Categories
LEVITIKO

LEVITIKO 13

Malamulo a pa nthenda yakhate

1 Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,

2 Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhatepa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;

3 ndipo wansembe aione nthenda pa khungu la thupi; ndipo ngati tsitsi la panthenda lasanduka la mbuu, ndi nthenda ikaoneka yapitirira khungu la thupi lake, ndiyo nthenda yakhate; ndipo wansembe amuone, namutche wodetsedwa.

4 Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;

5 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirire pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

6 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;

7 koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsa kwa wansembe kuti atchedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;

8 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nkhanambo yapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa, ndilo khate.

9 Pamene nthenda yakhate ili mwa munthu, azimfikitsa kwa wansembe;

10 ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati pali chotupa choyera pakhungu, ndipo chasanduliza tsitsi likhale loyera, ndipo pachotupa pali mnofu wofiira,

11 ndilo khate lakale pa khungu la thupi lake, ndipo wansembe amutche wodetsedwa; asambindikiretse popeza ali wodetsedwa.

12 Ndipo ngati khate libukabuka pakhungu, ndi khate lakuta khungu lonse la wanthendayo kuyambira mutu wake kufikira mapazi ake, monga momwe apenyera wansembe;

13 pamenepo wansembe aone, ndipo taonani, ngati khate lakuta thupi lake, amutche woyera wanthendayo; patuwa ponsepo; ndiye woyera.

14 Koma tsiku lililonse ukaoneka pa iye mnofu wofiira, adzakhala wodetsedwa.

15 Ndipo wansembe aone mnofu wofiirawo, namutche wodetsedwa; mnofu wofiira ndiwo wodetsa; ndilo khate.

16 Kapena mnofu wofiira ukasandukanso, nusandulika wotuwa, afike kwa wansembe,

17 ndi wansembe amuone, ndipo taonani, ngati nthenda yasandulika yotuwa, wansembe amutche woyera wanthendayo; ndiye woyera.

18 Ndipo pamene thupi lili ndi chilonda pakhungu pake, ndipo chapola,

19 ndipo padali chilonda pali chotupa choyera, kapena chikanga chotuuluka, pamenepo achionetse kwa wansembe; ndipo wansembe aone,

20 ndipo taonani, ngati chioneka chakumba kubzola khungu, ndipo tsitsi lake lisanduka lotuwa, pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate yabuka m’chilondamo.

21 Koma wansembe akachiona, ndipo taonani, palibe tsitsi loyera pamenepo, ndipo sichinakumbe kubzola khungu, koma chazimba, pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

22 ndipo ngati chapitirira khungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndilo khate.

23 Koma ngati chikanga chaima pomwepo, chosakula, ndicho chipsera cha chilonda; ndipo wansembe amutche woyera.

24 Kapena pamene thupi lidapsa ndi moto pakhungu pake, ndipo mnofu wofiira wakupsawo usanduka chikanga chotuuluka, kapena chotuwa;

25 pamenepo wansembe achione; ndipo taonani, ngati tsitsi la chikanga lasanduka lotuwa, ndipo chioneka chakumba kubzola khungu; pamenepo ndilo khate lobuka m’kupsamo; ndipo wansembe azimutcha wodetsedwa ndi nthenda yakhate.

26 Koma akaonapo wansembe, ndipo taonani, mulibe tsitsi loyera m’chikangamo, ndipo sichikumba kubzola khungu, koma chazimba; pamenepo wansembe ambindikiritse masiku asanu ndi awiri;

27 ndipo wansembe amuone tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati chakula pakhungu, wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo nthenda yakhate.

28 Ndipo ngati chikanga chiima pomwepo, chosakula pakhungu koma chazimba; ndicho chotupa chakupsa; ndipo wansembe amutche woyera; pakuti ndicho chipsera chakupsa.

29 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi nthenda pamutu kapena pandevu,

30 wansembe aziona nthenda; ndipo taonani, ngati ioneka yokumba kubzola khungu, ndipo pali tsitsi loyezuka lotetemera; pamenepo wansembe amutche wodetsedwa; ndiyo mfundu, ndilo khate la mutu kapena ndevu.

31 Ndipo wansembe akaona nthenda yamfundu, ndipo taonani, ioneka yosakumba kubzola khungu, ndipo palibe tsitsi lakuda pamenepo, wansembe ambindikiritse iye ali ndi mfundu masiku asanu ndi awiri;

32 ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe aone nthendayi; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula, ndipo mulibe tsitsi loyezuka, ndipo mfundu ikaoneka yosakumba kubzola khungu,

33 pamenepo azimeta, koma osameta pamfundu; ndipo wansembe ambindikiritse iye wamfundu masiku asanu ndi awiri ena;

34 ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri aone mfunduyo; ndipo taonani, ngati mfundu njosakula pakhungu, ndipo ioneka yosakula kubzola khungu, wansembe amutche woyera, ndipo iye atsuke zovala zake, nakhala woyera.

