1 Ndipo anafikanso ku Deribe ndi Listara; ndipo taonani, panali wophunzirawina pamenepo, dzina lake Timoteo, amake ndiye Myuda wokhulupirira; koma atate wake ndiye Mgriki.
2 Ameneyo anamchitira umboni wabwino abale a ku Listara ndi Ikonio.
3 Iyeyo Paulo anafuna kuti amuke naye, ndipo anamtenga, namdula, chifukwa cha Ayuda amene anakhala m’maikomo; pakuti onse anadziwa kuti atate wake anali Mgriki.
4 Pamene anapita kupyola pamizinda, anapereka kwa iwo malamulo awasunge, amene analamuliraatumwindi akulu a paYerusalemu.
5 KoteroMipingoyo inalimbikitsidwa m’chikhulupiriro, nachuluka m’chiwerengo chao tsiku ndi tsiku.
6 Ndipo anapita padziko la Frijiya ndi Galatiya, atawaletsa Mzimu Woyera kuti asalalikire mau mu Asiya;
7 pamene anafika kundunji kwa Misiya, anayesa kunka ku Bitiniya; ndipo Mzimu wa Yesu sanawaloleze;
8 ndipo pamene anapita pambali pa Misiya, anatsikira ku Troasi.
Masomphenya a ku Troasi. Paulo aoloka nalalikira ku Filipi. Za Lidia wogulitsa chibakuwa. Mdindo wa ku Filipi
9 Ndipo masomphenya anaonekera kwa Paulo usiku: Panali munthu wa ku Masedoniya alinkuimirira, namdandaulira kuti, Muolokere ku Masedoniya kuno, mudzatithangate ife.
10 Pamene anaona masomphenyawo, pomwepo tinayesa kutulukira kunka ku Masedoniya, poganizira kuti Mulungu anaitanira ife kulalikira Uthenga Wabwino kwa iwo.
11 Chotero tinachokera ku Troasi m’ngalawa, m’mene tinalunjikitsa ku Samotrase, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli;
12 pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mzinda wa ku Masedoniya, waukulu wa m’dzikomo, wa midzi ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.
13 Tsiku laSabatatinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.
14 Ndipo anatimva mkazi wina dzina lake Lidia, wakugulitsa chibakuwa, wa kumzinda wa Tiatira, amene anapembedza Mulungu; mtima wake Ambuye anatsegula; kuti amvere zimene anazinena Paulo.
15 Pamene anabatizidwa iye ndi a pabanja pake anatidandaulira ife, kuti, Ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, mulowe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo anatiumiriza ife.
16 Ndipo panali, pamene tinali kunka kukapemphera, anakomana ndi ife mdzakazi wina amene anali ndi mzimu wambwebwe, amene anapindulira ambuye ake zambiri pakubwebweta pake.
17 Ameneyo anatsata Paulo ndi ife, nafuula, kuti, Anthu awa ndi akapolo a Mulungu wa Kumwambamwamba, amene akulalikirani inu njira ya chipulumutso.
18 Ndipo anachita chotero masiku ambiri. Koma Paulo anavutika mtima ndithu, nacheuka, nati kwa mzimuwo, Ndikulamulira iwe m’dzina la YesuKhristu, tuluka mwa iye. Ndipo unatuluka nthawi yomweyo.
19 Koma pamene ambuye ake anaona kuti kulingalira kwa kupindula kwao kwatha, anagwira Paulo ndi Silasi, nawakokera kunka nao kubwalo kwa akulu,
20 ndipo pamene adanka nao kwa oweruza, anati, Anthu awa avuta kwambiri mzinda wathu, ndiwo Ayuda,
21 ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma.
22 Ndipo linagumukira iwo khamulo; ndipo oweruza anawang’ambira malaya ao; nalamulira kuti awakwapule.
23 Pamene anawaonetsa mikwingwirima yambiri, anawaika m’ndende, nauza mdindo kuti awasunge bwino.
24 Pakumva iye kulamulira kotero anawaika m’chipinda cha m’kati, namangitsa mapazi ao m’zigologolo.
25 Koma ngati pakati pa usiku, Paulo ndi Silasi analinkupemphera, naimbira Mulungu nyimbo, ndipo a m’ndendemo analinkuwamva;
26 ndipo mwadzidzidzi panali chivomezi chachikulu, chotero kuti maziko a ndende anagwedezeka: pomwepo pamakomo ponse panatseguka; ndi maunyolo a onse anamasuka.
27 Pamene anautsidwa kutulo mdindoyo, anaona kuti pa makomo a ndende panatseguka, ndipo anasolola lupanga lake, nati adziphe yekha, poyesa kuti am’ndende adathawa.
28 Koma Paulo anafuula ndi mau aakulu, nati, Usadzipweteka wekha; tonse tili muno.
29 Ndipo mdindo anaitanitsa nyali, natumphira m’kati, alinkunthunthumira ndi mantha, nagwa pamaso pa Paulo ndi Silasi,
30 nawatulutsira iwo kunja, nati, Ambuye, ndichitenji kuti ndipulumuke?
31 Ndipo iwo anati, Ukhulupirire Ambuye Yesu, ndipo udzapulumuka, iwe ndi apabanja ako.
32 Ndipo anamuuza iye mau a Ambuye, pamodzi ndi onse a pabanja pake.
33 Ndipo anawatenga ora lomwelo la usiku, natsuka mikwingwirima yao; nabatizidwa pomwepo, iye ndi a pabanja pake.
34 Ndipo anakwera nao kunka kunyumba kwake, nawakhazikira chakudya, nasangalala kwambiri, pamodzi ndi a pabanja pake, atakhulupirira Mulungu.
35 Kutacha, oweruza anatumiza akapitao, kuti, Mukamasule anthu aja.
36 Ndipo mdindo anafotokozera mauwo kwa Paulo, nati, Oweruza atumiza mau kunena kuti mumuke; tsopanotu tulukani, mukani mumtendere.
37 Koma Paulo anati kwa iwo, Adatikwapula ife pamaso pa anthu, osamva mlandu wathu, ife amene tili Aroma, natiika m’ndende; ndipo tsopano kodi afuna kutitulutsira ife m’tseri? Iai, ndithu; koma adze okha atitulutse.
38 Ndipo akapitao anafotokozera mauwo kwa oweruza; ndipo iwowo anaopa, pakumva kuti anali Aroma.
39 Ndipo anadza nawapembedza; ndipo pamene anawatulutsa, anawapempha kuti achoke pamzinda.
40 Ndipo anatuluka m’ndendemo, nalowa m’nyumba ya Lidia: ndipo pamene anaona abale, anawasangalatsa, namuka.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/16-d2fa865f2ae959b430bc4da3b5da4d7f.mp3?version_id=1068—