Kusayamika kwa Israele pa chikondi cha Mulungu
1 Katundu wa mau a Yehova wa kwa Israele mwa Malaki.
2 Ndakukondani, ati Yehova; koma inu mukuti, Mwatikonda motani? Esau si mkulu wake wa Yakobo kodi? Ati Yehova; ndipo ndinakonda Yakobo;
3 koma Esau ndinamuda, ndinasanduliza mapiri ake abwinja, ndi kupereka cholowa chake kwa ankhandwe a m’chipululu.
4 Chinkana Edomu akuti, Taphwanyika, koma tidzabwera ndi kumanganso mabwinja; atero Yehova wa makamu, Adzamanga, koma Ine ndidzapasula; ndipo adzawatcha, Dziko la choipa, ndiponso, Anthu amene Yehova akwiya nao chikwiyire.
5 Ndipo maso anu adzaona, nimudzati, Yehova ali wamkulu kupitirira malire a Israele.
6 Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani?
7 Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M’menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.
8 Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.
9 Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.
10 Mwenzi atakhala wina mwa inu wakutseka pamakomo, kuti musasonkhe moto chabe paguwa langa la nsembe! Sindikondwera nanu, ati Yehova wa makamu, ndipo sindidzalandira chopereka m’dzanja lanu.
11 Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwaamitundu; ndipo m’malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.
12 Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.
13 Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova.
14 Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m’gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/MAL/1-5411abd1b38cae2bed800f0e3693a448.mp3?version_id=1068—