Yesu pa bwalo la Pilato
1 Ndipo khamu lonselo linanyamuka kupita naye kwa Pilato.
2 Ndipo anayamba kumnenera Iye, kuti, Tinapeza munthu uyu alikupandutsa anthu a mtundu wathu, ndi kuwaletsa kupereka msonkho kwaKaisara, nadzinenera kuti Iye yekha ndiyeKhristumfumu.
3 Ndipo Pilato anamfunsa Iye, nanena, Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda? Ndipo Iye anamyankha nati, Mwatero.
4 Ndipo Pilato anati kwa ansembe aakulu ndi makamu a anthu, Ndilibe kupeza chifukwa cha mlandu ndi munthu uyu.
5 Koma iwo anapunda kunena kuti, Amautsa anthuwo, naphunzitsa mu Yudeya yense, kuyambira ku Galileya ndi kufikira kuno komwe.
6 Koma pamene Pilato anamva, anafunsa ngati munthuyu ali Mgalileya.
7 Ndipo m’mene anadziwa kuti ali wa mu ulamuliro wake waHerode, anamtumiza Iye kwa Herode, amene anali iye mwini kuYerusalemumasiku awa.
Yesu atumidwa kwa Herode
8 Ndipo Herode, pamene anaona Yesu, anakondwa ndithu; pakuti anayamba kale kufuna kumpenya Iye, chifukwa anamva za Iye; nayembekeza kuona chizindikiro china chochitidwa ndi Iye.
9 Ndipo anamfunsa Iye mau ambiri; koma Iye sanamyankhe kanthu.
10 Ndipo ansembe aakulu ndi alembi anaimirira, namnenera Iye kolimba.
11 Ndipo Herode ndi asilikali ake anampeputsa Iye, namnyoza, namveka Iye chofunda chonyezimira, nambwezera kwa Pilato.
12 Ndipo Herode ndi Pilato anachitana chibwenzi tsiku lomwelo; pakuti kale anadana.
Yesu abwezedwa kwa Pilato. Baraba amasulidwa. Yesu amangidwa
13 Ndipo Pilato anaitana ansembe aakulu, ndi akulu, ndi anthu, asonkhane,
14 nati kwa iwo, Munadza kwa ine ndi munthu uyu ngati munthu wakupandutsa anthu: ndipo taonani, Ine ndinamfunsa za mlanduwu pamaso panu, ndipo sindinapeze pa munthuyu chifukwa cha zinthu zimene mumnenera;
15 inde, ngakhale Herode yemwe; pakuti iye anambwezera Iye kwa ife; ndipo taonani, sanachite Iye kanthu kakuyenera kufa.
16 Chifukwa chake ndidzamkwapula ndi kummasula Iye.
18 Koma iwo onse pamodzi anafuula, nati, Chotsani munthu uyu, mutimasulire Barabasi;
19 ndiye munthu anaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko m’mzinda ndi cha kupha munthu.
20 Ndipo Pilato analankhulanso nao, nafuna kumasula Yesu;
21 koma iwo anafuula, nanena, Mpachikeni, mpachikeni pamtanda.
22 Ndipo anati kwa iwo nthawi yachitatu, Nanga munthuyu anachita choipa chiyani? Sindinapeze chifukwa cha kufera Iye; chotero ndidzamkwapula Iye ndi kummasula.
23 Koma anakakamiza ndi mau okweza, napempha kuti Iye apachikidwe. Ndipo mau ao anapambana.
24 Ndipo Pilato anaweruza kuti chimene alikufunsa chichitidwe.
25 Ndipo anawamasulira amene adaponyedwa m’ndende chifukwa cha mpanduko ndi kupha munthu, amene iwo anampempha; koma anapereka Yesu mwa chifuniro chao.
Yesu panjira ya ku Gologota
26 Ndipo popita naye, anagwira munthu, Simoni wa ku Kirene, alikuchokera kuminda, namsenza iye mtanda aunyamule pambuyo pake pa Yesu.
27 Ndipo unamtsata unyinji waukulu wa anthu, ndi wa akazi amene anadziguguda pachifuwa, namlirira Iye.
28 Koma Yesu anawapotolokera nati, Ana aakazi inu a Yerusalemu, musandilirire Ine, koma mudzilirire nokha ndi ana anu.
29 Chifukwa taonani masiku alinkudza, pamene adzati, Odala ali ouma ndi mimba yosabala, ndi mawere osayamwitsa.
30 Pomwepo adzayamba kunena kwa mapiri, Igwani pa ife; ndi kwa zitunda, Bisani ife.
31 Pakuti ngati azichitira izi mtengo wauwisi, nanga kudzatani ndi wouma?
32 Ndipo analinso awiri ena, ndiwo ochita zoipa, anatengedwa pamodzi ndi Iye kuti aphedwe.
Yesu apachikidwa pamtanda
33 Ndipo pamene anafika kumalo dzina lake Bade, anampachika Iye pamtanda pomwepo, ndi ochita zoipa omwe, mmodzi kudzanja lamanja ndi wina kulamanzere.
34 Ndipo Yesu ananena, Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziwa chimene achita. Ndipo anagawana zovala zake, poyesa maere.
35 Ndipo anthu anaima alikupenya. Ndi akulunso anamlalatira Iye, nanena, Anapulumutsa ena; adzipulumutse yekha ngati iye ndiye Khristu wa Mulungu, wosankhidwa wake.
36 Ndipo asilikalinso anamnyoza, nadza kwa Iye, nampatsa vinyo wosasa,
37 nanena, Ngati Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda, udzipulumutse wekha.
38 Ndipo kunalinso lembo pamwamba pake, ndilo: UYU NDIYE MFUMU YA AYUDA.
39 Ndipo mmodzi wa ochita zoipa anapachikidwawo anamchitira Iye mwano nanena, Kodi suli Khristu Iwe? Udzipulumutse wekha ndi ife.
40 Koma winayo anayankha, namdzudzula iye, nati, Kodi suopa Mulungu, poona uli m’kulangika komweku?
41 Ndipo ifetu kuyenera; pakuti tilikulandira zoyenera zimene tinazichita: koma munthu uyu sanachite kanthu kolakwa.
42 Ndipo ananena, Yesu, ndikumbukireni m’mene mulowa Ufumu wanu.
43 Ndipo Iye ananena naye, Indetu, ndinena ndi iwe, Lero lino udzakhala ndine mu Paradaiso.
44 Ndipo ora lake pamenepo linali ngati lachisanu ndi chimodzi. Ndipo panali mdima padziko lonse kufikira ora lachisanu ndi chinai, ndipo dzuwa linada.
45 Ndipo nsalu yotchinga ya mu Kachisi inang’ambika pakati.
46 Ndipo pamene Yesu anafuula ndi mau aakulu, anati, Atate, m’manja mwanu ndipereka mzimu wanga. Ndipo pakutero anapereka mzimu wake.
47 Ndipo pamenekenturiyoanaona chinachitikacho, analemekeza Mulungu, nanena, Zoonadi munthu uyu anali wolungama.
48 Ndipo makamu onse osonkhana kudzapenya ichi, pamene anaona zinachitikazo, anapita kwao ndi kudziguguda pachifuwa.
49 Ndipo omdziwa Iye onse, ndi akazi amene adamtsata kuchokera ku Galileya, anaima kutali, naona zinthu izi.
Aika maliro a Yesu
50 Ndipo taonani, munthu dzina lake Yosefe, ndiye mkulu wa milandu, munthu wabwino ndi wolungama
51 (amene sanavomereze kuweruza kwao ndi ntchito yao) wa ku Arimatea, mudzi wa Ayuda, ndiye woyembekezera Ufumu wa Mulungu,
52 yemweyo anapita kwa Pilato napempha mtembo wake wa Yesu.
53 Ndipo anautsitsa, naukulunga m’nsalu yabafuta, nauika m’manda osemedwa m’mwala, m’menemo sanaike munthu ndi kale lonse.
54 Ndipo panali tsiku lokonzera, ndiSabatalinayandikira.
55 Ndipo akazi, amene anachokera naye ku Galileya, anatsata m’mbuyo, naona manda, ndi maikidwe a mtembo wake.
56 Ndipo anapita kwao, nakonza zonunkhira ndi mafuta abwino. Ndipo pa Sabata anapumula monga mwa lamulo.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/23-5967a570e5332fcf7dc9c062d19e1e77.mp3?version_id=1068—