Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 23

Za nyengo zoikika za Yehova

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Nyengo zoikika za Yehova zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, ndizo nyengo zanga zoikika.

3 Masiku asanu ndi limodzi azigwira ntchito; koma lachisanu ndi chiwiri ndiloSabatalakupumula, msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito konse; ndilo Sabata la Yehova m’nyumba zanu zonse.

Paska

4 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, misonkhano yopatulika, zimene muzilalikira pa nyengo zoikika zao.

5 Mwezi woyamba, tsiku lakhumi ndi chinai la mweziwo, madzulo, paliPaskawa Yehova.

6 Ndipo tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi womwewo ndilochikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsaa Yehova; masiku asanu ndi awiri muzidya mkate wopanda chotupitsa.

7 Tsiku lake loyamba mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena.

8 Koma mubwere nayo kwa Yehova nsembe yamoto masiku asanu ndi awiri; pa tsiku lachisanu ndi chiwiri pakhale msonkhano wopatulika; musamachita ntchito ya masiku ena.

Zipatso zoyamba

9 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

10 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m’dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;

11 ndipo iye aweyule mtolowo pamaso pa Yehova, ulandirikire inu, tsiku lotsata Sabata wansembe aweyule.

12 Ndipo tsiku loweyula mtolowo, ukonzemwanawankhosawopanda chilema, wa chaka chimodzi, akhale nsembe yopsereza ya Yehova.

13 Ndipo nsembe yaufa yake ikhale awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, ndiyo nsembe yamoto ya Yehova, ichite fungo lokoma; ndi nsembe yake yothira ikhale yavinyo, limodzi la magawo anai la hini.

14 Musamadya mkate, kapena tirigu wokazinga, kapena ngala zaziwisi, kufikira tsiku lomweli, kufikira mutadza nacho chopereka cha Mulungu wanu; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu m’nyumba zanu zonse.

15 Ndipo mudziwerengere kuyambira tsiku lotsata Sabata, kuyambira tsikuli mudadza nao mtolo wansembe yoweyula; pakhale masabata asanu ndi awiri amphumphu;

16 muwerenge masiku makumi asanu kufikira tsiku lotsata sabata lachisanu ndi chiwiri; pamenepo mubwere nayo kwa Yehova nsembe ya ufa watsopano.

17 Mutuluke nayo m’zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.

18 Ndipo mubwere nao pamodzi ndi mikate, anaankhosa asanu ndi awiri, opanda chilema a chaka chimodzi, ndi ng’ombe yamphongo imodzi, ndi nkhosa zamphongo ziwiri; zikhale nsembe yopsereza ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yao yaufa, ndi nsembe zao zothira, ndizo nsembe yamoto ya fungo lokoma la Yehova.

19 Mukonzenso mwanawambuzi mmodzi akhale nsembe yauchimo, ndi anaankhosa awiri a chaka chimodzi akhale nsembe yoyamika.

20 Ndi wansembe awaweyule, pamodzi ndi mkate wa zipatso zoyamba, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova, pamodzi ndi anaankhosa awiriwo; zikhale zopatulikira Yehova, kuti zikhale za wansembe.

21 Ndipo mulalikire tsiku lomwelo; kuti mukhale nao msonkhano wopatulika; musamagwira ntchito ya masiku ena; ndilo lemba losatha m’nyumba zanu zonse, mwa mibadwo yanu yonse.

22 Ndipo pakukolola dzinthu za m’dziko mwanu, usamakololetsa m’mphepete mwa munda wako, nusamakunkha khunkha; uzisiyire wosauka ndi mlendo; Ine ndine Yehova Mulungu wako.

23 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

24 Nena ndi ana a Israele, ndi kuti, Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku loyamba la mweziwo, muzipumula, ndiko chikumbutso cha kuliza malipenga, msonkhano wopatulika.

25 Musamagwira ntchito ya masiku ena; mubwere nayo nsembe yamoto ya Yehova.

Tsiku la chitetezero

26 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

27 Komatu, tsiku lakhumi la mwezi uwu wachisanu ndi chiwiri, ndilo tsiku la chitetezero; mukhale nao msonkhano wopatulika, ndipo mudzichepetse; ndi kubwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova.

28 Musamagwira ntchito iliyonse tsiku limenelo; pakuti ndilo tsiku la chitetezero, kuchita chotetezera inu pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29 Pakuti munthu aliyense wosadzichepetsa tsiku limenelo, amsadze kwa anthu a mtundu wake.

30 Ndi munthu aliyense wakugwira ntchito iliyonse tsiku limenelo, ndidzaononga munthuyo pakati pa anthu a mtundu wake.

31 Musamagwira ntchito iliyonse; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu, m’nyumba zanu zonse.

32 Likhale ndi inu Sabata lakupumula; ndipo mudzichepetse; tsiku lachisanu ndi chinai madzulo, kuyambira madzulo kufikira madzulo musunge Sabata lanu.

Chikondwerero cha Misasa

33 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,

34 Nena ndi ana a Israele, kuti, Tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi uno wachisanu ndi chiwiri palichikondwerero cha Misasaya Yehova, masiku asanu ndi awiri.

35 Tsiku loyamba likhale msonkhano wopatulika, musamagwira ntchito ya masiku ena.

36 Masiku asanu ndi awiri mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; tsiku lachisanu ndi chitatu mukhale nao msonkhano wopatulika; ndipo mubwere nayo nsembe yamoto kwa Yehova; ndilo lotsirizira; musamagwira ntchito ya masiku ena.

37 Izi ndi nyengo zoikika za Yehova, zimene muzilalikira zikhale misonkhano yopatulika, kukabwera nayo nsembe yamoto kwa Yehova, nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa, nsembe yophera, ndi nsembe yothira, yonse pa tsiku lakelake;

38 pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.

39 Koma tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mutatuta zipatso za m’dziko, muzisunga chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri; tsiku loyamba mupumule, ndi tsiku lachisanu ndi chitatu mupumule.

40 Ndipo tsiku loyambali mudzitengere nthambi za mitengo yokoma, nsomo za kanjedza, ndi nthambi za mitengo yovalira, ndi misondodzi ya kumtsinje; ndipo mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu masiku asanu ndi awiri.

41 Ndipo musunge chikondwerero cha Yehova masiku asanu ndi awiri m’chaka; ndilo lemba losatha mwa mibadwo yanu; musunge mwezi wachisanu ndi chiwiri.

42 Mukhale m’misasa masiku asanu ndi awiri; onse obadwa m’dziko la Israele akhale m’misasa;

43 kuti mibadwo yanu ikadziwe kuti ndinakhalitsa ana a Israele m’misasa, pamene ndinawatulutsa m’dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

44 Ndipo Mose anafotokozera ana a Israele nyengo zoikika za Yehova.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/23-03d2b1e86ffff569a7652348a628cd3f.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *