Categories
LUKA

LUKA 4

Kuyesedwa kwa Yesu

1 Ndipo Yesu, wodzala ndi Mzimu Woyera, anabwera kuchokera ku Yordani, natsogozedwa ndi Mzimu kunka kuchipululu

2 kukayesedwa ndi mdierekezi masiku makumi anai. Ndipo Iye sanadye kanthu masiku awo; ndipo pamene anatha anamva njala.

3 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu usanduke mkate.

4 Ndipo Yesu anayankha nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha.

5 Ndipo m’mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m’kamphindi kakang’ono.

6 Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna.

7 Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu.

8 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti,

Ambuye Mulungu wako uzimgwadira,

ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.

9 Ndipo anamtsogolera Iye kuYerusalemu, namuika Iye pamwamba penipeni pa Kachisiyo, nati kwa Iye, Ngati muli Mwana wa Mulungu, tadzigwetsani nokha pansi;

10 pakuti kwalembedwa kuti,

Adzalamulaangeloake za iwe, kuti akutchinjirize.

11 Ndipo,

Pa manja ao adzakunyamula iwe,

kuti ungagunde konse phazi lako pamwala.

12 Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwanenedwa,

Usamuyese Ambuye Mulungu wako.

13 Ndipo mdierekezi, m’mene adamaliza mayesero onse, analekana naye kufikira nthawi ina.

Yesu aphunzitsa ku Nazarete nachotsedwako

14 Ndipo Yesu anabwera ndi mphamvu ya Mzimu ku Galileya; ndipo mbiri yake ya Iye inabuka ku dziko lonse loyandikira.

15 Ndipo Iye anaphunzitsa m’masunagogemwao, nalemekezedwa ndi anthu onse.

16 Ndipo anadza ku Nazarete, kumene analeredwa; ndipo tsiku la Sabata analowa m’sunagoge, monga anazolowera, naimiriramo kuwerenga m’kalata.

17 Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesayamneneri. Ndipo m’mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,

18 Mzimu wa Ambuye uli pa Ine,

chifukwa chake Iye anandidzoza Ine

ndiuze anthu osauka Uthenga Wabwino:

anandituma Ine kulalikira am’nsinga mamasulidwe,

ndi akhungu kuti apenyanso,

kutulutsa ndi ufulu ophwanyika,

19 kulalikira chaka chosankhika cha Ambuye.

20 Ndipo m’mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m’sunagogemo anamyang’anitsa Iye.

21 Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m’makutu anu.

22 Ndipo onse anamchitira Iye umboni nazizwa ndi mau a chisomo akutuluka m’kamwa mwake; nanena, Kodi uyu si mwana wa Yosefe?

23 Ndipo anati kwa iwo, Kwenikweni mudzati kwa Ine nkhani iyi, Sing’anga iwe, tadzichiritsa wekha: zonse zija tazimva zinachitidwa ku Kapernao, muzichitenso zomwezo kwanu kuno.

24 Ndipo Iye anati, Indetu, ndinena kwa inu, kuti, Palibe mneneri alandirika kudziko la kwao.

25 Koma zoonadi ndinena kwa inu, kuti, Munali akazi amasiye ambiri mu Israele masiku ake a Eliya, pamene kunatsekedwa kumwamba zaka zitatu ndi miyezi isanu ndi umodzi, pamene panakhala njala yaikulu padziko lonselo;

26 ndipo Eliya sanatumidwe kwa mmodzi wa iwo, koma ku Sarepta wa ku Sidoni, kwa mkazi wamasiye.

27 Ndipo munali akhateambiri mu Israele masiku a Elisa mneneri; ndipo palibe mmodzi wa iwo anakonzedwa, koma Naamani yekha wa ku Siriya.

28 Ndipo onse a m’sunagogemo anadzala ndi mkwiyo pakumva izi;

29 nanyamuka namtulutsira Iye kunja kwa mzindawo, nanka naye pamutu paphiri pamene panamangidwa mzinda wao, kuti akamponye Iye pansi.

30 Koma Iye anapyola pakati pao, nachokapo.

Yesu achiritsa munthu wogwidwa ndi chiwanda

31 Ndipo Iye anatsika nadza ku Kapernao, ndiwo mzinda wa ku Galileya. Ndipo analikuwaphunzitsa iwo pa Sabata; ndipo anadabwa ndi chiphunzitso chake;

32 chifukwa mau ake anali ndi ulamuliro.

33 Ndipo m’sunagoge munali munthu, wokhala nacho chiwanda chonyansa; nafuula ndi mau olimba, kuti,

34 Ha! Tili ndi chiyani ndi Inu, Yesu wa ku Nazarete? Kodi munadza kutiononga ife? Ndikudziwani Inu muli yani, ndinu Woyera wake wa Mulungu.

35 Ndipo Yesu anamdzudzula iye, nanena, Tonthola, nutuluke mwa iye. Ndipo chiwandacho m’mene chinamgwetsa iye pakati, chinatuluka mwa iye chosampweteka konse.

36 Ndipo anthu onse anadabwa, nalankhulana wina ndi mnzake, nanena, Mau amenewa ali otani? Chifukwa ndi ulamuliro ndi mphamvu angolamulira mizimu yonyansa, ndipo ingotuluka.

37 Ndipo mbiri yake ya Iye inafalikira kumalo onse a dziko loyandikira.

Yesu achiritsa mpongozi wa Simoni

38 Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m’sunagoge, nalowa m’nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye.

39 Ndipo Iye anaimirira, naweramira pa iye, nadzudzula nthendayo; ndipo inamleka iye: ndipo anauka msangatu, nawatumikira.

40 Ndipo pakulowa dzuwa anthu onse amene anali nao odwala ndi nthenda za mitundumitundu, anadza nao kwa Iye; ndipo Iye anaika manja ake pa munthu aliyense wa iwo, nawachiritsa.

41 Ndi ziwanda zomwe zinatuluka mwa ambiri, ndi kufuula, kuti, Inu ndinu Mwana wa Mulungu. Ndipo Iye anazidzudzula, wosazilola kulankhula, chifukwa zinamdziwa kuti Iye ndiyeKhristu.

Yesu alalikira m’masunagoge

42 Ndipo kutacha anatuluka Iye nanka kumalo achipululu; ndi makamu a anthu analikumfunafuna Iye, nadza nafika kwa Iye, nayesa kumletsa Iye, kuti asawachokere.

43 Koma anati kwa iwo, Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.

44 Ndipo Iye analikulalikira m’masunagoge a ku Yudeya.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/4-1264bf56b62a6c7b943fffc488829b55.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *