Popereka nsembe
1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2 Nena ndi Aroni, ndi ana ake aamuna, ndi ana a Israele onse, nuti nao, Ichi ndi chimene Yehova wauza, ndi kuti,
3 Munthu aliyense wa mbumba ya Israele akapha ng’ombe, kapenamwanawankhosa, kapena mbuzi, m’chigono, kapena akaipha kunja kwa chigono,
4 osadza nayo ku khomo lachihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;
5 kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.
6 Ndipo wansembeyo awaze mwaziwo paguwa la nsembe la Yehova, pa khomo la chihema chokomanako, natenthe mafuta akhale fungo lokoma lokwera kwa Yehova.
7 Ndipo asamapheranso milungu ina nsembe zao, zimene azitsata ndi chigololo. Ili liwakhalire lemba losatha mwa mibadwo yao.
8 Ndipo uzinena nao, Munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wakugonera pakati panu, amene apereka nsembe yopsereza kapena nsembe yophera,
9 osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuiphera Yehova; amsadze munthuyu kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
Aletsedwa kudya mwazi
10 Ndipo munthu aliyense wa mbumba ya Israele, kapena mlendo wogonera pakati panu, wakudya mwazi uliwonse; nkhope yanga idzatsutsana naye munthu wakudya mwaziyo, ndi kumsadza kumchotsa kwa anthu a mtundu wake.
11 Pakuti moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa la nsembe, uchite chotetezera moyo wanu; pakuti wochita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake.
12 Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu, kapena mlendo aliyense wakugonera mwa inu asamadya mwazi.
13 Ndipo munthu aliyense wa ana a Israele, kapena mlendo wakugonera pakati pa inu, akasaka nyama kapena mbalame yakudya, nakaigwira; azikhetsa mwazi wake, naufotsere ndi dothi.
14 Pakuti ndiwo moyo wa nyama zonse, mwazi wake ndiwo moyo wake; chifukwa chake ndinanena kwa ana a Israele, Musamadya mwazi wa nyama iliyonse; pakuti moyo wa nyama yonse ndi mwazi wake; aliyense akaudya adzachotsedwa.
15 Ndipo aliyense wakudya yakufa yokha, kapena yojiwa kuthengo, ngakhale ndiye wa m’dziko kapena mlendo, azitsuka nsalu zake, nasambe ndi madzi, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; pamenepo adzakhala woyera.
16 Koma akapanda kuzitsuka, kapena kusamba thupi lake, adzasenza mphulupulu yake.
—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/17-ffa03bba4158ccf6aea2c54bc7e4aad3.mp3?version_id=1068—