Tsiku la Pentekoste
1 Ndipo pakufika tsiku laPentekoste, anali onse pamodzi pamalo amodzi.
2 Ndipo mwadzidzidzi anamveka mau ochokera Kumwamba ngati mkokomo wa mphepo yolimba, nadzaza nyumba yonse imene analikukhalamo.
3 Ndipo anaonekera kwa iwo malilime ogawanikana, onga amoto; ndipo unakhala pa iwo onse wayekhawayekha.
4 Ndipo anadzazidwa onse ndi Mzimu Woyera, nayamba kulankhula ndi malilime ena, monga Mzimu anawalankhulitsa.
5 Koma anali muYerusalemuokhalako Ayuda, amuna opembedza, ochokera kumtundu uliwonse pansi pa thambo.
6 Koma pochitika mau awa, unyinji wa anthu unasonkhana, nusokonezedwa, popeza yense anawamva alikulankhula m’chilankhulidwe chake cha iye yekha.
7 Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?
8 Ndipo nanga ife timva bwanji, yense m’chilankhulidwe chathu chimene tinabadwa nacho?
9 Aparti ndi Amedi, ndi Aelamu, ndi iwo akukhala mu Mesopotamiya, mu Yudeya, ndiponso mu Kapadokiya, mu Ponto, ndi mu Asiya;
10 mu Frijiya, ndiponso mu Pamfiliya, mu Ejipito, ndi mbali za Libiya wa ku Kirene, ndi alendo ochokera ku Roma,
11 ndiwo Ayuda, ndiponso opinduka, Akrete, ndi Aarabu, tiwamva iwo alikulankhula m’malilime athu zazikulu za Mulungu.
12 Ndipo anadabwa onse, nathedwa nzeru, nanena wina ndi mnzake, Kodi ichi nchiyani?
13 Koma ena anawaseka, nanena kuti, Akhuta vinyo walero.
Chodzikanira cha Petro
14 Koma Petro, anaimirira pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo, nakweza mau ake, nanena kwa iwo, nati, Amuna inu Ayuda, ndi inu nonse akukhala kwanu mu Yerusalemu, ichi chizindikirike kwa inu, ndipo tcherani khutu mau anga.
15 Pakuti awa sanaledzere monga muyesa inu; pakuti ndi ora lachitatu lokha la tsiku;
16 komatu ichi ndi chimene chinanenedwa ndimneneriYowele,
17 Ndipo kudzali m’masiku otsiriza, anena Mulungu,
ndidzathira cha Mzimu wanga pa thupi lililonse,
ndipo ana anu aamuna, ndi aakazi adzanenera,
ndipo anyamata anu adzaona masomphenya,
ndi akulu anu adzalota maloto;
18 ndiponso pa akapolo anga ndi pa adzakazi anga m’masiku awa
ndidzathira cha Mzimu wanga; ndipo adzanenera.
19 Ndipo ndidzapatsa zodabwitsa m’thambo la kumwamba,
ndi zizindikiro padziko lapansi;
mwazi, ndi moto, ndi mpweya wa utsi;
20 dzuwa lidzasanduka mdima,
ndi mwezi udzasanduka mwazi,
lisanadze tsiku la Ambuye,
lalikulu ndi loonekera.
21 Ndipo kudzali, kuti yense amene akaitana
pa dzina la Ambuye adzapulumutsidwa.
22 Amuna inu Aisraele, mverani mau awa: Yesu Mnazarayo, mwamuna wochokera kwa Mulungu, wosonyezedwa kwa inu ndi zimphamvu, ndi zozizwa, ndi zizindikiro, zimene Mulungu anazichita mwa Iye pakati pa inu monga mudziwa nokha;
23 ameneyo, woperekedwa ndi uphungu woikidwa ndi kudziwiratu kwa Mulungu, inu mwampachika ndi kumupha ndi manja a anthu osaweruzika;
24 yemweyo Mulungu anamuukitsa, atamasula zowawa za imfa, mwakuti sikunali kotheka kuti Iye agwidwe nayo.
25 Pakuti Davide anena za Iye,
Ndinaona Mbuye pamaso panga nthawi zonse;
chifukwa ali padzanja langa lamanja, kuti ndingasinthike;
26 mwa ichi unakondwera mtima wanga,
ndipo linasangalala lilime langa;
ndipo thupi langanso lidzakhala m’chiyembekezo.
27 Pakuti simudzasiya moyo wanga ku dziko la akufa,
kapena simudzapereka Woyera wanu aone chivunde,
28 munandidziwitsa ine njira za moyo;
mudzandidzaza ndi kukondwera pamaso panu.
29 Amuna inu, abale, kuloleka kunena poyera posaopa kwa inu za kholo lija Davide, kuti adamwalira naikidwanso, ndipo manda ake ali ndi ife kufikira lero lino.
30 Potero, pokhala mneneri iye, ndi kudziwa kuti ndi lumbiro anamlumbirira Mulungu, kuti mwa chipatso cha m’chuuno mwake adzakhazika wina pa mpando wachifumu wake;
31 iye pakuona ichi kale, analankhula za kuuka kwaKhristu, kuti sanasiyidwe m’dziko la akufa, ndipo thupi lake silinaone chivunde.
32 Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa; za ichi tili mboni ife tonse.
33 Potero, popeza anakwezedwa ndi dzanja lamanja la Mulungu, nalandira kwa Atate lonjezano la Mzimu Woyera, anatsanulira ichi, chimene inu mupenya nimumva.
34 Pakuti Davide sanakwere Kumwamba ai; koma anena yekha,
Ambuye anati kwa Mbuye wanga,
khalani kudzanja lamanja langa,
35 kufikira ndikaike adani ako chopondapo mapazi ako.
36 Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israele, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Khristu, Yesu amene inu munampachika.
Otembenuka mtima oyamba
37 Koma pamene anamva ichi, analaswa mtima, natitu kwa Petro ndiatumwienawo, Tidzachita chiyani, amuna inu, abale?
38 Koma Petro anati kwa iwo, Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Khristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo anu; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera.
39 Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.
40 Ndipo ndi mau ena ambiri anachita umboni, nawadandaulira iwo, nanena, Mudzipulumutse kwa mbadwo uno wokhotakhota.
41 Pamenepo iwo amene analandira mau ake anabatizidwa; ndipo anaonjezedwa tsiku lomwelo anthu ngati zikwi zitatu.
42 Ndipo anali chikhalire m’chiphunzitso cha atumwi ndi m’chiyanjano, m’kunyema mkate ndi mapemphero.
43 Koma panadza mantha pa anthu onse; ndipo zozizwa ndi zizindikiro zambiri zinachitika ndi atumwi.
44 Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana.
45 Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.
46 Ndipo tsiku ndi tsiku anali chikhalire ndi mtima umodzi mu Kachisi, ndipo ananyema mkate kunyumba kwao, nalandira chakudya ndi msangalalo, ndi mtima woona;
47 nalemekeza Mulungu, ndi kukhala nacho chisomo ndi anthu onse. Ndipo Ambuye anawaonjezera tsiku ndi tsiku amene akuti apulumutsidwe.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/2-17a32e370ecf310f60447aa5b70a4ee1.mp3?version_id=1068—