 Ndipo Iye anapita m’tsogolo pang’ono, nagwa pansi, napemphera kuti ngati nkutheka nthawi imene impitirire.
36 Ndipo ananena,Abba, Atate, zinthu zonse zitheka ndi Inu; mundichotsere chikho ichi; komatu si chimene ndifuna Ine, koma chimene mufuna Inu.
37 Ndipo anadza nawapeza iwo ali m’tulo, nanena ndi Petro, Simoni, ugona kodi? Unalibe mphamvu yakudikira ora limodzi kodi?
38 Dikirani, pempherani, kuti mungalowe m’kuyesedwa; mzimutu uli wakufuna, koma thupi lili lolefuka.
39 Ndipo anachokanso, napemphera, nanena mau omwewo.
40 Ndipo anadzanso nawapeza ali m’tulo, pakuti maso ao analemeradi; ndipo sanadziwe chomyankha Iye.
41 Ndipo anadza kachitatu, nanena nao, Gonani tsopano, nimupumule; chakwanira; yafika nthawi; onani Mwana wa Munthu aperekedwa m’manja a anthu ochimwa.
42 Ukani, tizimuka; onani wakundiperekayo ali pafupi.
Amgwira Yesu
43 Ndipo pomwepo, Iye ali chilankhulire, anadza Yudasi, mmodzi wa khumi ndi awiriwo, ndipo pamodzi naye khamu la anthu, ali nao malupanga ndi mikunkhu, ochokera kwa ansembe aakulu ndi alembi ndi akulu.
44 Ndipo wakumpereka Iye anawapatsa chizindikiro, nanena, Iye amene ndidzampsompsona, ndiyetu; mgwireni munke naye chisungire.
45 Ndipo atafika, pomwepo anadza kwa Iye, nanena,Rabi; nampsompsonetsa.
46 Ndipo anamthira manja, namgwira.
47 Koma mmodzi wina wa iwo akuimirirapo, anasolola lupanga lake, nakantha kapolo wake wa mkulu wa ansembe, namdula khutu lake.
48 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iwo, Kodi mwatuluka ndi malupanga ndi mikunkhu kundigwira Ine monga wachifwamba?
49 Masiku onse ndinali nanu mu Kachisi ndilikuphunzitsa, ndipo simunandigwire Ine; koma ichi chachitika kuti malembo akwaniritsidwe.
50 Ndipo iwo onse anamsiya Iye, nathawa.
51 Ndipo mnyamata wina anamtsata Iye, atafundira pathupi nsalu yabafuta yokha; ndipo anamgwira;
52 koma iye anasiya nsaluyo, nathawa wamaliseche.
Yesu aweruzidwa ndi akulu a Ayuda
53 Ndipo ananka naye Yesu kwa mkulu wa ansembe; ndipo anasonkhana kwa iye ansembe aakulu onse ndi akulu a anthu, ndi alembi.
54 Ndipo Petro adamtsata Iye kutali, kufikira kulowa m’bwalo la mkulu wa ansembe; ndipo anali kukhala pansi pamodzi ndi anyamata, ndi kuotha moto.
55 Ndipo ansembe aakulu ndi akulu a milandu onse anafunafuna umboni wakutsutsa nao Yesu kuti amuphe Iye; koma sanaupeze.
56 Pakuti ambiri anamchitira umboni wonama, ndipo umboni wao sunalingane.
57 Ndipo ananyamukapo ena, namchitira umboni wakunama, nanena kuti,
58 Ife tinamva Iye alikunena, kuti, Ine ndidzaononga Kachisi uyu wopangidwa ndi manja, ndi masiku atatu ndidzamanga wina wosapangidwa ndi manja.
59 Ndipo ngakhale momwemo umboni wao sunalingane.
60 Ndipo mkulu wa ansembe ananyamuka pakati, namfunsa Yesu, nanena, Suyankha kanthu kodi? Nchiyani ichi chimene awa alikuchitira mboni?
61 Koma anakhala chete, osayankha kanthu. Mkulu wa ansembe anamfunsanso, nanena naye, Kodi Iwe ndiwe Khristu, Mwana wake wa Wolemekezeka?
62 Ndipo Yesu anati, Ndine amene; ndipo mudzaona Mwana wa Munthu alikukhala kudzanja lamanja la mphamvu, ndi kudza ndi mitambo ya kumwamba.
63 Ndipo mkulu wa ansembe anang’amba malaya ake, nanena, Tifuniranjinso mboni zina?
64 Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.
65 Ndipo ena anayamba kumthira malovu Iye, ndi kuphimba nkhope yake, ndi kumbwanyula, ndi kunena naye, Lota; ndipo anyamatawo anampanda Iye khofu.
Petro akana kuti sadziwa Yesu
66 Ndipo pamene Petro anali pansi m’bwalo, anadzapo mmodzi wa adzakazi a mkulu wa ansembe;
67 ndipo anaona Petro alikuotha moto, namyang’ana iye, nanena, Iwenso unali naye Mnazarene, Yesu.
68 Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira.
69 Ndipo anamuona mdzakaziyo, nayambanso kunena ndi iwo akuimirirapo, Uyu ngwa awo.
70 Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.
71 Koma iye anayamba kutemberera, ndi kulumbira, Sindimdziwa munthuyu mulikunena.
72 Ndipo pomwepo tambala analira kachiwiri. Ndipo Petro anakumbukira umo Yesu anati kwa iye, kuti, Tambala asanalire kawiri udzandikana katatu. Ndipo pakuganizira ichi analira misozi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/14-573e5591b496bf8172db623563b120c7.mp3?version_id=1068—