Za nsembe yauchimo pochimwa wansembe
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Munthu akachimwa, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, nakachitapo kanthu;
3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng’ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.
4 Ndipo adze nayo ng’ombeyo ku khomo lachihema chokomanakopamaso pa Yehova; naike dzanja lake pamutu pa ng’ombeyo, naiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova.
5 Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng’ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;
6 ndipo wansembeyo aviike chala chake m’mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.
7 Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m’chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng’ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.
8 Ndipo achotse mafuta onse a ng’ombe ya nsembe yauchimo, achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
9 ndi impso ziwiri ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso,
10 umo azikachotsera pa ng’ombe ya nsembe yoyamika; ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe yopsereza.
11 Natulutse chikopa cha ng’ombeyo, ndi nyama yake yonse, pamodzi ndi mutu wake, ndi miyendo yake, ndi matumbo ake, ndi chipwidza chake,
12 inde ng’ombe yonse, kunja kwa chigono, kunka nayo kumalo koyera, kumene atayako mapulusa, naitenthe pankhuni ndi moto; aitenthe potayira mapulusa.
Za nsembe yauchimo pochimwa mtundu wonse wa Israele
13 Ndipo gulu lonse la Israele likalakwa osati dala, ndipo chikabisika chinthuchi pamaso pa msonkhano, litachita china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, ndi kupalamula;
14 kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng’ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako.
15 Ndipo akulu a khamulo aike manja ao pamutu pa ng’ombeyo, pamaso pa Yehova; naiphe ng’ombeyo pamaso pa Yehova.
16 Ndipo wansembe wodzozedwayo adze nao mwazi wina wa ng’ombeyo ku chihema chokomanako;
17 naviike chala chake m’mwazi wa nsembewo, nauwaze kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova, chakuno cha nsalu yotchinga.
18 Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m’chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.
19 Ndipo achotse mafuta ake onse, nawatenthe paguwa la nsembe.
20 Atero nayo ng’ombeyo; monga umo anachitira ng’ombe ya nsembe yauchimo; ndipo wansembe awachitire chowatetezera, ndipo adzakhululukidwa.
21 Ndipo atulutse ng’ombeyo kunja kwa chigono, ndi kuitentha monga anatenthera ng’ombe yoyamba ija; ndiyo nsembe yauchimo ya kwa msonkhano.
Za nsembe yauchimo pochimwa mkulu
22 Akachimwa mkulu, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova Mulungu wake, napalamula;
23 akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;
24 naike dzanja lake pamutu pa mbuziyo, naiphe pamalo pophera nsembe yopsereza pamaso pa Yehova; ndiyo nsembe yauchimo.
25 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.
26 Ndipo atenthe mafuta ake onse paguwa la nsembe, monga mafuta a nsembe yoyamika; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.
Za nsembe yauchimo pochimwa munthu yekha
27 Ndipo akachimwa wina wa anthu a m’dziko, osati dala, pa china cha zinthu zilizonse aziletsa Yehova, napalamula;
28 akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.
29 Aike dzanja lake pamutu pa nsembe yauchimo, naiphe nsembe yauchimo pamalo pa nsembe yopsereza.
30 Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.
31 Nachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo awatenthe paguwa la nsembe akhale fungo lokoma la kwa Yehova; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhululukidwa.
32 Ndipo akadza nayo nkhosa, ndiyo chopereka chake, ikhale nsembe yauchimo, azidza nayo yaikazi, yopanda chilema.
33 Naike dzanja lake pamutu wa nsembe yauchimo, ndi kuipha ikhale nsembe yauchimo pamalo pophera nsembe yopsereza.
34 Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;
35 nawachotse mafuta ake onse, monga umo amachotsera mafuta a nkhosa pa nsembe yoyamika; ndipo wansembeyo atenthe awa paguwa la nsembe, monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pa kuchimwa kwake adakuchimwira, ndipo adzakhululukidwa.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/4-bba5afa812842cfceb4b415d57aac9c1.mp3?version_id=1068—