Categories
LUKA

LUKA 12

Yesu awachenjeza za chinyengo

1 Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwaophunziraake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate chaAfarisi, chimene chili chinyengo.

2 Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

3 Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m’khutu, m’zipinda za m’kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.

Awatchulira amene ayenera kumuopa

4 Ndipo ndinena kwa inu, abwenzi anga, Musaope iwo akupha thupi, ndipo akatha ichi alibe kanthu kena angathe kuchita.

5 Koma ndidzakulangizani amene muzimuopa; taopani Iye amene atatha kupha ali ndi mphamvu yakutaya kuGehena, inde, ndinena ndinu opani ameneyo.

6 Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu;

7 komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.

8 Ndipo ndinena kwa inu, Amene aliyense akavomereza Ine pamaso pa anthu, inde,Mwana wa Munthuadzamvomereza iye pamaso paangeloa Mulungu;

9 Koma iye wondikana Ine pamaso pa anthu, iye adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.

10 Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

11 Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m’sunagogendi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani;

12 pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena.

Fanizo la mwini chuma wopusa

13 Ndipo munthu wa m’khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye.

14 Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu?

15 Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang’anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

16 Ndipo Iye ananena naofanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino.

17 Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga?

18 Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa.

19 Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere.

20 Koma Mulungu anati kwa iye, Wopusa iwe, usiku womwe uno udzafunidwa moyo wako; ndipo zinthu zimene unazikonza zidzakhala za yani?

21 Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Nkhawa za moyo wathu

22 Ndipo Iye anati kwa ophunzira ake, Chifukwa chake ndinena ndinu, Musade nkhawa ndi moyo wanu, chimene mudzadya; kapena ndi thupi lanu, chimene mudzavala.

23 Pakuti moyo uli woposa chakudya, ndi thupi liposa chovala.

24 Lingirirani makwangwala, kuti samafesai, kapena kutemai; alibe nyumba yosungiramo, kapena nkhokwe; ndipo Mulungu awadyetsa; nanga inu simuziposa mbalame kwambiri!

25 Ndipo ndani wa inu, ndi kuda nkhawa angathe kuonjeza mkono pa msinkhu wake?

26 Kotero ngati simungathe ngakhale chaching’onong’ono, muderanji nkhawa chifukwa cha zina zija?

27 Lingalirani maluwa, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito ndi kusapota; koma ndinena kwa inu, Ngakhale Solomoni, mu ulemerero wake wonse sanavale ngati limodzi la awa.

28 Koma ngati Mulungu aveka kotere udzu wakuthengo ukhala lero, ndipo mawa uponyedwa pamoto; nanga inu sadzakuninkhani koposa, inu okhulupirira pang’ono?

29 Ndipo inu musafunefune chimene mudzadya, ndi chimene mudzamwa; ndipo musakayike mtima.

30 Pakuti izi zonse mitundu ya anthu a padziko lapansi amazifunafuna; koma Atate wanu adziwa kuti musowa zimenezi.

31 Komatu tafunafunani Ufumu wake, ndipo izi adzakuonjezerani.

32 Musaopa, kagulu ka nkhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani Ufumu.

33 Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga.

34 Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Fanizo la kapolo wochezera

35 Khalani odzimangira m’chuuno, ndipo nyali zanu zikhale zoyaka;

36 ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.

37 Odala akapolowo amene mbuye wao, pakudza iye, adzawapeza odikira; indetu ndinena ndinu, kuti iye adzadzimangira m’chuuno, nadzawakhalitsa pansi kudya, nadzafika, nadzawatumikira.

38 Ndipo akadza ulonda wachiwiri, kapena wachitatu, nakawapeza atero, odala amenewa.

39 Koma zindikirani ichi, kuti mwini nyumba akadadziwa nthawi yake yakudza mbala, akadadikira, ndipo sakadalola nyumba yake ibooledwe.

40 Khalani okonzeka inunso; chifukwa nthawi imene simulingirira, Mwana wa Munthu akudza.

41 Ndipo Petro anati, Ambuye, kodi fanizo ili mwalinena kwa ife, kapena kwa onse?

42 Ndipo Ambuye anati, Ndani tsono ali mdindo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake adzamuika kapitao wa pa banja lake, kuwapatsa iwo phoso lao pa nthawi yake?

43 Wodala kapoloyo amene mbuye wake pakufika, adzampeza alikuchita chotero.

44 Ndinena ndinu zoona, kuti adzamuika iye kapitao wa pa zonse ali nazo.

45 Koma kapolo uyo akanena mumtima mwake, Mbuye wanga azengereza kudza; ndimo akayamba kupanda anyamata ndi adzakazi ndi kudya ndi kumwa, ndi kuledzera;

46 mbuye wa kapolo uyo adzafika tsiku lakuti samuyembekezera, ndi nthawi yakuti saidziwa, nadzamdula iye pakati nadzamuika dera lake pamodzi ndi anthu osakhulupirira.

47 Ndipo kapolo uyo, wodziwa chifuniro cha mbuye wake, ndipo sanakonze, ndi kusachita zonga za chifuniro chakecho, adzakwapulidwa mikwapulo yambiri.

48 Koma iye amene sanachidziwe, ndipo anazichita zoyenera mikwapulo, adzakwapulidwa pang’ono. Ndipo kwa munthu aliyense adampatsa zambiri, kwa iye adzafuna zambiri; ndipo amene anamuikizira zambiri, adzamuuza abwezere zoposa.

Yesu aponya moto padziko lapansi

49 Ine ndinadzera kuponya moto padziko lapansi; ndipo ndifunanji ngati unatha kuyatsidwa?

50 Koma ndili ndi ubatizo ndikabatizidwe nao; ndipo ndikanikizidwa Ine kufikira ukatsirizidwa!

51 Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere padziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;

52 pakuti kuyambira tsopano adzakhala m’nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

53 Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.

Zizindikiro za nyengo yake

54 Koma Iye ananenanso kwa makamu a anthu, Pamene paliponse muona mtambo wokwera kumadzulo, pomwepo munena, kuti, Ikudza mvula; ndipo itero.

55 Ndipo pamene mphepo ya kumwera iomba, munena, kuti, Kudzakhala kutenthatu; ndipo kuterodi.

56 Onyenga inu, mudziwa kuzindikira nkhope yake ya dziko lapansi ndi ya thambo; koma simudziwa bwanji kuzindikira nyengo ino?

57 Ndipo inunso, pa nokha mulekeranji kuweruza kolungama?

58 Pakuti pamene ulikupita naye mnzako wa mlandu kwa oweruza, fulumira panjira kutha naye mlandu, kuti angakokere iwe kwa oweruza, ndipo oweruzayo angapereke iwe kwa msilikali, ndi msilikali angaponye iwe m’nyumba yandende.

59 Ine ndinena kwa iwe, Sudzatulukamo konse kufikira utalipira kakobiri kukumaliza.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/12-23493812a929ede4ee5f12ee3c0fe5f3.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *