Categories
MACHITIDWE

MACHITIDWE 13

Ulendo woyamba wa Paulo. Mpingo wa ku Antiokeya utuma Paulo ndi Barnabasi amuke kwa amitundu. Alalikira pa Kipro. Elimasi watsenga

1 Ndipo kunali aneneri ndi aphunzitsi ku Antiokeya muMpingowa komweko, ndiwo Barnabasi, ndi Simeoni, wonenedwa Wakuda, ndi Lusio wa ku Kirene, Manaene woleredwa pamodzi ndiHerodechiwangacho, ndi Saulo.

2 Ndipo pa kutumikira Ambuye iwowa, ndi kusala chakudya, Mzimu Woyera anati, Mundipatulire Ine Barnabasi ndi Saulo ku ntchito imene ndinawaitanirako.

3 Pamenepo, m’mene adasala chakudya ndi kupemphera ndi kuika manja pa iwo, anawatumiza amuke.

4 Pamenepo iwo, otumidwa ndi Mzimu Woyera, anatsikira ku Seleukiya; ndipo pochokerapo anapita m’ngalawa ku Kipro.

5 Ndipo pokhala ku Salami, analalikira mau a Mulungu m’masunagogea Ayuda; ndipo anali nayenso Yohane mnyamata wao.

6 Ndipo m’mene anapitirira chisumbu chonse kufikira Pafosi, anapezapo munthu watsenga,mneneriwonyenga, ndiye Myuda, dzina lake Barayesu;

7 ameneyo anali ndi kazembe Sergio Paulo, ndiye munthu wanzeru. Yemweyo anaitana Barnabasi ndi Saulo, nafunitsa kumva mau a Mulungu.

8 Koma Elimasi watsengayo (pakuti dzina lake litero posandulika) anawakaniza, nayesa kupatutsa kazembe asakhulupirire.

9 Koma Saulo, ndiye Paulo, wodzazidwa ndi Mzimu Woyera, anampenyetsetsa iye,

10 nati, Wodzala ndi chinyengo chonse ndi chenjerero lonse, iwe, mwana wa mdierekezi, mdani wa chilungamo chonse, kodi sudzaleka kuipsa njira zolunjika za Ambuye?

11 Ndipo tsopano, taona, dzanja la Ambuye lili pa iwe, ndipo udzakhala wakhungu wosapenya dzuwa nthawi. Ndipo pomwepo lidamgwera khungu ndi mdima; ndipo anamukamuka nafuna wina womgwira dzanja.

12 Pamenepo kazembe, pakuona chochitikacho anakhulupirira, nadabwa nacho chiphunzitso cha Ambuye.

Mau a Paulo m’sunagoge wa Antiokeya wa mu Pisidiya

13 Ndipo atamasula kuchokera ku Pafosi a ulendo wake wa Paulo anadza ku Perga wa ku Pamfiliya; koma Yohane anapatukana nao nabwerera kunka kuYerusalemu.

14 Koma iwowa, atapita pochokera ku Perga anafika ku Antiokeya wa mu Pisidiya; ndipo analowa m’sunagoge tsiku laSabata, nakhala pansi.

15 Ndipo m’mene adatha kuwerenga chilamulo ndi aneneri, akulu a sunagoge anatuma wina kwa iwo, ndi kunena, Amuna inu, abale, ngati muli nao mau akudandaulira anthu, nenani.

16 Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.

17 Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m’dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m’menemo.

18 Ndipo monga nthawi ya zaka makumi anai anawalekerera m’chipululu.

19 Ndipo m’mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri mu Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;

20 ndipo zitatha izi anawapatsa oweruza kufikira Samuele mneneriyo.

21 Ndipo kuyambira pamenepo anapempha mfumu; ndipo Mulungu anawapatsa Saulo mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini, zaka makumi anai.

22 Ndipo m’mene atamchotsa iye, anawautsira Davide akhale mfumu yao; amenenso anamchitira umboni, nati, Ndapeza Davide, mwana wa Yese, munthu wa pamtima panga, amene adzachita chifuniro changa chonse.

23 Wochokera mu mbeu yake Mulungu, monga mwa lonjezano, anautsira Israele Mpulumutsi, Yesu;

24 Yohane atalalikiratu, asanafike Iye, ubatizo wa kulapa kwa anthu onse a Israele.

25 Ndipo pakukwaniritsa njira yake Yohane, ananena, Muyesa kuti ine ndine yani? Ine sindine Iye. Koma taonani, akudza wina wonditsata ine, amene sindiyenera kummasulira nsapato za pa mapazi ake.

26 Amuna, abale, ana a mbadwa ya Abrahamu, ndi iwo mwa inu akuopa Mulungu, kwa ife atumidwa mau a chipulumutso ichi.

27 Pakuti iwo akukhala mu Yerusalemu, ndi akulu ao, popeza sanamzindikire Iye, ngakhale mau a aneneri owerengedwa masabata onse, anawakwaniritsa pakumtsutsa.

28 Ndipo ngakhale sanapeze chifukwa cha kumphera, anapempha Pilato kuti aphedwe.

29 Ndipo atatsiriza zonse zolembedwa za Iye, anamtsitsa kumtengo, namuika m’manda.

30 Koma Mulungu anamuukitsa Iye kwa akufa;

31 ndipo anaonekera masiku ambiri ndi iwo amene anamperekeza Iye pokwera ku Yerusalemu kuchokera ku Galileya, amenewo ndiwo akumchitira umboni tsopano kwa anthu.

32 Ndipo ife tikulalikirani inu Uthenga Wabwino wa lonjezano lochitidwa kwa makolo;

33 kuti Mulungu analikwaniritsa ili kwa ana athu pakuukitsa Yesu; monganso mulembedwa mu Salimo lachiwiri, Iwe ndiwe Mwana wanga, lero ndakubala.

34 Ndipo kuti anamuukitsa Iye kwa akufa, wosabweranso kuchivundi, anateropo, Ndidzakupatsani inu madalitso oyera ndi okhulupirika a Davide.

35 Chifukwa anenanso mu Salimo lina, Simudzapereka Woyera wanu aone chivundi.

36 Pakutitu, Davide, m’mene adautumikira uphungu wa Mulungu m’mbadwo mwake mwa iye yekha, anagona tulo, naikidwa kwa makolo ake, naona chivundi;

37 koma Iye amene Mulungu anamuukitsa sanaone chivundi.

38 Potero padziwike ndi inu amuna abale, kuti mwa Iye chilalikidwa kwa inu chikhululukiro cha machimo;

39 ndipo mwa Iye yense wokhulupirira ayesedwa wolungama kumchotsera zonse zimene simunangathe kudzichotsera poyesedwa wolungama ndi chilamulo cha Mose.

40 Chifukwa chake penyerani, kuti chingadzere inu chonenedwa ndi aneneriwo:

41 Taonani, opeputsa inu, zizwani, kanganukani;

kuti ndigwiritsa ntchito Ine masiku anu,

ntchito imene simudzaikhulupirira wina akakuuzani.

42 Ndipo pakutuluka iwo anapempha kuti alankhule naonso mau awa Sabata likudzalo.

43 Ndipo m’mene anthu a m’sunagoge anabalalika, Ayuda ambiri ndi akupinduka opembedza anatsata Paulo ndi Barnabasi; amene, polankhula nao, anawaumiriza akhale m’chisomo cha Mulungu.

44 Ndipo Sabata linalo udasonkhana pamodzi ngati mzinda wonse kumva mau a Mulungu.

45 Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.

46 Ndipo Paulo ndi Barnabasi analimbika mtima ponena, nati, Kunafunika kuti mau a Mulungu ayambe alankhulidwe kwa inu. Popeza muwakankha, nimudziyesera nokha osayenera moyo wosatha, taonani, titembenukira kwaamitundu.

47 Pakuti kotero anatilamula Ambuye ndi kuti,

Ndakuika iwe kuunika kwa amitundu,

kuti udzakhala iwe chipulumutso kufikira malekezero a dziko.

48 Ndipo pakumva ichi amitundu anakondwera, nalemekeza mau a Mulungu; ndipo anakhulupirira onse amene anaikidwiratu kumoyo wosatha.

49 Ndipo mau a Ambuye anabukitsidwa m’dziko lonse.

50 Koma Ayuda anakakamiza akazi opembedza ndi omveka, ndi akulu a mzindawo, nawautsira chizunzo Paulo ndi Barnabasi, ndipo anawapirikitsa iwo m’malire ao.

51 Koma iwo, m’mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio.

52 Ndipoophunziraanadzazidwa ndi chimwemwe ndi Mzimu Woyera.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/13-cf553d947e36e623913694e7382b1a75.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *