Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 18

Malamulo a pa ulemu

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,

2 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

3 Musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Ejipito, muja munakhalamo; musamachita monga mwa machitidwe a dziko la Kanani kumene ndipita nanuko, nimusamayenda m’malemba ao.

4 Muzichita maweruzo anga, ndi kusunga malemba anga, kumayenda m’mwemo; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

5 Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.

6 Asasendere mmodzi wa inu kwa mbale wake kumvula; Ine ndine Yehova.

7 Usamavula atate wako, ndi mai wako; ndiye mai wako, usamamvula.

8 Usamavula mkazi wa atate wako; ndiye thupi la atate wako.

9 Usamavula mlongo wako, mwana wamkazi wa atate wako, kapena mwana wamkazi wa mai wako, wobadwa kwanu, kapena wobadwa kwina.

10 Usamavula mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wako, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wako; pakuti thupi lao ndi lako.

11 Usamavula mwana wamkazi wa mkazi wa atate wako, amene anambala atate wako, ndiye mlongo wako.

12 Usamavula mlongo wa atate wako; ndiye wa chibale cha atate wako.

13 Usamavula mbale wa mai wako; popeza ndiye mbale wa mai wako.

14 Usamavula mbale wa atate wako; usamasendera kwa mkazi wake; ndiye mai wako.

15 Usamavula mpongozi wako; ndiye mkazi wa mwana wamwamuna wako; usamamvula.

16 Usamavula mkazi wa mbale wako; ndiye thupi la mbale wako.

17 Usamavula mkazi ndi mwana wamkazi wake; usamatenga mwana wamkazi wa mwana wamwamuna wake, kapena mwana wamkazi wa mwana wamkazi wake kumvula; ndiwo abale; chochititsa manyazi ichi.

18 Usamtenga mkazi kumuonjezera kwa mbale wake, kumvula, kumvula pamodzi ndi mnzake, akali ndi moyo mnzakeyo.

19 Usamasendera kwa mkazi kumvula pokhala ali padera chifukwa cha kudetsedwa kwake.

20 Usagona naye mkazi wa mnansi wako, kudetsedwa naye limodzi.

21 Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa chaMoleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

22 Usamagonana ndi mwamuna, monga amagonana ndi mkazi; chonyansa ichi.

23 Ndipo usamagonana ndi nyama iliyonse, kudetsedwa nayo; kapena mkazi asamaima panyama, kugonana nayo; chisokonezo choopsa ichi.

24 Musamadzidetsa nacho chimodzi cha izi; pakutiamitunduamene ndiwapirikitsa pamaso panu amadetsedwa nazo zonsezi;

25 dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m’mwemo.

26 Koma inu, muzisunga malemba anga ndi maweruzo anga, osachita chimodzi chonse cha zonyansa izi; ngakhale wa m’dziko ngakhale mlendo wakugonera pakati pa inu.

27 (Pakuti eni dziko okhalako, musanafike inu, anazichita zonyansa izi zonse, ndi dziko linadetsedwa)

28 lingakusanzeni inunso dzikoli, polidetsa inu, monga linasanza mtundu wa anthu wokhalako musanafike inu.

29 Pakuti aliyense akachita chilichonse cha zonyansa izi, inde amene azichita adzachotsedwa pakati pa anthu a mtundu wao.

30 Potero muzisunga chilangizo changa, ndi kusachita zilizonse za miyambo yonyansayi anaichita musanafike inu, ndi kusadzidetsa nayo: Ine ndine Yehova Mulungu wako.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/18-e8b4ea68235ca78f2defb92a03425d3d.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *