Za Ananiya ndi Safira
1 Koma munthu wina dzina lake Ananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake,
2 anagulitsa chao, napatula pa mtengo wake, mkazi yemwe anadziwa, natenga chotsala, nachiika pa mapazi aatumwi.
3 Koma Petro anati, Ananiya,Satanaanadzaza mtima wako chifukwa ninji kudzanyenga Mzimu Woyera, ndi kupatula pa mtengo wake wa mundawo?
4 Pamene unali nao, sunali wako kodi? Ndipo pamene unagulitsa sunali m’manja mwako kodi? Bwanji chinalowa ichi mumtima mwako? Sunanyenga anthu, komatu Mulungu.
5 Koma Ananiya pakumva mau awa anagwa pansi namwalira: ndipo mantha aakulu anagwera onse akumvawo.
6 Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika.
7 Koma atapita monga maora atatu, ndipo mkazi wake, wosadziwa chidachitikacho, analowa.
8 Ndipo Petro ananena naye, Undiuze, ngati munagulitsa mundawo pa mtengo wakuti. Ndipo ananena, Inde, wakuti.
9 Koma Petro anati kwa iye, Munapangana pamodzi bwanji kuyesa Mzimu wa Ambuye? Taona, mapazi ao a iwo amene anaika mwamuna wako ali pakhomo, ndipo adzakunyamula kutuluka nawe.
10 Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.
11 Ndipo anadza mantha aakulu paMpingowonse, ndi pa onse akumva izi.
12 Ndipo mwa manja a atumwi zizindikiro ndi zozizwa zambiri zinachitidwa pa anthu; ndipo anali onse ndi mtima umodzi m’khonde la Solomoni.
13 Koma palibe mmodzi wa otsalawo analimba mtima kuphatikana nao; komatu anthu anawakuzitsa;
14 ndipo makamaka anaonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi;
15 kotero kuti ananyamulanso natuluka nao odwala kumakwalala, nawaika pamakama ndi pamphasa, kuti, popita Petro, ngakhale chithunzi chake chigwere wina wa iwo.
16 Komanso unasonkhana pamodzi unyinji wa anthu ochokera kumidzi yozunguliraYerusalemu, alikutenga odwala, ndi ovutika ndi mizimu yonyansa; ndipo anachiritsidwa onsewa.
Atumwi apulumutsidwa m’ndende, natengedwanso kupita nao kubwalo la akulu
17 Koma anauka mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, ndiwo a chipatuko chaAsaduki, nadukidwa,
18 nathira manja atumwi, nawaika m’ndende ya anthu wamba.
19 Komamngelowa Ambuye anatsegula pakhomo pa ndende usiku, nawatulutsa, nati,
20 Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.
21 Ndipo atamva ichi, analowa mu Kachisi mbandakucha, naphunzitsa. Koma anadza mkulu wa ansembe ndi iwo amene anali naye, nasonkhanitsa abwalo la akulu a milandu, ndi akulu onse a ana a Israele, natuma kundende atengedwe ajawo.
22 Koma anyamata amene adafikako sanawapeze m’ndende, ndipo pobwera anafotokoza,
23 nanena, Nyumba yandende tinapeza chitsekere, ndi alonda alikuimirira pamakomo; koma pamene tinatsegula sitinapezamo mmodzi yense.
24 Koma m’mene anamva mau awa mdindo wa Kachisi ndi ansembe aakulu anathedwa nzeru ndi iwo aja, kuti ichi chidzatani.
25 Ndipo anadza wina nawafotokozera, kuti, Taonani, amuna aja mudawaika m’ndende ali mu Kachisi, alikuimirira ndi kuphunzitsa anthu.
26 Pamenepo anachoka mdindo pamodzi ndi anyamata; anadza nao, koma osawagwiritsa, pakuti anaopa anthu, angaponyedwe miyala.
27 Ndipo m’mene adadza nao, anawaika pabwalo la akulu a milandu. Ndipo anawafunsa mkulu wa ansembe,
28 nanena, Tidakulamulirani chilamulire, musaphunzitsa kutchula dzina ili; ndipo taonani, mwadzaza Yerusalemu ndi chiphunzitso chanu, ndipo mufuna kutidzetsera ife mwazi wa munthu uja.
29 Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.
30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene munamupha inu, ndi kumpachika pamtengo.
31 Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.
32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu izi; Mzimu Woyeranso, amene Mulungu anapatsa kwa iwo akumvera Iye.
33 Koma m’mene anamva iwo analaswa mtima, nafuna kuwapha.
34 Koma ananyamukapo wina pabwalo la akulu a milandu, ndiyeMfarisi, dzina lake Gamaliele, mphunzitsi wa malamulo, wochitidwa ulemu ndi anthu onse, nalamula kuti atumwiwo akhale kunja pang’ono.
35 Ndipo anati kwa iwo, Amuna inu a Israele, kadzichenjerani nokha za anthu awa, chimene muti muwachitire.
36 Pakuti asanafike masiku ano anauka Teudasi, nanena kuti ali kanthu iye mwini; amene anthu anaphatikana naye, chiwerengero chao ngati mazana anai; ndiye anaphedwa; ndi onse amene anamvera iye anamwazika, napita pachabe.
37 Atapita ameneyo, anauka Yudasi wa ku Galileya, masiku a kalembera, nakopa anthu amtsate. Iyeyunso anaonongeka, ndi onse amene anamvera iye anabalalitsidwa.
38 Ndipo tsopano ndinena ndi inu, Lekani anthu amenewa, nimuwalole akhale; pakuti ngati uphungu umene kapena ntchito iyi ichokera kwa anthu, idzapasuka;
39 koma ngati ichokera kwa Mulungu simungathe kuwapasula; kuti kapena mungapezeke otsutsana ndi Mulungu.
40 Ndipo anavomerezana ndi iye; ndipo m’mene adaitana atumwi, anawakwapula nawalamulira asalankhule kutchula dzina la Yesu, ndipo anawamasula.
41 Pamenepo ndipo anapita kuchokera kubwalo la akulu a milandu, nakondwera kuti anayesedwa oyenera kunyozedwa chifukwa cha dzinalo.
42 Ndipo masiku onse, mu Kachisi ndi m’nyumba, sanaleke kuphunzitsa ndi kulalikiraKhristuYesu.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/5-66f69414f814cb0f3eebc1e508cbb28c.mp3?version_id=1068—