Asodzi athandizidwa ndi Yesu, namtsata
1 Ndipo panali, pakumkanikiza khamu la anthu, kudzamva mau a Mulungu, Iye analikuimirira m’mbali mwa nyanja ya Genesarete;
2 ndipo anaona ngalawa ziwiri zinakhala m’mbali mwa nyanja; koma asodzi a nsomba adatuluka m’menemo, nalikutsuka makoka ao.
3 Ndipo Iye analowa m’ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang’ono. Ndipo anakhala pansi m’menemo, naphunzitsa m’ngalawa makamuwo a anthu.
4 Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza.
5 Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.
6 Ndipo pamene anachita ichi, anazinga unyinji waukulu wa nsomba; ndipo makoka ao analinkung’ambika;
7 ndipo anakodola anzao a m’ngalawa yinayo, adze awathangate. Ndipo anadza, nadzaza ngalawa zonse ziwiri, motero kuti zinalinkumira.
8 Koma Simoni Petro, pamene anaona, anagwa pansi pa mawondo ake a Yesu, nanena, Muchoke kwa ine, Ambuye, chifukwa ndine munthu wochimwa.
9 Pakuti chizizwo chidagwira iye, ndi onse amene anali naye, pa kusodzako kwa nsomba zimene anazikola;
10 ndipo chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedeo, amene anali anzake a Simoni. Ndipo Yesu anati kwa Simoni, Usaope, kuyambira tsopano udzakhala msodzi wa anthu.
11 Ndipo m’mene iwo anakocheza ngalawa zao pamtunda, anasiya zonse, namtsata Iye.
Wakhate achiritsidwa
12 Ndipo panali, pamene Iye anali mumzinda wina, taona, munthu wodzala ndikhate; ndipo pamene anaona Yesu, anagwa nkhope yake pansi, nampempha Iye, nanena, Ambuye, ngati mufuna mungathe kundikonza.
13 Ndipo Iye anatambalitsa dzanja lake, namkhudza, nanena, Ndifuna, takonzeka. Ndipo pomwepo khate linachoka kwa iye.
14 Ndipo Iye anamuuzitsa, kuti asanene kwa munthu aliyense; koma uchoke, nudzionetse wekha kwa wansembe, nupereke nsembe ya pa chikonzedwe chako, monga adalamulira Mose, kukhale umboni kwa iwo.
15 Koma makamaka mbiri yake ya Iye inabuka: ndipo mipingo yambiri ya anthu inasonkhana kudzamvera, ndi kudzachiritsidwa nthenda zao.
16 Koma Iye anazemba, nanka m’mapululu, nakapemphera.
Yesu achiritsa munthu wamanjenje
17 Ndipo panali tsiku limodzi la masiku awo, Iye analikuphunzitsa; ndipo analikukhalapoAfarisindiaphunzitsi a malamulo, amene anachokera kumidzi yonse ya ku Galileya, ndi Yudeya ndiYerusalemu:ndipo mphamvu ya Ambuye inali ndi Iye yakuwachiritsa.
18 Ndipo onani, anthu alikunyamulira pakama munthu wamanjenje; nafunafuna kulowa naye, ndi kumuika pamaso pa Iye.
19 Ndipo posapeza polowa naye, chifukwa cha unyinji wa anthu, anakwera pamwamba pa tsindwi, namtsitsira iye poboola pa tsindwi ndi kama wake, namfikitsa pakati pomwe pamaso pa Yesu.
20 Ndipo Iye, pakuona chikhulupiriro chao, anati, Munthu iwe, machimo ako akhululukidwa.
21 Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?
22 Koma Yesu anadziwa zoyesayesa zao, nayankha, nati kwa iwo, Muyesayesa bwanji m’mitima yanu?
23 Chapafupi nchiti, kunena, Akhululukidwa kwa iwe machimo ako; kapena kunena, Tauka, nuyende?
24 Koma kuti mudziwe kutiMwana wa Munthuali nayo mphamvu padziko lapansi yakukhululukira machimo, (anati Iye kwa wamanjenjeyo), Ndinena kwa iwe, Tauka, nusenze kama wako, numuke kunyumba kwako.
25 Ndipo pomwepo anaimirira pamaso pao, nasenza chimene adagonapo, nachokapo, kunka kunyumba kwake, wakulemekeza Mulungu.
26 Ndipo chizizwo chinagwira anthu onse ndipo analemekeza Mulungu; nadzazidwa ndi mantha, nanena kuti, Lero taona zodabwitsa.
Kuitanidwa kwa Levi
27 Ndipo zitatha izi Iye anatuluka, naona munthuwamsonkho, dzina lake Levi, alikukhala polandirira msonkho, nati kwa iye, Unditsate Ine.
28 Ndipo iye anasiya zonse, nanyamuka, namtsata Iye.
29 Ndipo Levi anamkonzera Iye phwando lalikulu kunyumba kwake; ndipo panali khamu lalikulu la amisonkho, ndi enanso amene analikuseama pachakudya pamodzi nao.
30 Ndipo Afarisi ndi alembi ao anang’ung’udza kwaophunziraake, nanena, kuti, Bwanji inu mukudya ndi kumwa pamodzi ndi anthu amisonkho ndi ochimwa?
31 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Amene ali olimba safuna sing’anga; koma akudwala ndiwo.
32 Sindinadza Ine kuitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.
Za kudzikana kudya
33 Ndipo iwo anati kwa Iye, Ophunzira a Yohane amasala kudya kawirikawiri, ndi kuchita mapemphero; chimodzimodzinso iwo a Afarisi; koma anu amangokudya ndi kumwa.
34 Koma Yesu anati kwa iwo, Kodi mungathe kuletsa anyamata a ukwati asadye, pamene mkwati ali nao pamodzi?
35 Koma masiku adzafika; ndipo pamene mkwati adzachotsedwa kwa iwo, pamenepo adzasala kudya masiku omwewo.
36 Ndipo Iye ananenansofanizokwa iwo, kuti, Palibe munthu ang’amba chigamba cha malaya atsopano, nachiphatika pa malaya akale; chifukwa ngati atero, angong’ambitsa atsopanowo, ndi chigamba cha atsopanowo sichidzayenerana ndi akalewo.
37 Ndipo palibe munthu atsanulira vinyo watsopano m’matumba akale; chifukwa ngati atero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba, ndipo ameneyo adzatayika, ndi matumba adzaonongeka.
38 Koma kuyenera kutsanulira vinyo watsopano m’matumba atsopano.
39 Ndipo palibe munthu atamwa vinyo wakale afuna watsopano; pakuti anena, Wakale ali wokoma.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/5-8c13c28ffeb75c80b5816d67601277f7.mp3?version_id=1068—