Za nsembe yopalamula pochimwa dala munthu
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;
3 kapena anapeza chinthu chotayika, nanenapo bodza, nalumbira pabodza; pa chimodzi cha izi zonse amachita munthu, ndi kuchimwapo;
4 pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;
5 kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.
6 Ndipo adze nayo nsembe yake yopalamula kwa Yehova, ndiyo nkhosa yamphongo yopanda chilema ya m’khola mwake, monga umayesa mtengo wake, ikhale nsembe yopalamula, adze nayo kwa wansembe;
7 ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena zilizonse akazichita ndi kupalamula nazo.
Chilamulo cha nsembe yopsereza
8 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,
9 Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m’mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.
10 Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m’mphepete mwa guwa la nsembe.
11 Pamenepo avule zovala zake, navale zovala zina, nachotse phulusa kunka nalo kunja kwa chigono, kumalo koyera.
12 Ndipo moto wa paguwa la nsembe uyakebe pamenepo, wosazima; wansembe ayatsepo nkhuni m’mawa ndi m’mawa; nakonzepo nsembe yopsereza, natenthepo mafuta a nsembe zoyamika.
13 Moto uziyakabe paguwa la nsembe, wosazima.
Chilamulo cha nsembe yaufa
14 Ndipo chilamulo cha chopereka chaufa ndicho: ana a Aroni azibwera nacho pamaso pa Yehova ku guwa la nsembe.
15 Ndipo atengeko wodzala manja pa ufa wa chopereka cha ufa wosalala, ndi pa mafuta ake, ndilubanilonse lili pa chopereka chaufa, nazitenthe paguwa la nsembe, zichite fungo lokoma, ndizo chikumbutso chake cha kwa Yehova.
16 Ndipo chotsalira chake adye Aroni ndi ana ake; achidye chopanda chotupitsa m’malo opatulika; pa bwalo lachihema chokomanakoachidye.
17 Asachiphike ndi chotupitsa. Ndachipereka chikhale gawo lao lochokera pa nsembe zanga zamoto; ndicho chopatulika kwambiri, monga nsembe yauchimo, ndi monga nsembe yopalamula.
18 Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.
Nsembe ya ansembe podzozedwa iwo
19 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,
20 Chopereka cha Aroni ndi ana ake, chimene azibwera nacho kwa Yehova tsiku la kudzozedwa iye ndi ichi: limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale chopereka chaufa kosalekeza, nusu lake m’mawa, nusu lake madzulo.
21 Chikonzeke pachiwaya ndi mafuta; udze nacho chokazinga; chopereka chaufa chazidutsu ubwere nacho, chikhale fungo lokoma la kwa Yehova.
22 Ndipo wansembe wodzozedwa m’malo mwake, wa mwa ana ake, achite ichi; likhale lemba losatha; achitenthe konse kwa Yehova.
23 Ndipo zopereka zaufa zonse za wansembe azitenthe konse; asamazidya.
Chilamulo cha nsembe yauchimo
24 Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,
25 Lankhula ndi Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yauchimo ndi ichi: Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo pophera nsembe yauchimo pamaso pa Yehova; ndiyo yopatulika kwambiri.
26 Ndipo azidya iyi wansembe amene aipereka chifukwa cha zoipa; aidyere m’malo opatulika, pa bwalo la chihema chokomanako.
27 Aliyense akakhudza nyama yake adzakhala wopatulika; ndipo akawaza mwazi wake wina pa chovala chilichonse, utsuke chimene adauwazacho m’malo opatulika.
28 Ndipo mphika wadothi umene anaphikamo nyamayi auswe, koma ngati anaiphika mu mphika wamkuwa, atsuke uwu, nautsukuluze ndi madzi.
29 Amuna onse a mwa ansembe adyeko; ndiyo yopatulika kwambiri.
30 Koma asadye nsembe yauchimo iliyonse, imene amadza nao mwazi wake ku chihema chokomanako kutetezera nao m’malo opatulika; aitenthe ndi moto.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/6-ae8dc593c6f88e91662651c97fe1fbbe.mp3?version_id=1068—