Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 15

Ku Yerusalemu atumwi ndi akulu aweruza za mdulidwe ndi Malamulo a Mose

1 Ndipo anadza ena akutsika ku Yudeya, nawaphunzitsa abale, nati, Mukapandakudulidwamonga mwambo wa Mose, simungathe kupulumuka.

2 Ndipo pamene Paulo ndi Barnabasi anachitana nao makani ndi mafunsano, abale anapatula Paulo ndi Barnabasi, ndi ena a iwo, kuti akwere kunka kuYerusalemukwaatumwindi akulu kukanena za funsolo.

3 Ndipo iwo anaperekezedwa ndiMpingo, napita pa Fenisiya ndi Samariya, nafotokozera chisanduliko chaamitundu; nakondweretsa kwambiri abale onse.

4 Pamene anafika ku Yerusalemu, analandiridwa ndi Mpingo, ndi atumwi ndi akulu, ndipo anabwerezanso zonse zimene Mulungu anachita nao.

5 Koma anauka ena a mpatuko waAfarisiokhulupirira, nati, Kuyenera kuwadula iwo, ndi kuwauza kuti asunge chilamulo cha Mose.

6 Ndipo anasonkhana atumwi ndi akulu kuti anene za mlanduwo.

7 Ndipo pamene panali mafunsano ambiri, Petro anaimirira, nati kwa iwo, Abale, mudziwa kuti poyamba Mulungu anasankha mwa inu, kuti m’kamwa mwanga amitundu amve mau a Uthenga Wabwino, nakhulupirire.

8 Ndipo Mulungu, amene adziwa mtima, anawachitira umboni; nawapatsa Mzimu Woyera, monga anatipatsa ife;

9 ndipo sanalekanitse ife ndi iwo, nayeretsa mitima yao m’chikhulupiriro.

10 Nanga bwanji tsopano mulikumuyesa Mulungu, kuti muike pa khosi laophunziragoli, limene sanathe kunyamula kapena makolo athu kapena ife?

11 Koma tikhulupirira tidzapulumuka mwa chisomo cha Ambuye YesuKhristu, monga iwo omwe.

12 Ndipo khamu lonse linatonthola; ndipo anamvera Barnabasi ndi Paulo alikubwerezanso zizindikiro ndi zozizwitsa zimene Mulungu anachita nao pa amitundu.

13 Pamene iwo anatonthola Yakobo anayankha, nati, Abale, mverani ine:

14 Simoni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.

15 Ndipo mau a aneneri avomereza pamenepo; monga kunalembedwa,

16 Zikatha izo ndidzabwera,

ndidzamanganso chihema cha Davide, chimene chinagwa;

ndidzamanganso zopasuka zake,

ndipo ndidzachiimikanso:

17 Kuti anthu otsalira afunefune Ambuye,

ndi amitundu onse amene dzina langa linatchulidwa pa iwo,

18 ati Ambuye, amene azidziwitsa zinthu zonsezo

chiyambire dziko lapansi.

19 Chifukwa chake ine ndiweruza, kuti tisavute a mwa amitundu amene anatembenukira kwa Mulungu,

20 koma kuti tilembere kwa iwo, kuti asale zonyansa za mafano, ndi dama, ndi zopotola, ndi mwazi.

21 Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m’mizinda yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m’masunagogemasabata onse.

22 Pamenepo chinakomera atumwi ndi akulu ndi Mpingo wonse kusankha anthu a m’gulu lao, ndi kuwatumiza ku Antiokeya ndi Paulo ndi Barnabasi; ndiwo Yudasi wotchedwa Barsabasi, ndi Silasi, akulu a mwa abale; ndipo analembera mau natumiza ndi iwo:

23 Atumwi ndi abale aakulu, kwa abale a mwa amitundu a mu Antiokeya, ndi Siriya, ndi Silisiya, tikupatsani moni:

24 Popeza tamva kuti ena amene anatuluka mwa ife anakuvutani ndi mau, nasocheretsa mitima yanu; amenewo sitinawalamulire;

25 chinatikomera ndi mtima umodzi, tisankhe anthu, ndi kuwatumiza kwa inu pamodzi ndi okondedwa anthu Barnabasi ndi Paulo,

26 anthu amene anapereka moyo wao chifukwa cha dzina la Yesu Khristu Ambuye wathu.

27 Tatumiza tsono Yudasi ndi Silasi, omwenso adzakuuzani ndi mau zinthu zomwezo.

28 Pakuti chinakomera Mzimu Woyera ndi ife, kuti tisasenzetse inu chothodwetsa chachikulu china choposa izi zoyenerazi;

29 kuti musale nsembe za mafano, ndi mwazi, ndi zopotola, ndi dama; ngati mudzisungitsa pa zimenezi, kudzakhala bwino kwa inu. Tsalani bwino.

30 Tsono pamene iwo anamuka anatsikira ku Antiokeya; ndipo anasonkhanitsa khamu, napereka kalatayo.

31 Pamene anawerenga, anakondwera chifukwa cha chisangalatso chake.

32 Ndipo Yudasi ndi Silasi, okhala eni okha aneneri, anasangalatsa abale ndi mau ambiri, nawalimbikitsa.

33 Pamene anakhala nthawi, abale analawirana nao ndi mtendere amuke kwa iwo amene anawatumiza.

35 Koma Paulo ndi Barnabasi anakhalabe mu Antiokeya, nalinkuphunzitsa, ndi kulalikira mau a Ambuye pamodzi ndi ena ambiri.

Paulo ndi Barnabasi alekana

36 Patapita masiku, Paulo anati kwa Barnabasi, Tibwerere, tizonde abale m’mizinda yonse m’mene tinalalikiramo mau a Ambuye, tione mkhalidwe wao.

37 Ndipo Barnabasi anafuna kumtenga Yohane uja, wotchedwa Marko

38 Koma sikunamkomere Paulo kumtenga iye amene anawasiya nabwerera pa Pamfiliya paja osamuka nao kuntchito.

39 Ndipo panali kupsetsana mtima, kotero kuti analekana wina ndi mnzake; ndipo Barnabasi anatenga Marko, nalowa m’ngalawa, nanka ku Kipro.

Ulendo wachiwiri wa Paulo

40 Koma Paulo anasankha Silasi, namuka, woikizidwa ndi abale ku chisomo cha Ambuye.

41 Ndipo iye anapita kupyola pa Siriya ndi Silisiya, nakhazikitsa Mipingo.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/15-83ee5dd69ebe51144522b3b168a38dbb.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *