Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 25

Za chaka chopumula dziko

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose m’phiri la Sinai, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m’dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira YehovaSabata.

3 Zaka zisanu ndi chimodzi ubzale m’munda mwako, ndi zaka zisanu ndi chimodzi udzombole mpesa zako, ndi kucheka zipatso zake;

4 koma chaka chachisanu ndi chiwiri chikhale Sabata lakupumula la dziko, Sabata la Yehova; usamabzala m’munda mwako, usamadzombola mipesa yako.

5 Zophuka zokha zofikira masika usamazithyola, ndi mphesa za mipesa yako yosadzombola usazicheka; chikhale chaka chopumula dziko.

6 Ndipo Sabata la dzikoli likhale kwa inu la chakudya; kwa iwe, ndi mnyamata wako, ndi mdzakazi wako, ndi wolembedwa ntchito yako, ndi mlendo wako wakugonera kwanu;

7 ndi ng’ombe zako, ndi nyama zili m’dziko lako; zipatso zake zonse zikhale chakudya chao.

Za chaka choliza lipenga

8 Ndipo uziwerengera masabata a zaka asanu ndi awiri, zaka zisanu ndi ziwiri kasanu ndi kawiri; kotero kuti zaka za masabata a zaka asanu ndi awiri, zifikire zaka makumi anai kudza zisanu ndi zinai.

9 Pamenepo uzitumizira lipenga lomveka m’mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi la mweziwo; tsiku la chitetezero mutumizire lipenga lifikire m’dziko lanu lonse.

10 Ndipo muchipatule chaka cha makumi asanu, ndi kulalikira kwa onse okhala m’dzikomo kuti akhale aufulu; muchiyese chaka choliza lipenga; ndipo mubwerere munthu aliyense ku zakezake, ndipo mubwerere yense ku banja lake.

11 Muchiyese chaka cha makumi asanucho choliza lipenga, musamabzala, kapena kucheka zophuka zokha m’mwemo; kapena kucheka mphesa zake za mipesa yosadzombola.

12 Popeza ndicho chaka choliza lipenga; muchiyese chopatulika, mudye zipatso zake kunja kwa munda.

13 Chaka choliza lipenga ichi mubwerere nonse ku zakezake.

14 Ndipo ukagulitsa kanthu kwa mnansi wako, kapena kugula kanthu ka mnansi wako, musamasautsana;

15 monga mwa kuwerenga kwake kwa zaka, chitapita choliza lipenga, uzigula kwa mnansi wako, ndi monga mwa kuwerenga kwa zaka za zipatso azigulitsa.

16 Monga mwa kuchuluka kwa zaka zake uonjeze mtengo wake, ndi monga mwa kuchepa kwa zaka zake uchepetse mtengo wake; pakuti akugulitsa powerenga masiku ake.

17 Musamasautsana, koma uope Mulungu wako; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

18 M’mwemo muchite malemba anga, ndi kusunga maweruzo anga, ndi kuwachita; ndipo mudzakhala m’dzikomo okhazikika.

19 Dziko lidzaperekanso zipatso zake, ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kukhalamo okhazikika.

20 Ndipo mukadzati, Tidzadyanji chaka chachisanu ndi chiwiri? Taonani, sitidzabzala, sitidzakolola dzinthu;

21 pamenepo ndidzauza dalitso langa litsike pa inu chaka chachisanu ndi chimodzi, ndipo chidzapatsa zipatso zofikira zaka zitatu.

22 Ndipo mubzale chaka chachisanu ndi chitatu, ndi kudya zipatso zasundwe; kufikira chaka chachisanu ndi chinai, mpaka zitacha zipatso zake mudzadya zasundwe.

Za kuombola dziko ndi nyumba

23 Ndipo asaligulitse dziko chigulitsire; popeza dzikoli ndi langa; pakuti inu ndinu alendo akugonera ndi Ine.

24 Potero muzilola liomboledwe dziko lonse muli nalo.

25 Mbale wako akasaukira chuma, nakagulitsa chakechake, pamenepo mombolo wake, mbale wake weniweni azidza, naombole chimene mbale wake anagulitsacho.

26 Ndipo munthu akasowa mombolo, koma dzanja lake lachionetsa, nachipeza chofikira kuchiombola;

27 pamenepo awerenge zaka za kugulitsa kwake, nabwezere wogulayo zotsalirapo nabwerere iye ku dziko lake.

28 Koma dzanja lake likapanda kupeza zofikira za kumbwezera, pamenepo chogulitsacho chikhale m’dzanja lake la iye adachigulayo, kufikira chaka choliza lipenga; koma chaka choliza lipenga chituluke, nabwerere iye ku dziko lake.

29 Munthu akagulitsa nyumba yogonamo, m’mzinda wa m’linga, aiombole chisanathe chaka choigulitsa; kufikira kutha chaka akhoza kuombola.

30 Ndipo akapanda kuiombola kufikira kutha kwake kwa chaka champhumphu, nyumba ili m’mzinda wa m’lingayi idzakhala yake ya iye adaigula yosamchokeranso mwa mibadwo yake; siidzatuluka chaka choliza lipenga.

31 Koma nyumba za m’midzi yopanda linga aziyese monga minda ya m’dziko; ziomboledwe, zituluke m’chaka choliza lipenga.

32 Kunena za mizinda ya Alevi, nyumba za m’mizinda yaoyao, Alevi akhoza kuziombola nthawi zonse.

33 Ndipo munthu akagula kwa Mlevi, nyumba yogulayo yokhala m’mzinda wakewake, ituluke m’chaka choliza lipenga, popeza nyumba za m’mizinda ya Alevi ndizo zaozao mwa ana a Israele.

34 Koma dambo la podyera pao siligulika; popeza ndilo laolao kosatha.

35 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.

36 Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.

37 Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera.

38 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m’dziko la Ejipito, kukupatsani dziko la Kanani, kuti ndikhale Mulungu wanu.

Za mbale wodzigulitsa akhale kapolo

39 Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi kudzigulitsa kwa iwe; usamamgwiritsa ntchito monga kapolo;

40 azikhala nawe ngati wolipidwa ntchito, ngati mlendo wako; akutumikire kufikira chaka choliza lipenga.

41 Pamenepo azituluka kukuchokera, iye ndi ana ake omwe, nabwerere ku mbumba yake; abwerere ku dziko laolao la makolo ake.

42 Pakuti iwo ndiwo atumiki anga, amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; asamawagulitsa monga amagulitsa kapolo.

43 Usamamweruza momzunza; koma uope Mulungu wako.

44 Kunena za kapolo wako wamwamuna, kapena wamkazi amene ukhala nao; azikhala aamitunduakuzungulira inu, kwa iwowa muzigula akapolo aamuna ndi aakazi.

45 Muwagulenso ana a alendo akukhala mwa inu, a iwowa ndi a mabanja ao akukhala nanu, amene anabadwa m’dziko lanu; ndipo adzakhala anuanu.

46 Ndipo muwayese cholowa cha ana anu akudza m’mbuyo, akhale aoao; muwayese akapolo kosatha; koma za abale anu, ana a Israele, musamalamulirana mozunza.

47 Ndipo mlendo wakugonera kwanu akalemera chuma, ndi mbale wako wakukhala naye akasauka, nadzigulitsa kwa mlendo wakugonera kwanu, kapena kwa fuko la banja la mlendo;

48 atatha kudzigulitsa, aomboledwe; wina wa abale ake amuombole;

49 kapena mbale wa atate wake, kapena mwana wa mbale wa atate wake amuombole, kapena mbale wake aliyense wa banja lake amuombole; kapena akalemera chuma yekha adziombole yekha.

50 Ndipo awerengere amene anamgulayo kuyambira chaka adadzigulitsa kwa iye kufikira chaka choliza lipenga; ndipo mtengo wake ukhale monga mwa kuwerenga kwa zaka; amuyesere monga masiku a munthu wolipidwa.

51 Zikamtsalira zaka zambiri, monga mwa izi abwezere ndalama zakumuombola zochokera ku ndalama zomgulazo.

52 Ndipo zikamtsalira zaka pang’ono kufikira chaka choliza lipenga amwerengere; monga mwa zaka zake abwezere mtengo wake wakumuombola.

53 Akhale naye monga wolipidwa chaka ndi chaka; asamamlamulira momzunza pamaso pako.

54 Ndipo akapanda kumuombola motero, azituluka chaka choliza lipenga, iye ndi ana ake omwe.

55 Pakuti ana a Israele ndi atumiki anga; iwo ndiwo atumiki anga amene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/25-e056d396e53fb7fe0389a3bf17133017.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *