Categories
MALAKI

MALAKI 3

Za mthenga wokonzeratu njira ya Ambuye

1 Taonani, ndituma mthenga wanga, kuti akonzeretu njira pamaso panga; ndipo Ambuye amene mumfuna adzadza ku Kachisi wake modzidzimutsa; ndiye mthenga wachipanganoamene mukondwera naye; taonani akudza, ati Yehova wa makamu.

2 Koma ndani adzapirira tsiku la kudza kwake? Ndipo adzaima ndani pooneka Iye? Pakuti adzanga moto wa woyenga, ndi sopo wa otsuka;

3 ndipo adzakhala pansi ndi kuyenga ndi kuyeretsasiliva, nadzayeretsa ana a Levi, nadzawayengetsa ngati golide ndi siliva; pamenepo iwo adzapereka kwa Yehova zopereka m’chilungamo.

4 Pamenepo chopereka cha Yuda ndiYerusalemuchidzakomera Yehova, ngati masiku a kale lija, ndi ngati zaka zoyamba zija.

5 Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.

6 Pakuti Ine Yehova sindisinthika, chifukwa chake inu ana a Yakobo simunathedwe.

Za kusalanda za Mulungu ndi madalitso atsatapo

7 Kuyambira masiku a makolo anu mwapatuka kuleka malemba anga osawasunga. Bwererani kudza kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu, ati Yehova wa makamu. Koma inu mukuti, Tibwerere motani?

8 Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka.

9 Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

10 Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m’nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

11 Ndipo ndidzadzudzula zolusa chifukwa cha inu, kuti zisakuonongereni zipatso za nthaka yanu; ngakhale mpesa wanu sudzayoyoka zipatso zake, zosacha m’munda, ati Yehova wa makamu.

12 Ndipoamitunduonse adzatcha inu odala; pakuti mudzakhala dziko lokondweretsa, ati Yehova wa makamu.

13 Mau anu andilimbira, ati Yehova. Koma inu mukuti, Tanena motsutsana nanu ndi chiyani?

14 Mwanena, Kutumikira Mulungu nkwa chabe; ndipo tapindulanji ndi kusunga udikiro wake, ndi kuyenda ovala zamaliro pamaso pa Yehova wa makamu?

15 Ndipo tsopano tiwatcha odzikuza odala, inde iwo ochita zoipa amangidwa ngati nyumba; inde, ayesa Mulungu, napulumuka.

16 Pamenepo iwo akuopa Yehova analankhulana wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchera khutu namva, ndi buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuopa Yehova, nakumbukira dzina lake.

17 Ndipo adzakhala angaanga, ati Yehova wa makamu, tsiku ndidzaikalo, ndipo ndidzawaleka monga munthu aleka mwana wake womtumikira.

18 Pamenepo mudzabwera ndi kuzindikira pakati pa wolungama ndi woipa, pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosamtumikira.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/3-789b8f3961efcb83707bd67ef5b71b72.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *