Yesu akwera kunka Kumwamba
1 Taonani Teofilo inu, mau aja oyamba ndinakonza, za zonse Yesu anayamba kuzichita ndi kuziphunzitsa,
2 kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba, atatha kulamula mwa Mzimu Woyeraatumwiamene adawasankha;
3 kwa iwonso anadzionetsera yekha wamoyo ndi zitsimikizo zambiri, zitatha zowawa zake, naonekera kwa iwo masiku makumi anai, ndi kunena zinthu za Ufumu wa Mulungu;
4 ndipo posonkhana nao pamodzi, anawalamulira asachoke kuYerusalemu, komatu alindire lonjezano la Atate, limene, anati, munalimva kwa Ine;
5 pakuti Yohane anabatizadi ndi madzi; koma inu mudzabatizidwa ndi Mzimu Woyera, asanapite masiku ambiri.
6 Pamenepo iwowa, atasonkhana pamodzi, anamfunsa Iye, nanena, Ambuye, kodi nthawi ino mubwezera ufumu kwa Israele?
7 Koma anati kwa iwo, Sikuli kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo, zimene Atate anaziika mu ulamuliro wake wa Iye yekha.
8 Komatu mudzalandira mphamvu, Mzimu Woyera atadza pa inu: ndipo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ndi mu Yudeya monse, ndi mu Samariya, ndi kufikira malekezero ake a dziko.
9 Ndipo m’mene adanena izi, ali chipenyerere iwo, ananyamulidwa; ndipo mtambo unamlandira Iye kumchotsa kumaso kwao.
10 Ndipo pakukhala iwo chipenyerere kumwamba pomuka Iye, taonani, amuna awiri ovala zoyera anaimirira pambali pao;
11 amenenso anati, Amuna a ku Galileya, muimiranji ndi kuyang’ana kumwamba? Yesu amene walandiridwa kunka Kumwamba kuchokera kwa inu, adzadza momwemo monga munamuona alinkupita Kumwamba.
Asankha mlowammalo wa Yudasi
12 Pamenepo anabwera ku Yerusalemu kuchokera kuphiri lonenedwa la Azitona, limene liyandikana ndi Yerusalemu, loyendako tsiku laSabata.
13 Ndipo pamene adalowa, anakwera kuchipinda chapamwamba, kumene analikukhalako; ndiwo Petro ndi Yohane ndi Yakobo ndi Andrea, Filipo ndi Tomasi, Bartolomeo ndi Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi SimoniZelote, ndi Yudasi mwana wa Yakobo.
14 Iwo onse analikukangalika m’kupemphera, pamodzi ndi akazi, ndi Maria, amake wa Yesu, ndi abale ake omwe.
15 Ndipo m’masiku awa anaimirira Petro pakati pa abale, nati (gulu la anthu losonkhana pamalo pomwe ndilo ngati zana limodzi ndi makumi awiri),
16 Amuna inu, abale, kunayenera kuti lemba likwanitsidwe, limene Mzimu Woyera anayamba kunena mwa m’kamwa mwa Davide za Yudasi, wokhala mtsogoleri wa iwo adagwira Yesu.
17 Chifukwa anali wowerengedwa mwa ife, ndipo analandira gawo lake la utumiki uwu.
18 (Uyutu tsono anadzitengera kadziko ndi mphotho ya chosalungama; ndipo anagwa chamutu, naphulika pakati, ndi matumbo ake onse anakhuthuka;
19 ndipo chinadziwika ndi onse akukhala ku Yerusalemu; kotero kuti m’manenedwe ao kadzikoka kanatchedwa Akeledama, ndiko, kadziko ka mwazi.)
20 Pakuti kwalembedwa m’buku la Masalimo,
Pogonera pake pakhale bwinja,
ndipo pasakhale munthu wogonapo;
ndipo uyang’aniro wake autenge wina.
21 Potero kuyenera kuti wina wa amunawo anatsatana nafe nthawi yonseyi Ambuye Yesu analowa natuluka mwa ife,
22 kuyambira ubatizo wa Yohane, kufikira tsiku lija anatengedwa kunka Kumwamba kutisiya ife, mmodzi wa awa akhale mboni ya kuuka kwake pamodzi ndi ife.
23 Ndipo anaimikapo awiri, Yosefe wotchedwa Barsabasi, amene anatchedwanso Yusto, ndi Matiasi.
24 Ndipo anapemphera, nati, Inu, Ambuye, wozindikira mitima ya onse, sonyezani mwa awa awiri mmodziyo amene munamsankha,
25 alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.
26 Ndipo anayesa maere pa iwo; ndipo anagwera Matiasi; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi khumi ndi mmodziwo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/ACT/1-efff22e641f1f1523c69ab3ddd472107.mp3?version_id=1068—