35 Koma ngati mfundu ikula pakhungu atatchedwa woyera;

36 pamenepo wansembe amuone, ndipo taonani, ngati mfundu yakula pakhungu, wansembe asafunefune tsitsi loyezuka, ndiye wodetsedwa.

37 Koma monga momwe apenyera iye, ngati mfundu yaima pomwe, ndipo pamera tsitsi lakuda, mfundu yapola, ndiye woyera, ndipo wansembe amutche woyera.

38 Ndipo ngati mwamuna kapena mkazi ali ndi zikanga pa khungu la thupi lake, zikanga zoyerayera;

39 wansembe aziona; ndipo taonani ngati zikanga zili pa khungu la thupi lao zikhala zotuwatuwa; ndilo thuza labuka pakhungu; ndiye woyera.

40 Ndipo ngati tsitsi la munthu lathothoka, ndiye wadazi; koma woyera.

41 Ndipo ngati tsitsi lathothoka pamphumi pake ndiye wa masweswe, koma woyera.

42 Koma ngati pali nthenda yotuuluka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi, ndipo khate lilikubuka pakati pa dazi lake la pamutu, kapena la pamphumi.

43 Pamenepo wansembe azimuona, ndipo taonani, ngati chotupa chake cha nthenda chili chotuuluka pa dazi la pamutu wake, kapena la pamphumi pake, monga maonekedwe a khate pa khungu la thupi;

44 ndiye wakhate, ndiye wodetsedwa; wansembe amutchetu wodetsedwa; nthenda yake ili pamutu pake.

45 Ndipo azing’amba zovala zake za wakhate ali ndi nthendayo, ndi tsitsi la pamutu pake lizikhala lomasuka, naphimbe iye mlomo wake wa m’mwamba, nafuule, Wodetsedwa, wodetsedwa!

46 Masiku onse nthenda ikali pa iye azikhala wodetsedwa; ali wodetsedwa, agone pa yekha pokhala pake pakhale kunja kwa chigono.

47 Ndiponso ngati nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya, kapena chathonje;

48 ngakhale ili pamuyaro, kapena pamtsendero, chathonje, kapena chaubweya, ngakhale ili pa chikopa, kapena pa chinthu chilichonse chopanga ndi chikopa;

49 ngati nthenda ili yobiriwira, kapena yofiira pachovala, kapena pachikopa, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ndiyo nthenda yakhate; aziionetsa kwa wansembe;

50 ndipo wansembe aone nthendayo, nabindikiritse chija cha nthenda masiku asanu ndi awiri;

51 naone nthenda tsiku lachisanu ndi chiwiri; ngati nthenda yakula pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pachikopa, zilizonse zantchito zopangika ndi chikopa; nthendayo ndiyo khate lofukuta; ndicho chodetsedwa.

52 Ndipo atenthe chovalacho ngakhale muyaro wake, ngakhale mtsendero wake, chaubweya kapena chathonje, kapena chilichonse chachikopa chili ndi khate, ndilo khate lofetsa; achitenthe ndi moto.

53 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda njosakula pachovala, kapena pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa;

54 pamenepo wansembe aziuza kuti atsuke chija pali khate, nachibindikiritse masiku asanu ndi awiri ena;

55 ndipo wansembe aone nthenda ataitsuka, ndipo taonani, ngati nthendayi siinasandulike maonekedwe ake, yosakulanso nthenda, ndicho chodetsedwa; uchitenthe ndi moto; ndilo funka, kungakhale kuyera kwake kuli patsogolo kapena kumbuyo.

56 Ndipo wansembe akaona, ndipo taonani, nthenda yazimba ataitsuka, pamenepo aikadzule pa chovala, kapena chikopa, kapena muyaro, kapena mtsendero;

57 ndipo ikaonekabe pachovala, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ilikubukanso; uchitenthe ndi moto chija chanthenda.

58 Ndipo ukatsuka chovalacho, kapena muyaro, kapena mtsendero, kapena chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa, ngati nthenda yalekapo pa chimenecho, achitsukenso kawiri, pamenepo chili choyera.

59 Ichi ndi chilamulo cha nthenda yakhate ili pa chovala chaubweya kapena chathonje, ngakhale pamuyaro, kapena pamtsendero, kapena pa chinthu chilichonse chopangika ndi chikopa; kuchitcha choyera kapena kuchitcha chodetsa.

—https://api-cdn.youversionapi.com/audio-bible-youversionapi/355/32k/LEV/13-2b30359154b7c3a72df02d2519f25819.mp3?version_id=1068—

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *