Categories
LUKA

LUKA 7

Kenturiyo wa ku Kapernao

1 Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m’makutu a anthu, analowa mu Kapernao.

2 Ndipo kapolo wakenturiyo, wokondedwa naye, anadwala, nafuna kutsirizika.

3 Ndipo pamene iye anamva za Yesu, anatuma kwa Iye akulu a Ayuda, namfunsa Iye kuti adze kupulumutsa kapolo wake.

4 Ndipo iwo, pakufika kwa Yesu, anampempha Iye koumirira, nati, Ayenera iye kuti mumchitire ichi;

5 pakuti akonda mtundu wathu, ndipo anatimangira ifesunagoge.

6 Ndipo Yesu anapita nao. Ndipo pakufika Iye tsono pafupi pa nyumba yake, kenturiyo anatuma kwa Iye abwenzi ake, kunena naye, Ambuye, musadzivute; pakuti sindiyenera ine kuti mudzalowe pansi pa tsindwi langa;

7 chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.

8 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita.

9 Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.

10 Ndipo pakubwera kunyumba otumidwawo, anapeza kapoloyo wachira ndithu.

Aukitsa mnyamata ku Naini

11 Ndipo kunali, katapita kamphindi, Iye anapita kumzinda, dzina lake Naini; ndipoophunziraake ndi mpingo waukulu wa anthu anapita naye.

12 Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.

13 Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.

14 Ndipo anayandikira, nakhudza chithatha; ndipo akumnyamulawo anaima. Ndipo Iye anati, Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.

15 Ndipo wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.

16 Ndipo mantha anagwira onsewo: ndipo analemekeza Mulungu, nanena kuti,Mneneriwamkulu wauka mwa ife; ndipo Mulungu wadzacheza ndi anthu ake.

17 Ndipo mbiri yake imeneyo inabuka ku Yudeya yense, ndi ku dziko lonse loyandikira.

Amithenga a Yohane Mbatizi

18 Ndipo ophunzira a Yohane anamuuza iye zonsezi.

19 Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

20 Ndipo pakufika kwa Iye anthu awo, anati, Yohane Mbatizi watituma ife kwa Inu, kuti, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang’anire wina?

21 Nthawi yomweyo Iye anachiritsa anthu ambiri nthenda zao, ndi zovuta, ndi ziwanda; napenyetsanso anthu akhungu ambiri.

22 Ndipo anayankha, nati kwa iwo, Mukani, muuze Yohane zimene mwaziona, nimwazimva; anthu akhungu alandira kuona kwao, opunduka miyendo ayenda, akhateakonzedwa, ogontha akumva, akufa aukitsidwa, kwa aumphawi ulalikidwa Uthenga Wabwino.

23 Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.

24 Ndipo atachoka amithenga ake a Yohane, Iye anayamba kunena za Yohane kwa anthu a makamu aja, nati, Munatuluka kunka kuchipululu kukapenya chiyani? Bango logwedezeka ndi mphepo kodi?

25 Koma munatuluka kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zofewa kodi? Onani, iwo akuvala zolemera, ndi akukhala odyerera, ali m’nyumba za mafumu.

26 Koma munatuluka kukaona chiyani? Mneneri kodi? Etu, ndinena kwa inu, ndipo wakuposa mneneri.

27 Uyu ndi iye amene kunalembedwa za iye,

Ona, ndituma Ine mthenga wanga akutsogolere,

amene adzakukonzera njira yako pamaso pako.

28 Ndinena kwa inu, kuti, Mwa akubadwa ndi akazi palibe mmodzi wamkulu woposa Yohane; koma iye amene ali wamng’ono mu Ufumu wa Mulungu amposa iye.

29 Ndipo anthu onse ndiamisonkhoomwe, pakumva, anavomereza kuti Mulungu ali wolungama, popeza anabatizidwa iwo ndi ubatizo wa Yohane.

30 KomaAfarisindi achilamulo anakaniza uphungu wa Mulungu kwa iwo okha, popeza sanabatizidwe ndi iye.

31 Ndipo, ndidzafanizira ndi chiyani anthu a mbadwo uno? Ndipo afanana ndi chiyani?

32 Angofanana ndi ana akukhala pamsika, ndi kuitanizana wina ndi mnzake, ndi kunena, Ife tinakulizirani chitoliro, ndipo inu simunavine ai; tinabuma maliro, ndimo simunalire ai.

33 Pakuti Yohane Mbatizi wafika wosadya mkate ndi wosamwa vinyo; ndipo munena, Ali ndi chiwanda.

34 Mwana wa Munthuwafika wakudya ndi wakumwa; ndipo munena, Onani, munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi anthu ochimwa!

35 Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ana ake onse.

Mkazi adzoza mapazi a Yesu

36 Ndipo mmodzi wa Afarisi anamuitana Iye kuti akadye naye. Ndipo analowa m’nyumba ya Mfarisi, naseama pachakudya.

37 Ndipo onani, mkazi wochimwa, amene anali m’mzindamo; ndipo pakudziwa kuti Yesu analikuseama pachakudya m’nyumba ya Mfarisi, anatenga nsupa ya alabastero ya mafuta onunkhira bwino,

38 naimirira kumbuyo, pa mapazi ake, nalira, nayamba kukhathamiza mapazi ake ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi la mutu wake, nampsompsonetsa mapazi ake, nawadzoza ndi mafuta onunkhira bwino.

39 Koma Mfarisi, amene adamuitana Iye, pakuona, ananena mwa yekha, nati, Akadakhala mneneri uyu akadazindikira ali yani, ndi wotani mkaziyo womkhudza Iye, chifukwa ali wochimwa.

40 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Simoni, ndili ndi kanthu kakunena kwa iwe. Ndipo iye anavomera, Mphunzitsi, nenani.

41 Munthu wokongoletsa ndalama anali nao amangawa awiri; mmodziyo anali ndi mangawa ake a marupiya mazana asanu, koma mnzake makumi asanu.

42 Popeza analibe chobwezera iwo, anawakhululukira onse awiri. Chotero, ndani wa iwo adzaposa kumkonda?

43 Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa.

44 Ndipo anati kwa iye, Waweruza bwino. Ndipo m’mene Iye anacheukira kwa mkaziyo, anati kwa Simoni, Upenya mkazi ameneyu kodi? Ndinalowa m’nyumba yako, sunandipatse madzi akusambitsa mapazi anga; koma uyu anakonkha mapazi anga ndi misozi, nawapukuta ndi tsitsi lake.

45 Sunandipatsa mpsompsono wa chibwenzi; koma uyu sanaleke kupsompsonetsa mapazi anga, chilowere muno Ine.

46 Sunandidzoza mutu wanga ndi mafuta; koma uyu anadzoza mapazi anga ndi mafuta onunkhira bwino.

47 Chifukwa chake, ndinena kwa iwe, Machimo ake, ndiwo ambiri, akhululukidwa; chifukwa anakonda kwambiri; koma munthu amene anamkhululukira pang’ono, iye akonda pang’ono.

48 Ndipo anati kwa mkazi, Machimo ako akhululukidwa.

49 Ndipo iwo akuseama naye pachakudya anayamba kunena mwa okha, Uyu ndani amene akhululukiranso machimo?

50 Ndipo Iye anati kwa mkaziyo, Chikhulupiriro chako chakupulumutsa iwe; muka ndi mtendere.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/7-543b8d72ae78bbff60c8e929963b6646.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *