Categories
MARKO

MARKO 1

Yohane Mbatizi

1 Chiyambi chake cha Uthenga Wabwino wa YesuKhristu, Mwana wa Mulungu.

2 Monga mwalembedwa mu Yesayamneneri,

Ona, ndituma mthenga wanga patsogolo pa nkhope yanu,

amene adzakonza njira yanu.

3 Mau a wofuula m’chipululu,

konzani khwalala la Ambuye,

lungamitsani njira zake.

4 Yohane anadza nabatiza m’chipululu, nalalikira ubatizo wa kutembenuka mtima wakuloza ku chikhululukiro cha machimo.

5 Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a kuYerusalemuonse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.

6 Ndipo Yohane anavala ubweya wangamira, ndi lamba lachikopa m’chuuno mwake, nadya dzombe ndi uchi wakuthengo.

7 Ndipo analalikira, kuti, Wondipambana ine mphamvu akudza pambuyo panga, sindiyenera kuwerama kumasula zingwe za nsapato zake.

8 Ndakubatizani inu ndi madzi; koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.

Kubatizidwa ndi kuyesedwa kwa Yesu

9 Ndipo kunali masiku omwewo, Yesu anadza kuchokera ku Nazarete wa ku Galileya, nabatizidwa ndi Yohane mu Yordani.

10 Ndipo pomwepo, alimkukwera potuluka m’madzi, anaona Iye thambo litang’ambika, ndi Mzimu alikutsikira pa Iye monga nkhunda:

11 ndipo mau anatuluka m’thambo, Mwana wanga wokondedwa ndiwe, mwa Iwe ndikondwera bwino.

12 Ndipo pomwepo Mzimu anamkakamiza kunka kuchipululu.

13 Ndipo anakhala m’chipululu masiku makumi anai woyesedwa ndiSatana; nakhala ndi zilombo, ndipoangeloanamtumikira.

Yesu aitana ophunzira ake oyamba

14 Ndipo ataperekedwa Yohane, Yesu anadza ku Galileya, nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu,

15 nanena, Nthawi yakwanira, ndipo Ufumu wa Mulungu wayandikira; tembenukani mtima, khulupirirani Uthenga Wabwino.

16 Ndipo pakuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi Andrea, mbale wake wa Simoni, alinkuponya khoka m’nyanja; pakuti anali asodzi.

17 Ndipo Yesu ananena nao, Idzani pambuyo panga, ndipo ndidzakusandutsani inu asodzi a anthu.

18 Ndipo pomwepo anasiya makoka ao, namtsata Iye.

19 Ndipo atapita patsogolo pang’ono, anaona Yakobo, mwana wa Zebedeo, ndi Yohane mbale wake, iwonso anali m’chombo nakonza makoka ao.

20 Ndipo pomwepo anawaitana: ndipo anasiya atate wao Zebedeo m’chombomo pamodzi ndi antchito olembedwa, namtsata.

Achiritsidwa wogwidwa ndi chiwanda ku Kapernao

21 Ndipo iwo analowa mu Kapernao; ndipo pomwepo pa tsiku laSabataiye analowa m’sunagogenaphunzitsa.

22 Ndipo anazizwa ndi chiphunzitso chake; pakuti anaphunzitsa monga mwini mphamvu, si monga alembi.

23 Ndipo pomwepo panali munthu m’sunagoge mwao ali ndi mzimu wonyansa; ndipo anafuula iye.

24 Kuti, Tili ndi chiyani ife ndi Inu Yesu wa ku Nazarete? Kodi mwadza kudzationonga ife: Ndikudziwani, ndinu Woyerayo wa Mulungu.

25 Ndipo Yesu anaudzudzula, kuti, Khala uli chete, nutuluke mwa iye.

26 Ndipo mzimu wonyansa, pomng’amba, ndi kufuula ndi mau aakulu, unatuluka mwa iye.

27 Ndipo anazizwa onse, kotero kuti anafunsana mwa iwo okha, kuti, Ichi nchiyani? Chiphunzitso chatsopano! Ndi mphamvu alamula ingakhale mizimu yonyansa, ndipo imvera Iye.

28 Ndipo mbiri yake inabuka pompaja kudziko lonse la Galileya lozungulirapo.

Achiritsidwa mpongozi wa Petro ndi odwala ena

29 Ndipo pomwepo, potuluka m’sunagoge, iwo analowa m’nyumba ya Simoni ndi Andrea pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane.

30 Ndipo mpongozi wake wa Simoni anali gone wodwala malungo; ndipo pomwepo anamuuza za iye:

31 ndipo anadza namgwira dzanja, namuutsa; ndipo malungo anamleka, ndipo anawatumikira iwo.

32 Ndipo madzulo, litalowa dzuwa, anadza nao kwa Iye onse akudwala, ndi akugwidwa ndi ziwanda.

33 Ndipo mzinda wonse unasonkhana pakhomo.

34 Ndipo anachiritsa anthu ambiri akudwala nthenda za mitundumitundu, natulutsa ziwanda zambiri; ndipo sanalole ziwandazo zilankhule, chifukwa zinamdziwa Iye.

35 Ndipo m’mawa mwake anauka usikusiku, natuluka namuka kuchipululu, napemphera kumeneko.

36 Ndipo Simoni ndi anzake anali naye anamtsata,

37 nampeza, nanena naye, Akufunani Inu anthu onse.

38 Ndipo ananena nao, Tiyeni kwina, kumidzi ili pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imeneyi.

39 Ndipo analowa m’masunagoge mwao mu Galileya monse, nalalikira, natulutsa ziwanda.

Yesu achiritsa wakhate

40 Ndipo anadza kwa Iye wodwalakhate, nampempha Iye, namgwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza.

41 Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.

42 Ndipo pomwepo khate linamchoka, ndipo anakonzedwa.

43 Ndipo anamuuzitsa, namtulutsa pomwepo,

44 nanena naye, Ona, usati unene kanthu kwa munthu aliyense: koma muka, ukadzionetse kwa wansembe, nupereke pa makonzedwe ako zimene adalamulira Mose, zikhale mboni kwa iwo.

45 Koma iye anatuluka nayamba kulalikira ndithu, ndi kubukitsa mauwo, kotero kuti Yesu sanathe kulowanso poyera m’mudzi, koma anakhala padera m’mapululu; ndipo anadza kwa Iye anthu a kumalo onse.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MRK/1-cf352c2d6b715dfd62ddd3f707f6522f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *