Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 22

Paulo achita chodzikanira chake kwa anthu

1 Amuna, abale, ndi atate, mverani chodzikanira changa tsopano, cha kwa inu.

2 Ndipo pakumva kuti analankhula nao m’chinenedwe cha Chihebri, anaposa kukhala chete; ndipo anati,

3 Ine ndine munthu Myuda, wobadwa mu Tariso wa Silisiya, koma ndaleredwa m’mzinda muno, pa mapazi a Gamaliele, wolangizidwa monga mwa chitsatidwe chenicheni cha chilamulo cha makolo athu, ndipo ndinali wachangu, cholinga kwa Mulungu, monga muli inu nonse lero;

4 ndipo ndinalondalonda Njira iyi kufikira imfa, ndi kumanga ndi kupereka kundende amuna ndi akazi.

5 Monganso mkulu wa ansembe andichitira umboni, ndi bwalo lonse la akulu; kwa iwo amenenso ndinalandira makalata kunka nao kwa abale, ndipo ndinapita ku Damasiko, kuti ndikatenge iwonso akukhala kumeneko kudza nao omangidwa kuYerusalemu, kuti alangidwe.

6 Ndipo kunali, pakupita ine ndi kuyandikira ku Damasiko, monga usana, mwadzidzidzi kunandiwalira pondizungulira ine kuunika kwakukulu kochokera kumwamba.

7 Ndipo ndinagwa pansitu, ndipo ndinamva mau akunena nane, Saulo, Saulo, undilondalonderanji Ine?

8 Ndipo ndinayankha, Ndinu yani Mbuye? Ndipo anati kwa ine, Ndine Yesu wa ku Nazarete, amene umlondalonda.

9 Ndipo iwo akukhala nane anaonadi kuunika, koma sanamve mau akulankhula nane.

10 Ndipo ndinati, Ndidzachita chiyani, Ambuye? Ndipo Ambuye anati kwa ine, Tauka, pita ku Damasiko; kumeneko adzakufotokozera zonse zoikika kwa iwe uzichite.

11 Ndipo popeza sindinapenye, chifukwa cha ulemerero wa kuunikako, anandigwira dzanja iwo amene anali ndi ine, ndipo ndinafika ku Damasiko.

12 Ndipo munthu dzina lake Ananiya, ndiye munthu wopembedza monga mwa chilamulo, amene amchitira umboni wabwino Ayuda onse akukhalako,

13 anadza kwa ine, ndipo poimirirapo anati kwa ine, Saulo, mbale, penyanso. Ndipo ine, ora lomweli ndinampenya.

14 Ndipo anati, Mulungu wa makolo athu anakusankhiratu udziwe chifuniro chake, nuone Wolungamayo, numve mau otuluka m’kamwa mwake.

15 Ndipo udzamkhalira Iye mboni kwa anthu onse, za izo udaziona ndi kuzimva.

16 Ndipo tsopano uchedweranji? Tauka, nubatizidwe ndi kusamba kuchotsa machimo ako, nuitane pa dzina lake.

17 Ndipo kunali, nditabwera ku Yerusalemu ndinalikupemphera mu Kachisi, ndinachita ngati kukomoka,

18 ndipo ndinamuona Iye, nanena nane, Fulumira, tuluka msanga mu Yerusalemu; popeza sadzalandira umboni wako wakunena za Ine.

19 Ndipo ndinati ine, Ambuye, adziwa iwo okha kuti ndinali kuika m’ndende ndi kuwapanda m’masunagogeonse iwo akukhulupirira Inu;

20 ndipo pamene anakhetsa mwazi wa Stefano mboni yanu, ine ndemwe ndinalikuimirirako, ndi kuvomerezana nao, ndi kusunga zovala za iwo amene anamupha iye.

21 Ndipo anati kwa ine, Pita; chifukwa Ine ndidzakutuma iwe kunka kutali kwaamitundu.

22 Ndipo adamumva kufikira mau awa; ndipo anakweza mau ao nanena, Achoke padziko lapansi munthu wotere; pakuti sayenera iye kukhala ndi moyo.

23 Ndipo pakufuula iwo, ndi kutaya zovala zao, ndi kuwaza fumbi mumlengalenga,

24 kapitao wamkulu analamulira kuti amtenge iye kulowa naye kulinga, nati amfunsefunse ndi kumkwapula, kuti adziwe chifukwa chake nchiyani kuti amfuulira chomwecho.

25 Ndipo m’mene anammanga iye ndi nsingazo, Paulo anati kwakenturiyowakuimirirako, Kodi nkuloleka kwa inu kukwapula munthu Mroma, mlandu wake wosamveka?

26 Ndipo pakumva ichi kenturiyoyo, ananka kwa kapitao wamkulu, namuuza, nanena, Nchiyani ichi uti uchite? Pakuti munthuyo ndiye Mroma.

27 Ndipo kapitao wamkuluyo anadza, nati kwa iye, Ndiuze, iwe ndiwe Mroma kodi? Ndipo anati, Inde.

28 Ndipo kapitao wamkulu anayankha, Ine ndalandira ufulu umene ndi kuperekapo mtengo wake waukulu. Ndipo Paulo anati, Koma ine ndabadwa Mroma.

29 Pamenepo ndipo iwo amene anati amfunsefunse, anamsiya; ndipo kapitao wamkulunso anaopa, pozindikira kuti ndiye Mroma, ndiponso popeza adammanga iye.

Paulo pa bwalo la akulu

30 Koma m’mawa mwake pofuna kuzindikira chifukwa chake chenicheni chakuti anamnenera Ayuda, anammasula iye, nalamulira asonkhane ansembe aakulu, ndi bwalo lonse la akulu a milandu, ndipo anatsika naye Paulo, namuika pamaso pao.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/22-704f7465cd64b43aa563953d43cc3a5b.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *