Pemphero la Ambuye
1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m’mene analeka, wina waophunziraake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.
2 Ndipo anati kwa iwo, M’mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze;
3 tipatseni ife tsiku ndi tsiku chakudya cha patsiku.
4 Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa.
Fanizo la bwenzi laliuma
5 Ndipo anati kwa iwo, Ndani wa inu adzakhala ndi bwenzi lake, nadzapita kwa iye pakati pa usiku, nadzati kwa iye, Bwenzi, ndibwereke mikate itatu;
6 popeza wandidzera bwenzi langa lochokera paulendo ndipo ndilibe chompatsa;
7 ndipo iyeyu wa m’katimo poyankha akati, Usandivuta; pakhomo mpotseka tsopano, ndipo ana anga ali nane pamodzi pogona; sindingathe kuuka ndi kukupatsa?
8 Ndinena ndi inu, ngakhale sadzauka ndi kumpatsa, chifukwa ali bwenzi lake, koma chifukwa cha liuma lake adzauka nadzampatsa iye zilizonse azisowa.
9 Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.
10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.
11 Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m’malo mwa nsomba?
12 Kapena akadzampempha dzira kodi adzampatsa chinkhanira?
13 Potero, ngati inu, okhala oipa, mudziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, koposa kotani nanga Atate wanu wa Kumwamba adzapatsa Mzimu Woyera kwa iwo akumpempha Iye?
Za Yesu ndi Belezebulu
14 Ndipo analikutulutsa chiwanda chosalankhula. Ndipo kunali, chitatuluka chiwanda, wosalankhulayo analankhula; ndipo makamu a anthu anazizwa.
15 Koma ena mwa iwo anati, NdiBelezebulumkulu wa ziwanda amatulutsa ziwanda.
16 Koma ena anamuyesa, nafuna kwa Iye chizindikiro chochokera Kumwamba.
17 Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m’kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m’kati mwake igwa.
18 Ndiponso ngatiSatanaagawanika kudzitsutsa mwini, udzaimika bwanji ufumu wake? Popeza munena kuti nditulutsa ziwanda ndi Belezebulu.
19 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.
20 Koma ngati Ine nditulutsa ziwanda ndi chala cha Mulungu, pamenepo Ufumu wa Mulungu wafikira inu.
21 Pamene paliponse mwini mphamvu alonda pabwalo pake zinthu zake zili mumtendere;
22 koma pamene paliponse amdzera wakumposa mphamvu, nakamgonjetsa, amchotsera zida zake zonse zimene anazitama, nagawa zofunkha zake.
23 Iye wosavomerezana ndi Ine atsutsana ndi Ine; ndipo iye wosasonkhanitsa pamodzi ndi Ine amwaza.
24 Pamene paliponse mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, upyola malo opanda madzi nufunafuna mpumulo; ndipo posaupeza unena, Ndidzabwera kunyumba kwanga kumene ndinatulukako;
25 ndipo pofika, uipeza yosesa ndi yokonzeka.
26 Pomwepo upita nutenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoipa yoposa ndi uwu mwini; ndipo ilowa nikhalira komweko; ndipo makhalidwe otsiriza a munthu uyu aipa koposa oyambawo.
27 Ndipo kunali, pakunena izi Iye, mkazi wina mwa khamu la anthu anakweza mau, nati kwa Iye, Yodala mimba imene idakubalani, ndi mawere amene munayamwa.
28 Koma Iye anati, Inde, koma odala iwo akumva mau a Mulungu, nawasunga.
Chizindikiro cha Yona
29 Ndipo pakusonkhana pamodzi makamu a anthu, anayamba kunena, Mbadwo uno ndi mbadwo woipa; ufuna chizindikiro, ndipo chizindikiro sichidzapatsidwa kwa uwu koma chizindikiro cha Yona.
30 Pakuti monga ngati Yona anali chizindikiro kwa Aninive, chotero adzakhalansoMwana wa Munthukwa mbadwo uno.
31 Mfumu yaikazi ya kumwera idzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi amuna a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti anadza kuchokera kumalekezero a dziko kudzamva nzeru za Solomoni; ndipo onani, woposa Solomoni ali pano.
32 Amuna a ku Ninive adzaimirira pa mlandu wotsiriza pamodzi ndi anthu a mbadwo uno, nadzawatsutsa; pakuti iwo analapa pa kulalikira kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano.
Za nyali ya thupi
33 Palibe munthu, atayatsa nyali, aiika m’chipinda chapansi, kapena pansi pa mbiya, koma pa choikapo chake, kuti iwo akulowamo aone kuunika.
34 Nyali ya thupi ndiyo diso lako; pamene paliponse diso lako lili langwiro thupi lako lonse liunikidwanso monsemo; koma likakhala loipa, thupi lako lomwe lili la mdima wokhawokha.
35 Potero yang’anira kuunika kuli mwa iwe kungakhale mdima.
36 Pamenepo, ngati thupi lako lonse liunikidwa losakhala nalo dera lake lamdima, lidzakhala lounikidwa monsemo, ngati pamene nyali ndi kuwala kwake ikuunikira iwe.
Yesu adzudzula Alembi ndi Afarisi
37 Ndipo pakulankhula Iye, anamuitanaMfarisikuti adye naye; ndipo analowa naseama kudya.
38 Ndipo anazizwa Mfarisiyo, pakuona kuti anayamba chakudya asanasambe.
39 Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m’kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa.
40 Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m’kati mwake?
41 Koma patsani mphatso yachifundo za m’katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.
42 Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.
43 Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m’masunagoge, ndi kupatsidwa moni m’misika.
44 Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.
45 Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.
46 Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.
47 Tsoka inu! Chifukwa mumanga za pa manda a aneneri, ndipo makolo anu anawapha.
48 Chomwecho muli mboni, ndipo muvomera ntchito za makolo anu; chifukwa iwotu anawapha, koma inu muwamangira iwo zapamanda.
49 Mwa ichinso nzeru ya Mulungu inati, Ndidzatumiza kwa iwo aneneri ndiatumwi; ndipo ena a iwo adzawapha, nadzawazunza;
50 kuti mwazi wa aneneri onse, wakhetsedwa kuyambira kukhazika kwa dziko lapansi, ukafunidwe kwa anthu a mbadwo uno;
51 kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.
52 Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.
53 Ndipo pamene Iye anatuluka m’menemo, alembi ndi Afarisi anayamba kumuumiriza Iye kolimba, ndi kumfunsa zinthu zambiri;
54 namlindira akakole kanthu kotuluka m’kamwa mwake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LUK/11-2845763e9c31457eda97cf907371e2fd.mp3?version_id=1068—