Chowinda ndi chiombolo chake
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Pamene munthu achita chowinda cha padera, anthuwo azikhala a Yehova monga mwa kuyesa kwako.
3 Ukayesa wamwamuna wa zaka makumi awiri kufikira wina wa zaka makumi asanu ndi limodzi, uziwayesera a masekeli makumi asanu asiliva, monga mwa sekeli wa malo opatulika.
4 Koma akakhala wamkazi, umuyesere wa masekeli makumi atatu.
5 Akakhala munthu wa zaka zisanu kufikira wina wa zaka makumi awiri uwayesere, wamwamuna wa masekeli makumi awiri, ndi wamkazi wa masekeli khumi.
6 Akakhala mwana wa mwezi umodzi kufikira zaka zisanu, uziwayesera wamwamuna wa masekeli asanu a siliva, ndi wamkazi wa masekeli atatu a siliva.
7 Akakhala munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi mphambu, akakhala wamwamuna, umuyesere wa masekeli khumi ndi asanu, akakhala wamkazi wa masekeli khumi.
8 Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.
9 Ndipo chikakhala cha nyama imene anthu amabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, zonse zotere munthu akazipereka kwa Yehova zikhale zopatulika.
10 Asaisinthe, yokoma m’malo mwa yoipa, kapena yoipa m’malo mwa yokoma; ndipo akasinthadi nyama m’malo mwa inzake, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika.
11 Ndipo chikakhala cha nyama yodetsa, imene sabwera nayo ikhale chopereka cha Yehova, aike nyamayi pamaso pa wansembe;
12 ndipo wansembeyo aiyese mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga uiyesa wansembewe, momwemo.
13 Ndipo akaiombola ndithu, pamenepo aonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake.
14 Munthu akapatula nyumba yake ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe aziiyesa mtengo wake, ingakhale yokoma kapena yoipa; monga wansembeyo aiyesa, ikhale momwemo.
15 Ndipo iye wakuipatula akaombola nyumba yake, aonjezepo limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo idzakhala yake.
16 Munthu akapatulirako Yehova munda wakewake, uziuyesa monga mwa mbeu zake zikakhala; homeri wa barele uuyese wa masekeli makumi asanu a siliva.
17 Akapatula munda wake kuyambira chaka choliza lipenga, mundawo ukhale monga momwe unauyesera.
18 Akaupatula munda wake chitapita chaka choliza lipenga, wansembe azimwerengera ndalama monga mwa zaka zotsalira kufikira chaka choliza lipenga, nazichepsako pa kuyesa kwako.
19 Ndipo wakupatula mundayo akauomboladi, aonjezeko limodzi la magawo asanu la ndalama za kuyesa kwako, ndipo uzikhalitsa wake.
20 Koma akapanda kuombola mundawo, kapena atagulitsa mundawo kwa munthu wina, suomboledwanso;
21 koma potuluka m’chaka choliza lipenga, mundawo ukhale wopatulikira Yehova, ngati munda woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; ukhale wakewake wa wansembe.
22 Ndipo akapatulira Yehova munda woti adaugula, wosati wogawako ku munda wakewake;
23 pamenepo wansembeyo amwerengere mtengo wake wa kuyesa kwako kufikira chaka choliza lipenga; ndipo apereke kuyesa kwako tsiku lomwelo, chikhale chinthu chopatulikira Yehova.
24 Chaka choliza lipenga mundawo ubwerere kwa iye amene adaugulitsa, kwa iye amene dzikoli ndi lakelake.
25 Ndipo kuyesa kwako konse kukhale monga mwa sekeli wa malo opatulika sekeli ndi magera makumi awiri.
26 Komatu woyamba kubadwa mwa nyama akhale wobadwa woyamba wa Yehova, munthu asampatule; ingakhale ng’ombe ingakhale nkhosa, ndiye wa Yehova.
27 Koma akakhala wa nyama zodetsa, azimuombola monga mwa kuyesa kwako, naonjezepo limodzi la magawo asanu la mtengo wake; ndipo akapanda kumuombola, amgulitse monga mwa kuyesa kwako.
Za choperekedwa chiperekere, ndi lakhumi la za nthaka ndi za m’khola
28 Koma asachigulitse kapena kuchiombola chinthu choperekedwa chiperekere kwa Mulungu, chimene munthu achipereka chiperekere kwa Yehova, chotengako ku zonse ali nazo, ngakhale munthu, kapena nyama, kapena munda wakewake; chilichonse choperekedwa chiperekere kwa Mulungu nchopatulika kwambiri.
29 Asamuombole munthu woperekedwa chiperekere kwa Mulungu; amuphe ndithu.
30 Limodzi mwa magawo khumi la zonse m’dziko, la mbeu zake za dziko, la zipatso za mtengo, ndilo la Yehova; likhale lopatulikira Yehova.
31 Koma munthu akaombolatu kanthu ka limodzi la magawo khumiwo aonjezeko limodzi la magawo asanu.
32 Ndipo limodzi la magawo khumi lonse la ng’ombe, kapena la nkhosa, kapena la mbuzi, zilizonse zimapita pansi pa ndodo, limodzi la magawo khumi likhala lopatulikira Yehova.
33 Asafunse ngati yabwino kapena yoipa, kapena kuisintha; koma akaisinthatu, pamenepo iyo ndi yosinthikayo zikhale zopatulika zonse ziwiri; asamaiombola.
34 Awa ndi malamulo, amene Yehova analamula Mose, awauze ana a Israele, m’phiri la Sinai.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/27-a285716b27d48e26454d0e64634e00c4.mp3?version_id=1068—