Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 23

1 Ndipo Paulo, popenyetsetsa a m’bwalo la akulu a milanduanati, Amuna, abale, ndakhala ine pamaso pa Mulungu ndi chikumbumtima chokoma chonse kufikira lero lomwe.

2 Ndipo mkulu wa ansembe Ananiya analamulira akuimirirako ampande pakamwa pake.

3 Pamenepo Paulo anati kwa iye, Mulungu adzakupanda iwe, khoma loyeretsedwa iwe; ndipo kodi ukhala iwe wakundiweruza mlandu monga mwa chilamulo, ndipo ulamulira andipande ine posanga chilamulo?

4 Ndipo iwo akuimirirako anati, Ulalatira kodi mkulu wa ansembe wa Mulungu?

5 Ndipo Paulo anati, Sindinadziwe, abale, kuti ndiye mkulu wa ansembe; pakuti kwalembedwa, Usamnenera choipa mkulu wa anthu ako.

6 Koma pozindikira Paulo kuti ena ndiAsaduki, ndi enaAfarisi, anafuula m’bwalomo, Amuna, abale, ine ndine Mfarisi, mwana wa Afarisi: andinenera mlandu wa chiyembekezo ndi kuuka kwa akufa.

7 Ndipo pamene adatero, kunakhala chilekano pakati pa Afarisi ndi Asaduki; ndipo osonkhanawo anagawikana.

8 Pakutitu Asaduki anena kuti kulibe kuuka kwa akufa, kapenamngelo, kapena mzimu; koma Afarisi avomereza ponse pawiri.

9 Ndipo chidauka chipolowe chachikulu, ndipo alembi ena a kwa Afarisi anaimirira, natsutsana, nanena, Sitipeza choipa chilichonse mwa munthuyu; ndipo nanga bwanji ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye?

10 Ndipo pamene padauka chipolowe chachikulu, kapitao wamkulu anaopa kuti angamkadzule Paulo, ndipo analamulira asilikali atsike, namkwatule pakati pao, nadze naye kulowa naye m’linga.

11 Ndipo usiku wake Ambuye anaimirira pa iye, nati, Limbika mtima; pakuti monga wandichitira umboni kuYerusalemu, koteronso uyenera kundichitira umboni ku Roma.

Ayuda apangana chiwembu cha kupha Paulo. Apulumukira ku Kesareya

12 Ndipo kutacha, Ayuda anapangana chiwembu, nadzitemberera, ndi kunena kuti sadzadya kapena kumwa kanthu, kufikira atamupha Paulo;

13 ndipo iwo amene adachita chilumbiro ichi anali oposa makumi anai.

14 Amenewo anadza kwa ansembe aakulu ndi akulu, nati, Tadzitemberera nalo temberero kuti sitidzalawa kanthu kufikira titamupha Paulo.

15 Potero tsopano inu ndi bwalo la akulu a milandu muzindikiritse kapitao wamkulu kuti atsike naye kwa inu, monga ngati mufuna kudziwitsitsa bwino za iye; koma tadzikonzeratu timuphe asanayandikire iye.

16 Koma mwana wa mlongo wake wa Paulo anamva za chifwamba chao, ndipo anadza nalowa m’linga, namfotokozera Paulo.

17 Ndipo Paulo anadziitanirakenturiyowina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.

18 Pamenepo ndipo anamtenga, napita naye kwa kapitao wamkulu, nati, Wam’nsingayo Paulo anandiitana, nandipempha ndidze naye mnyamata uyu kwa inu, ali nako kanthu kakulankhula ndi inu.

19 Ndipo kapitao wamkulu anamgwira dzanja, napita naye padera, namfunsa m’tseri, Chiyani ichi uli nacho kundifotokozera?

20 Ndipo anati, Ayuda anapangana kuti akufunseni mutsike naye Paulo mawa kubwalo la akulu a milandu, monga ngati mufuna kufunsitsa za iye.

21 Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang’anira lonjezano lanu.

22 Pamenepo ndipo kapitao wamkulu anauza mnyamatayo apite, namlamulira kuti, Usauze munthu yense kuti wandizindikiritsa izi.

23 Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;

24 ndiponso mukonzeretu nyama zobereka amkwezepo Paulo, nampereke wosungika kwa Felikisi kazembeyo.

25 Ndipo analembera kalata yakuti,

26 Klaudio Lisiasi kwa kazembe womveketsa Felikisi, ndikupatsani moni.

27 Munthu uyu anagwiridwa ndi Ayuda, ndipo akadaphedwa ndi iwo; pamenepo ndinafikako ine ndi asilikali, ndipo ndinamlanditsa pakumva kuti ndiye Mroma.

28 Ndipo pofuna kuzindikira chifukwa chakuti anamnenera iye, ndinatsikira naye kubwalo lao la akulu a milandu.

29 Ndipo ndinapeza kuti adamnenera za mafunso a chilamulo chao; koma analibe kumnenera kanthu kakuyenera imfa kapena nsinga.

30 Ndipo m’mene anandidziwitsa kuti pali chiwembu cha pa munthuyu, pomwepo ndinamtumiza kwa inu; ndipo ndalamulira akumnenera akamnenere kwa inu.

31 Pamenepo ndipo asilikali, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.

32 Koma m’mawa mwake anasiya apakavalo amperekeze, nabwera kulinga;

33 iwowo, m’mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.

34 Ndipo m’mene adawerenga anafunsa achokera m’dziko liti; ndipo pozindikira kuti anali wa ku Silisiya,

35 anati, Ndidzamva mlandu wako, pamene akukunenera afika. Ndipo analamulira kuti amdikire iye m’nyumba ya milandu yaHerode.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/23-568074d4eaa1e3d0ebcd7ef8fa118d2c.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *