Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 28

Paulo pa Melita

1 Ndipo titapulumuka, pamenepo tinadziwa kuti chisumbucho chinatchedwa Melita.

2 Ndipo akunja anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.

3 Koma pamene Paulo adaola chisakata cha nkhuni, nachiika pamoto, inatulukamo njoka, chifukwa cha kutenthaku, niluma dzanja lake.

4 Koma pamene akunjawo anaona chilombocho chili lende padzanja lake, ananena wina ndi mnzake, Zoona munthuyu ndiye wambanda. Angakhale anapulumuka m’nyanja, chilungamo sichimlola akhale ndi moyo.

5 Koma anakutumulira chilombocho kumoto, osamva kupweteka.

6 Koma anayesa kuti adzatupa, kapena mwini wake kugwa kufa pomwepo; koma m’mene adalindira nthawitu, naona kuti sanapweteke konse, anasintha maganizo, nati, Ndiye Mulungu.

7 Koma pafupi pamenepo panali minda, mwini wake ndiye mkulu chisumbucho, dzina lake Publio; amene anatilandira ife, natichereza okoma masiku atatu.

8 Ndipo kunatero kuti atate wake wa Publioyo anagona wodwala nthenda ya malungo ndi kamwazi. Kwa iyeyu Paulo analowa, napemphera, naika manja pa iye, namchiritsa.

9 Ndipo patachitika ichi, enanso a m’chisumbu, okhala nazo nthenda, anadza, nachiritsidwa;

10 amenenso anatichitira ulemu wambiri; ndipo pochoka ife anatiikira zotisowa.

Paulo afika ku Roma, nakhala wandende m’nyumba ya iye yekha zaka ziwiri

11 Ndipo itapita miyezi itatu tinayenda m’ngalawa ya ku Aleksandriya, idagonera nyengo ya chisanu kuchisumbuko, chizindikiro chake, Ana Amapasa.

12 Ndipo pamene tinakocheza ku Sirakusa, tinatsotsako masiku atatu.

13 Ndipo pochokapo tinapaza ntifika ku Regio; ndipo litapita tsiku limodzi unayamba mwera, ndipo m’mawa mwake tinafika ku Puteoli:

14 pamenepo tinakomana ndi abale, amene anatiumirira tikhale nao masiku asanu ndi awiri; ndipo potero tinafika ku Roma.

15 Kuchokera kumeneko abalewo, pakumva za ife, anadza kukomana nafe ku Bwalo la Apio, ndi ku Nyumba za Alendo Zitatu; ndipo pamene Paulo anawaona, anayamika Mulungu, nalimbika mtima.

16 Ndipo pamene tinalowa mu Roma, analola Paulo akhale pa yekha ndi msilikali womdikira iye.

17 Ndipo kunali, atapita masiku atatu, anaitana akulu a Ayuda asonkhane; ndipo atasonkhana, ananena nao, Ine, amuna, abale, ndingakhale sindinachite kanthu kakuipsa anthu, kapena miyambo ya makolo, anandipereka wam’nsinga kuchokera kuYerusalemuku manja a Aroma;

18 ndiwo, atandifunsafunsa ine anafuna kundimasula, popeza panalibe chifukwa cha kundiphera.

19 Koma pakukanapo Ayuda, ndinafulumidwa mtima kutulukira kwaKaisara; si kunena kuti ndinali nako kanthu kakunenera mtundu wanga.

20 Chifukwa cha ichi tsono ndinakupemphani inu mundione ndi kulankhula nane; pakuti chifukwa cha chiyembekezo cha Israele ndamangidwa ndi unyolo uwu.

21 Ndipo anati kwa iye, Ife sitinalandire makalata onena za inu ochokera ku Yudeya, kapena sanadze kuno wina wa abale ndi kutiuza kapena kulankhula kanthu koipa ka inu.

22 Koma tifuna kumva mutiuze muganiza chiyani; pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponseponse.

23 Ndipo pamene adampangira tsiku, anadza kunyumba yake anthu ambiri; amenewo anawafotokozera, ndi kuchitira umboni Ufumu wa Mulungu, ndi kuwakopa za Yesu, zochokera m’chilamulo cha Mose ndi mwa aneneri, kuyambira mamawa kufikira madzulo.

24 Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere.

25 Koma popeza sanavomerezane, anachoka atanena Paulo mau amodzi, kuti, Mzimu Woyera analankhula kokoma mwa YesayaMnenerikwa makolo anu,

26 ndi kuti,

Pita kwa anthu awa, nuti,

Ndi kumva mudzamva, ndipo simudzazindikira konse;

ndipo pakupenya mudzapenya, koma osaona konse;

27 pakuti mtima wa anthu awa watupatu,

ndipo m’makutu mwao mmolema kumva,

ndipo maso ao anawatseka;

kuti angaone ndi maso,

nangamve ndi makutu,

nangazindikire ndi mtima,

nangatembenuke,

ndipo Ine ndingawachiritse.

28 Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwaamitundu; iwonso adzamva.

30 Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m’nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye,

31 ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye YesuKhristundi kulimbika konse, wosamletsa munthu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/28-3811151ec2daa4795f028ad84138f818.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *