Za nsembe yoyamika
1 Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng’ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.
2 Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata chachihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.
3 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
4 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.
5 Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.
6 Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;
7 akabwera nayo nkhosa kuti ikhale chopereka chake, abwere nayo pamaso pa Yehova;
8 naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.
9 Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova; yotengako ku nsembe yoyamika; mafuta ake, mchira wamafuta wonse, atauchotsa kufupi ku fupa la msana; naichotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
10 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.
11 Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.
12 Ndipo chopereka chake chikakhala mbuzi, azibwera nayo pamaso pa Yehova;
13 naike dzanja lake pamutu pake, naiphe pa khomo la chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.
14 Ndipo abwere nacho chopereka chake chotengako, ndicho nsembe yamoto ya kwa Yehova; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,
15 ndi impso ziwiri, ndi mafuta ali pomwepo, okhala m’chuuno, ndi chokuta cha mphafa chofikira kuimpso.
16 Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.
17 Likhale lemba losatha m’mibadwo yanu m’nyumba zanu zonse, musamadya kapena mafuta kapena mwazi.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/3-71dd31a1ca0c0ac9186cc3e776eb3866.mp3?version_id=1068—